M’pofunika Kumapitako Mwachangu
Kungoyambira nthawi imene webusaiti yathu yatsopano inakhazikitsidwa, anthu ambiri akhala akupempha kuti munthu aziwaphunzitsa Baibulo. Komanso njira yatsopano yolalikirira m’malo opezeka anthu ambiri yapangitsa kuti chiwerengero cha anthu ofuna kuphunzira Baibulo chiwonjezeke. Munthu akapempha pa webusaiti yathu ya jw.org/ny kuti akufuna kuphunzira Baibulo, nthawi yomweyo ofesi ya nthambi imayesetsa kukonza zoti papezeke munthu woti azimuphunzitsa. Pakangodutsa masiku awiri kuchokera pamene munthu wapempha izi, ofesi ya nthambi imadziwitsa akulu a m’dera limene munthuyo akukhala. Komabe zikuoneka kuti pamatenga nthawi yaitali anthu ena amene anapempha kuti akufuna kuphunzira Baibulo asanayenderedwe. Ndiye kodi tingatani kuti tizipita mwamsanga kwa anthu oterewa?—Maliko 4:14, 15.
Mukakumana ndi munthu wachidwi, yemwe sakhala m’gawo lanu, nthawi yomweyo muzilemba fomu ya Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43) n’kuipereka kwa mlembi wa mpingo wanu pasanathe mlungu umodzi. Mlembi ayenera kutumiza fomuyi ku mpingo woyenera kapena ku ofesi ya nthambi pasanathe masiku awiri ndipo angapite pamene palembedwa kuti, “Mpingo” pa webusaiti yathu. Akulu ayenera kumaona zimene zili pa webusaitiyi pafupipafupi. Ngati alandira uthenga woti m’gawo lawo muli munthu wachidwi, ayenera kuonetsetsa kuti munthuyo wayenderedwa pasanapite nthawi yaitali. Wofalitsa aliyense akapemphedwa kuti apite kwa munthu wotereyu, azipitako mwamsanga. Ngati simunam’pezeko munthuyo, mungasiye uthenga wachidule n’kulembapo dzina ndi nambala ya foni yanu.