“Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya”
1. Kodi ndi buku liti lomwe linatulutsidwa pa Msonkhano Wachigawo wa 2010, nanga tidzaligwiritsa ntchito bwanji?
1 Tinasangalala kwambiri pamene buku latsopano la mutu umenewu linatulutsidwa pa Msonkhano Wachigawo wa 2010, womwe unali ndi mutu wakuti “Khalanibe Paubwenzi ndi Yehova.” M’bukuli muli mfundo zomwe zingatithandize pa moyo wathu zopezeka m’mabuku a Yeremiya ndi Maliro. (Aroma 15:4) Bukuli linakonzedwa kuti lidzaphunziridwe pa Phunziro la Baibulo la Mpingo ndipo tiyamba kuliphunzira mlungu woyambira September 16, 2013.
2. Kodi kuphunzira buku la Yeremiya ndi la Maliro kungatithandize bwanji?
2 Ndi Lothandiza Masiku Ano: Yeremiya anali mneneri pa nthawi imene ku Yuda kunali mavuto ambiri. Poyamba ankaona ngati sangakwanitse kugwira ntchitoyi. (Yer. 1:6) Iye ankazunzidwanso ndi anzake komanso achibale ake a mumzinda wa kwawo ku Anatoti. (Yer. 11:21, 22) Mpake kuti nthawi zina Yeremiya ankakhala wokhumudwa. (Yer. 20:14) Pamene tikugwira ntchito imene tinapatsidwa ‘yophunzitsa anthu a mitundu yonse,’ nthawi zambiri timakumana ndi mavuto komanso timamva ngati mmene Yeremiya ankamvera. (Mat. 28:19) Kuphunzira zimene analemba kutithandiza kuchita utumiki wathu molimba mtima komanso mwakhama.
3. Kodi zinthu zosiyanasiyana za m’buku la Yeremiya tidzazigwiritsa ntchito bwanji?
3 Zimene Zili M’bukuli: Malemba amene ali ndi mfundo zikuluzikulu omwe ndi ofunika kuwawerenga pa phunzirolo alembedwa ndi mawu okuda kwambiri. Kumapeto kwa ndime zophunzira mlungu uliwonse kuli funso limodzi kapena awiri omwe akusonyeza mfundo zazikulu ndipo alembedwa ndi mawu okuda kwambiri. Wochititsa phunziro azidzafunsa mafunso amenewa pobwereza zimene taphunzira. M’bukuli mulinso zithunzi zambiri zomwe omvera angakonde kuzifotokoza.
4. Kodi tingatani kuti tidzapindule kwambiri tikamadzaphunzira buku la Yeremiya?
4 Kuti mudzapindule kwambiri ndi phunziroli, muzidzakonzekera pasadakhale. Muzidzaganizira mfundo zomwe mungagwiritse ntchito pa moyo wanu komanso mu utumiki ndipo muzidzapereka ndemanga momasuka. Yehova anathandiza Yeremiya kuti akwanitse ntchito imene anam’patsa mwachimwemwe komanso kuti akhale wokhutira ndi zimene anachita. (Yer. 15:16) Tikukhulupirira kuti kuphunzira buku latsopanoli kutithandiza kuchita utumiki wathu ngati mmene Yeremiya anachitira.