Mmene Mungagwiritsire Ntchito Fomu Yakuti Kaonaneni Ndi Wachidwi Uyu (S-43)
Muzilemba fomu imeneyi mukapeza munthu wachidwi amene sakhala m’gawo lanu kapena amene amalankhula chinenero china. M’mbuyomu tinkagwiritsa ntchito fomuyi tikakumana ndi munthu wolankhula chinenero china ngakhale amene sanachite chidwi ndi uthenga wathu. Koma tsopano tizilemba fomuyi munthuyo akachita chidwi basi. Komabe, tingalembe fomu ya S-43 tikakumana ndi munthu wogontha kaya wasonyeza chidwi kapena ayi.
Kodi fomuyi tizipita nayo kuti tikalembapo zonse zofunikira? Tiziipereka kwa mlembi wa mpingo wathu. Ngati mlembiyo akudziwa mpingo wakufupi ndi kumene munthuyo akukhala, angatumize fomuyo kwa akulu a mpingowo kuti akamuthandize. Koma ngati sakudziwa bwinobwino mpingo umene ungamuthandize, azitumiza fomuyo ku ofesi ya nthambi.
Ngati munthu wolankhula chinenero china amene wachita chidwi ndi uthenga wathuyo akukhala m’gawo lanu, muzimuyenderabe kuti mukulitse chidwi chake mpaka patapezeka wofalitsa wa mpingo wa chinenero chake amene angamuthandize.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2009, tsamba 4.