Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/11 tsamba 1
  • Tizikhala Okonzeka Kulalikira Nthawi Zonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizikhala Okonzeka Kulalikira Nthawi Zonse
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • ‘Chitani Ntchito ya Mlaliki wa Uthenga Wabwino’
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Phunzitsani Poyera ndi Kunyumba ndi Nyumba
    Nsanja ya Olonda—1991
  • N’chifukwa Chiyani Utumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba Uli Wofunika Kwambiri Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
km 12/11 tsamba 1

Tizikhala Okonzeka Kulalikira Nthawi Zonse

1. Tikudziwa bwanji kuti Akhristu oyambirira ankakhala okonzeka kulalikira nthawi zonse?

1 Akhristu oyambirira analalikira uthenga wabwino “mwakhama” kwambiri kulikonse kumene anapezako anthu. (Mac. 5:42) Izi zikusonyezeratu kuti polalikira kunyumba ndi nyumba, sakanalolera kungodutsana ndi anthu panjira osawauza uthenga wabwino. Komanso atamaliza kulalikira, sakanalekerera mpata wolalikira mwamwayi pogula zinthu pamsika. Mofanana ndi Yesu, Akhristu oyambirira anali okonzeka kulalikira nthawi zonse.—Maliko 6:31-34.

2. Kodi kukhala Mboni za Yehova kumafuna chiyani?

2 Tizikhala Okonzeka Nthawi Zonse: Dzina lathu lakuti Mboni za Yehova limanena zimene timachita komanso kuti ndife ndani. (Yes. 43:10-12) Choncho, tiyenera kukhala okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene watifunsa za chiyembekezo chathu, ngakhale pamene sitikulalikira kunyumba ndi nyumba. (1 Pet. 3:15) Kodi mumakonzekera zimene munganene pa zochitika zosiyanasiyana ngati patapezeka mpaka wolalikira mwamwayi? Kodi mumayenda ndi mabuku athu kuti muzipatsa anthu amene achita chidwi ndi uthenga wathu? (Miy. 21:5) Kodi mumangolalikira kunyumba ndi nyumba basi kapena mumafalitsanso uthenga wabwino kwa anthu kumalo ena, kukakhala kotheka?

3. N’chifukwa chiyani kuli koyenera kutchula ntchito yolalikira mumsewu, m’malo oimikako magalimoto, malo ochezerako, malo azamalonda ndi malo ena otero kuti kulalikira ‘poyera’ kapena kuti m’malo opezeka anthu ambiri?

3 Kulalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri: Kodi ntchito yolalikira mumsewu, m’malo oimikako magalimoto, malo ochezerako, malo azamalonda ndi ena otero tiziitchula kuti chiyani? Mtumwi Paulo ananena kuti ankalalikira “poyera” ndiponso kunyumba ndi nyumba. (Mac. 20:20) Choncho mawu akuti kulalikira “poyera” kapena kuti m’malo opezeka anthu ambiri, ndi dzina loyenera lotchulira ulaliki wamtundu umenewu. N’zoona kuti kulalikira kunyumba ndi nyumba ndi njira yaikulu ndiponso yabwino kwambiri youzira anthu uthenga wa Ufumu. Komatu Akhristu oyambirira sankaganizira kwambiri za nyumba polalikira, koma za anthu. Sankalekerera mwayi uliwonse wolankhula za choonadi kwa anthu m’malo opezeka anthu ambiri, mwamwayi ndiponso kunyumba ndi nyumba. Ifenso tili ndi mwayi waukulu wolalikira mumsewu, m’malo oimikako magalimoto, m’malo ochezerako, m’malo azamalonda ndi m’malo ena otero. Tiyeni tikhale ndi maganizo ofanana ndi a Akhristu oyambirira kuti tikwaniritse mbali zonse za utumiki wathu.—2 Tim. 4:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena