Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Dec. 1
“Kodi inu simukuvomereza kuti anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pankhani ya ukhondo? [Yembekezani ayankhe.] Taonani chifukwa chimene ukhondo uli wofunika kwambiri. [Werengani 1 Petulo 1:16.] Nkhani iyi ikufotokoza njira zimene zingatithandize kukhala anthu aukhondo.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 9.
Galamukani Dec.
“Anthu ambiri amayesetsa kulemekeza Yesu m’nyengo ino. Komano mogwirizana ndi lemba ili, munganene kuti njira yoyenera yolemekezera Yesu ndi iti? [Werengani Yohane 14:15. Yembekezani ayankhe.] Tsiku lenileni limene Yesu anabadwa silidziwika ndipo mungadabwe kumva chifukwa chimene anthu anasankhira deti la December 25 kuti likhale tsiku la Khirisimasi.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 10.
Nsanja ya Olonda Jan. 1
“Anthu pa dziko lonse amanena zinthu zosiyanasiyana zokhudza mayi wa Yesu, Mariya. Kodi inuyo mukudziwa zotani? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limasonyeza kuti Mariya anali ndi udindo wapadera kwambiri. [Werengani Luka 1:30-32.] Magazini iyi ikufotokoza zimene tingaphunzire kuchokera pa chitsanzo chake.”
Galamukani Jan.
“Nyanja ndi mitsinje yambiri ya padziko lonse ikuuma ndipo anthu ambiri akusowa madzi abwino akumwa. Kodi mukuganiza kuti anthu angathetse vuto limeneli? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Yeremiya 10:23.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena posonyeza kuti vutoli lidzatheratu.”