Mawu a Mulungu Ndi Opindulitsa pa Kuphunzitsa
1. Kodi mutu wa msonkhano wadera wa 2014 udzakhala wotani, nanga ndi funso liti limene lidzayankhidwe pa msonkhanowo?
1 ‘Mlangizi wathu Wamkulu’ Yehova ndi mphunzitsi wabwino kwambiri kuposa aphunzitsi onse. (Yes. 30:20, 21) Koma kodi Yehova amatilangiza bwanji? Watipatsa Mawu ake, Baibulo, lomwe ndi buku lapadera kwambiri kuposa mabuku onse. Kodi maphunziro ochokera kwa Mulungu angatithandize bwanji pa moyo wathu? Yankho la funso limeneli lidzafotokozedwa pa msonkhano wadera wa chaka chautumiki cha 2014. Mutu wa msonkhanowu ndi wakuti “Mawu a Mulungu Ndi Opindulitsa pa Kuphunzitsa” ndipo wachokera pa lemba la 2 Timoteyo 3:16.
2. Kodi ndi mafunso ati amene adzasonyeze mfundo zikuluzikulu za msonkhanowo?
2 Mudzayesetse Kupeza Mfundo Izi: Mfundo zikuluzikulu za msonkhanowo zidzakhala mayankho a mafunso otsatirawa:
• Kodi tingapindule bwanji pa moyo wathu chifukwa chophunzitsidwa ndi Mulungu? (Yes. 48:17, 18)
• Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani ngati tikufuna kusintha zinthu zina pa moyo wathu n’cholinga choti tiyambe utumiki wanthawi zonse? (Mal. 3:10)
• Kodi tiyenera kutani ngati ena akuphunzitsa ‘ziphunzitso zachilendo’? (Aheb. 13:9)
• Kodi tingatsanzire bwanji “kaphunzitsidwe” ka Yesu? (Mat. 7:28, 29)
• N’chifukwa chiyani anthu amene amaphunzitsa mu mpingo ayeneranso kumadziphunzitsa okha? (Aroma 2:21)
• Kodi Mawu a Mulungu ndi opindulitsa pa zinthu ngati ziti? (2 Tim. 3:16)
• Kodi anthu akuchita chiyani chifukwa chakuti Mulungu ‘akugwedeza’ mitundu yonse ya anthu? (Hag. 2:6, 7)
• Kodi Yehova amadziwa zoti tingakwanitse kuchita chiyani? (Aef. 5:1)
• N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizitsatirabe zimene Yehova amatiphunzitsa? (Luka 13:24)
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kudzapezeka pamsonkhano wadera?
3 Kumayambiriro kwa 2 Timoteyo chaputala 3, Paulo asanafotokoze mawu omwe ndi mutu wa msonkhanowu, anafotokoza mavuto omwe adzachitike m’masiku otsiriza. Iye ananena kuti: “Anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.” (2 Tim. 3:13) Kuti tisasocheretsedwe tikufunika kumamvetsera ndiponso kutsatira zimene Mulungu akutiphunzitsa. Choncho, tiyeni tiyesetse kuti tidzapezeke pamsonkhanowu ndipo tizidzamvetsera mfundo za pa nthawi yake zimenezi.