Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/15 tsamba 2
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • M’pofunika Kumapitako Mwachangu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Intaneti Mwanzeru
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
km 7/15 tsamba 2

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi ofalitsa ayenera kulalikira kapena kuphunzira Baibulo ndi munthu wosamudziwa wa m’dziko lina pogwiritsa ntchito Intaneti?

Ofalitsa ena amagwiritsa ntchito Intaneti kupeza maphunziro m’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa kapena m’mayiko omwe muli ofalitsa ochepa. Nthawi zina zimenezi zimakhala ndi zotsatira zabwino. Komabe pangakhale mavuto ngati ofalitsa atamacheza ndi anthu osawadziwa pa Intaneti kapena kulemberana nawo maimelo. (Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa July 2007, tsa. 5.) Ngakhale kuti ofalitsa angachite zimenezi pofuna kuuza anthu uthenga wa Ufumu, izi zingachititse kuti ayambe kucheza ndi anthu olakwika komanso ampatuko. (1 Akor. 1:19-25; Akol. 2:8) Komanso m’mayiko amene ntchito yolalikira Ufumu ndi yoletsedwa, akuluakulu a boma angathe kumaona zomwe mukulemberana kudzera pa Intaneti ndipo zingabweretse mavuto kwa abale ndi alongo a m’dzikolo. Choncho ofalitsa sayenera kupita pa Intaneti n’cholinga chofufuza anthu a m’mayiko ena kuti aziwalalikira uthenga wabwino.

Tikalalikira mwamwayi munthu wa m’dziko lina amene wabwera m’dziko lathu, sitiyenera kupitiriza kukambirana naye pa Intaneti akabwerera kwawo, pokhapokha ngati talandira malangizo kuchokera ku ofesi ya nthambi oti tipitirize kukambirana naye. M’malomwake tiyenera kumusonyeza mmene angagwiritsire ntchito webusaiti yathu ya jw.org kuti adziwe zambiri. Kapenanso tingamuuze zimene angachite kuti alumikizane ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lawolo. Tingamulimbikitsenso kuti akapite ku Nyumba ya Ufumu yakufupi ndi komwe amakhala. Ngati munthuyo amakhala m’dziko lomwe mulibe Nyumba za Ufumu, ndipo akufuna kuti a Mboni a m’dera lawo adzapite kukamuchezera, tingalembe fomu yakuti, Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43) n’kuipereka kwa mlembi wa mpingo wathu. Iye adzatumiza fomuyo m’dziko limene munthuyo amakhala kudzera pa webusaiti ya jw.org kapena adzaitumiza ku ofesi ya nthambi ngati kalata kapena kudzera pa imelo. Ofesi ya nthambi yomwe imayang’anira ntchito yathu m’dziko limene munthuyo akukhala, ndi yomwe ingadziwe bwino mmene zinthu zilili m’dzikolo. Choncho ndi yomwe ingathe kudziwa mmene ingamuthandizire.—Onani Utumiki wa Ufumu wa June 2014, tsa. 7 ndi wa November 2011, tsa. 2.

Ngati munthu amene mumamulalikira wasamukira m’dziko lina kapena ngati mukuphunzira ndi munthu wosamudziwa wa m’dziko lina kudzera pa Intaneti, tikukulimbikitsani kuti mutsatire malangizo omwe ali m’nkhaniyi. Komabe mungapitirize kuthandiza munthuyo mpaka patapezeka wofalitsa wa kudera lawo, woti azimuthandiza. Koma ngati munthuyo amakhala m’dziko lomwe ntchito yolalikira ndi yoletsedwa, muyenera kuchita zinthu mosamala mukamakambirana naye mfundo za m’Baibulo kudzera m’makalata, pa foni kapena pa Intaneti.—Mat. 10:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena