‘Chifuniro cha Mulungu Chichitike’
1. Kodi mutu wa msonkhano wa tsiku la msonkhano wapadera wa chaka chautumiki cha 2012 ndi woti chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa zambiri zokhudza mutu umenewu?
1 Yehova anatilenga mwa chifuniro chake. (Chiv. 4:11) Choncho anthufe sitingathe kukwaniritsa cholinga chimene anatilengera popanda kuphunzira komanso kuchita chifuniro cha Mulungu. Koma kuchita chifuniro cha Mulungu n’kovuta ngakhale kuti zimaoneka ngati zosavuta. Zimenezi zili choncho chifukwa nthawi zonse timalimbana ndi mtima wathu wofuna “kuchita zofuna za thupi ndi maganizo,” kapena “kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli.” (Aef. 2:3; 1 Pet. 4:3; 2 Pet. 2:10) Mulungu atapanda kutithandiza, ‘Mdyerekezi angatigwire amoyo pofuna kuti tikwaniritse cholinga chake.’ (2 Tim. 2:26) Pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera ya chaka chautumiki cha 2012 idzatithandiza kuti tiziyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi pempho lachitatu mu pemphero lachitsanzo. Pempho limeneli ndi lakuti, “chifuniro chanu chichitike.”—Mat. 6:9, 10.
2. Kodi pa tsiku lamsonkhano wapadera tidzapeza mayankho a mafunso ati?
2 Mafunso Amene Adzayankhidwe: Mukamadzamvetsera msonkhanowu, dzayesetseni kupeza mayankho amafunso awa: Kodi n’chiyani chimene chili chofunika kwambiri ngati kumva mawu a Mulungu? Kodi tingadziwe bwanji chifuniro cha Mulungu chokhudza anthufe? N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ofunitsitsa kuthandiza anthu onse? Kodi tingatani kuti tizikhala ndi moyo wosangalala komanso waphindu? Achinyamatanu, kodi mufunika kumusonyeza chiyani Yehova? Kodi tidzapeza madalitso otani tikamachita chifuniro cha Mulungu? N’chifukwa chiyani kulimbikitsa ena kuli kofunika kwambiri panopo?
3. Kodi tingadzapindule bwanji ndi msonkhano wapadera?
3 Yesetsani kuti mudzapezeke pamsokhanowu ndipo mudzamvetsere mwachidwi nkhani zonse zimene zidzakambidwe. M’bale woimira Beteli kapena woyang’anira woyendayenda adzakhala pamsonkhanowu monga mlendo. Msonkhano usanayambe kapena utatha, dzakhaleni omasuka kucheza ndi m’baleyu ndiponso mkazi wake ngati ndi wokwatira. Mukadzabwerera kunyumba, musadzakhale munthu wongomva zinthu n’kuiwala. M’malomwake, dzayesetseni kukambirananso monga banja nkhani zonse za msonkhanowu ndipo dzakambiraneni zimene mungachite kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.—Yak. 1:25.
4. N’chifukwa chiyani kuchita chifuniro cha Mulungu kuyenera kukhala kofunika kwambiri pa moyo wathu?
4 Posachedwapa anthu onse amene akuchita zinthu zongodzisangalatsa okha komanso amene akukana kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova awonongedwa. (1 Yoh. 2:17) Ifeyo tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chotikonzera malangizo a pa nthawi yake amenewa. Malangizowa adzatithandiza kuti tiziona kuti kuchita chifuniro cha Mulungu n’kofunika kwambiri pa moyo wathu.