Ndife Mboni za Yehova Nthawi Zonse
1. Kodi nkhani yonena zimene Yesu anachita zolalikira mkazi wina pachitsime ikutiphunzitsa chiyani?
1 Yesu anali atayenda kwa maola ambiri. Anatopa kwambiri ndipo anali ndi ludzu. Ophunzira ake atapita kukagula chakudya, iye anakhala pachitsime china cha kunja kwa mzinda wina wa ku Samariya kuti apume. Iye sanali ku Samariyako n’cholinga choti alalikireko ayi, koma ankangodutsa. Ankapita ku Galileya kukapitiriza utumiki wake kumeneko. Ngakhale zinali choncho, iye anapezerapo mwayi wolalikira mkazi wina wachisamariya amene ankatunga madzi. (Yoh. 4:5-14) N’chifukwa chiyani Yesu anachita zimenezi? Chifukwa chakuti iye sanasiye kukhala “mboni yokhulupirika ndi yoona” ya Yehova. (Chiv. 3:14) Ifeyo timatsanzira Yesu pokhala Mboni za Yehova nthawi zonse.—1 Pet. 2:21.
2. Kodi tingachite chiyani kuti tizikhala okonzekeratu kulalikira mwamwayi?
2 Muzikhala Okonzekeratu: Tingakhale okonzekeratu kulalikira mwamwayi tikamanyamula mabuku athu poyenda. Ofalitsa ambiri akamayenda, tsiku lililonse amayenda ndi timapepala ndipo amagawira timapepalati kwa ogwira ntchito m’sitolo, malo ogulitsira mafuta a galimoto ndiponso kwa anthu ena amene amakumana nawo. (Mlal. 11:6) Mlongo wina amene amayenda pa basi kawirikawiri, nthawi zonse akamayenda amaonetsetsa kuti m’kachikwama kake watenga Baibulo laling’ono ndiponso buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndipo amayesetsa kuyamba kukambirana ndi anthu amene akhala pafupi naye.
3. Kodi tingatani kuti tiyambe kukambirana ndi anthu?
3 Mmene Mungayambire Kukambirana: Polalikira mwamwayi, ndi bwino kuti tisamangoyambiratu ndi nkhani ya m’Malemba. Yesu sanayambe kukambirana ndi mkazi uja pachitsime pomudziwitsa kuti iyeyo ndiye Mesiya. Iye anangoyamba ndi kumupempha madzi kuti amwe, zimene zinachititsa mkaziyo kudabwa. (Yoh. 4:7-9) Mlongo wina anaona kuti kuyamba kukambirana mwa njira yotere kumam’thandiza, anthu akamufunsa kuti afotokoze mmene anasangalalira pa tchuti chinachake, monga cha Khirisimasi kapena Chaka Chatsopano. M’malo mowayankha kuti sanasangalalire nawo tchuticho chifukwa chakuti ndi wa Mboni za Yehova, iye amawauza kuti, “Ndinasankha kuti ndisamasangalalire nawo tchuti chimenechi.” Kawirikawiri wofunsayo podabwa nazo amafunsa chifukwa chake iye anasankha choncho, ndipo zikatero mlongoyo amapezerapo mwayi wolalikira munthu wofunsayo.
4. N’chifukwa chiyani lemba la Mateyo 28:18-20 limakulimbikitsani?
4 Ngakhale kuti Yesu anamaliza utumiki wake umene ankachita mwachangu padziko lapansili, iye akupitirizabe kuchita chidwi ndi ntchito yolalikira imene ikuchitika mofanana ndi mmene iye ankaichitira. (Mat. 28:18-20) Choncho, mofanana ndi Yesu amene tikutengera chitsanzo chake, ndife mboni zokonzeka kulengeza poyera chikhulupiriro chathu nthawi ina iliyonse.—Aheb. 10:23.