Musafulumire Kuganiza Kuti Simungakwanitse—Zimene Mungachite Ngati Mumachita Mantha
1. N’chifukwa chiyani anthu ena amalephera kupempha mwininyumba kuti aziphunzira naye Baibulo?
1 Kodi mumalephera kupempha mwininyumba kuti muziphunzira naye Baibulo chifukwa chochita mantha kuti simungakwanitse kuchititsa phunziro? Atumiki ena okhulupirika akale monga Mose ndi Yeremiya nawonso ankadziona kuti sangakwanitse kuchita utumiki umene anapatsidwa. (Eks. 3:10, 11; 4:10; Yer. 1:4-6) Choncho musaganize kuti ndinu nokha amene mumachita mantha. Komano kodi mungatani kuti muthetse mantha amenewa?
2. N’chifukwa chiyani sitiyenera kumangokhutira ndi ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba, n’kumasiyira ntchito yopangitsa maphunziro a Baibulo anthu ena?
2 Tizikumbukira kuti Yehova satipempha kuchita zinthu zimene sitingakwanitse. (Sal. 103:14) Chotero, ntchito yathu ‘yothandiza anthu kuti akhale ophunzira’ ndiponso ‘kuwaphunzitsa’ ndi yoti tikhoza kukwanitsa. (Mat. 28:19, 20) Sikuti Yehova anapereka ntchitoyi kwa anthu okhawo amene amaidziwa bwino komanso aluso kwambiri ayi. (1 Akor. 1:26, 27) Ndiye tisamangokhutira ndi ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba n’kumasiyira ntchito yopangitsa maphunziro a Baibulo anthu ena.
3. Kodi Yehova wachita zotani kuti atithandize kukhala oyenera kugwira ntchito yophunzitsa anthu Baibulo?
3 Yehova Ndi Amene Amatipangitsa Kukhala Oyenera: Timakwanitsa kugwira ntchito yophunzitsa anthu chifukwa cha thandizo la Yehova. (2 Akor. 3:5) Pogwiritsira ntchito gulu lake, Yehova watiphunzitsa choonadi cha m’Baibulo chimene ngakhale anthu ophunzira kwambiri m’dzikoli sachidziwa. (1 Akor. 2:7, 8) Iye analemba m’Baibulo njira zimene Mphunzitsi Waluso Yesu, ankagwiritsira ntchito pophunzitsa ndi cholinga choti ifeyo titsanzire. Komanso nthawi zonse amatiphunzitsa mmene tingagwirire ntchitoyi kudzera m’misonkhano ya mpingo. Kuwonjezera pamenepa, Yehova sanangotisiya kuti tizisankha tokha mabuku ophunzitsira anthu Baibulo. Iye watipatsa mabuku monga buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, lomwe limaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo mwandondomeko komanso mosavuta kumva. Chotero kuchititsa phunziro la Baibulo ndi kophweka kuposa mmene tingaganizire.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza pa ntchito yophunzitsa anthu Baibulo?
4 Mose ndi Yeremiya anakwanitsa kugwira ntchito imene anapatsidwa chifukwa chothandizidwa ndi Yehova. (Eks. 4:11, 12; Yer. 1:7, 8) Ifenso tingapemphe Yehova kuti atithandize. Ndipotu tikamachititsa phunziro la Baibulo, timakhala tikuphunzitsa munthuyo zoona zenizeni zokhudza Yehova. Ntchito imeneyi Mulungu amasangalala nayo. (1 Yoh. 3:22) Choncho yesetsani kukhala ndi cholinga choti muzigwira nawo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Imeneyi ndi mbali yosangalatsa komanso yopindulitsa ya utumiki wathu.