Muzisonyeza Ena ‘Chifundo Chachikulu’
1. Kodi anthu akufunikira kwambiri chiyani masiku ano?
1 Anthu ambiri masiku ano akufunika kuwachitira chifundo kwambiri kuposa kale lonse. Mavuto amene anthu akukumana nawo m’dzikoli akuchititsa anthu kulikonse kukhala osasangalala, ovutika maganizo ndiponso opanda chiyembekezo. Anthu mamiliyoni ambiri akufunika thandizo ndipo Akhristufe ndi amene tingawathandize powasonyeza kuti timawaderadi nkhawa. (Mat. 22:39; Agal. 6:10) Kodi tingachite chiyani posonyeza kuti timawaderadi nkhawa?
2. Tchulani njira yabwino kwambiri imene tingasonyezere chifundo.
2 Ntchito Yachifundo: Mulungu ndi amene amapereka chitonthozo chenicheni. (2 Akor. 1:3, 4) Yehova akutilimbikitsa kuti tizisonyeza ena “chifundo chachikulu” ndipo watipatsa ntchito youza anthu uthenga wabwino wa Ufumu. (1 Pet. 3:8) Kugwira nawo ntchito imeneyi mwakhama ndi njira yabwino yolimbikitsira “osweka mtima,” chifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wokhawo umene udzathetse kuvutika kwa anthu. (Yes. 61:1) Posachedwapa Yehova, chifukwa chomvera chifundo anthu ake, achitapo kanthu kuti achotse zoipa zonse n’kukhazikitsa dziko latsopano lolungama.—2 Pet. 3:13.
3. Kodi tingatsanzire bwanji mmene Yesu ankaonera anthu?
3 Muziona Anthu Mmene Yesu Ankawaonera: Ngakhale polalikira gulu lalikulu la anthu, Yesu ankachita chidwi ndi munthu aliyense payekha. Iye ankaona kuti munthu aliyense ndi wofunika kumuthandiza mwauzimu. Anthuwo anali ngati nkhosa zopanda m’busa wozitsogolera. Choncho mtima wa Yesu unakhudzika ndi zimene anaona, ndipo anayamba kuwaphunzitsa modekha. (Maliko 6:34) Ngati ifenso tingamaone anthu mmene Yesu ankawaonera, tidzalimbikitsidwa kuchitira chifundo chenicheni munthu aliyense. Tidzasonyeza zimenezi ndi mmene nkhope zathu zikuonekera ndiponso mmene tikuwalankhulira. Ntchito yolalikira idzakhala patsogolo pa moyo wathu, ndipo tidzalankhula zinthu zosonyeza kuti timadera nkhawa munthu aliyense.—1 Akor. 9:19-23.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuvala chifundo?
4 Anthu ambiri ochokera m’mitundu yonse akumvetsera uthenga wa Ufumu ndiponso akusangalala ndi chikondi chimene akusonyezedwa. Tikapitiriza kuvala khalidwe la chifundo, tidzalemekeza ndi kusangalatsa Yehova, Mulungu wathu wachifundo.—Akol. 3:12.