Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndani ayenera kulemba m’kabokosi ka pa magazini ndiponso pa Intaneti koitanitsira buku kapena kupempha munthu wophunzira naye?
Nthawi zambiri mabuku athu amakhala ndi kabokosi kamene munthu angalembepo n’kukatumiza ku ofesi ya nthambi kuti aitanitse mabuku kapena kupempha kuti amutumizire wa Mboni za Yehova woti ayambe kuphunzira naye Baibulo. Kuwonjezera pamenepa, anthu angagwiritsenso ntchito adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org kuti apemphe munthu woti aziphunzira naye Baibulo. Njira zimenezi zikuthandiza anthu ambiri kuphunzira choonadi. Komabe, pamakhala mavuto ena ngati ofalitsa agwiritsa ntchito njira zimenezi pofuna kuti achibale kapena anthu ena alandire mabuku kapena wa Mboni za Yehova akayambe kuphunzira nawo Baibulo.
Anthu ena akhala akudandaula chifukwa cholandira mabuku kuchokera ku ofesi ya nthambi amene iwowo sanapemphe kuti azilandira. Zimenezi zawachititsa kuona ngati kuti gulu lathu limawavutitsa ndipo linawaika pa gulu la anthu amene limawatumizira mabuku. Ofalitsa amene anapemphedwa kuti akaonane ndi munthu wina amene sanapemphe yekha kuti Amboni akamuchezere amachita manyazi kwambiri mwininyumbayo akawakalipira. Choncho, amene ayenera kulemba m’kabokosi ka pa magazini ndiponso pa Intaneti koitanitsira buku kapena kupempha munthu wophunzira naye, azikhala munthu wachidwiyo osati ofalitsa amene akufuna kuthandiza anzawo kapena achibale awo. A ku ofesi ya nthambi akazindikira kuti wofalitsa watumiza pempholi m’malo mwa munthu wina, sadzatumiza mabuku kapena munthu wokathandiza munthuyo.
Ndiyeno tingatani kuti tithandize wachibale kapena mnzathu mwauzimu? Ngati mukufuna kuti alandire mabuku athu, mungachite bwino kumutumizira inuyo mabukuwo monga mphatso. Ngati wasonyeza chidwi ndipo akufuna kuchezeredwa ndi Mboni koma simukudziwa zimene mungachite kuti mulankhulane ndi akulu a ku mpingo wa kumene akukhala, muzilemba fomu ya Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43) n’kuipereka kwa mlembi wa mpingo wanu. Mlembiyo ndi amene adzaonanso fomuyi mosamala kenako n’kuitumiza ku ofesi ya nthambi. Koma ngati munthu amene wasonyeza chidwiyo ali kundende, malo amene amathandizirako anthu omwa mankhwala osokoneza bongo kapena chipatala cha boma, musalembere a ku ofesi ya nthambi m’malo mwa munthuyo. Anthu otere muziwalimbikitsa kukumana ndi abale amene amafika kumalowa kapena azilembera okha ku ofesi ya nthambi.