Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa September
“Ulendo wathu ndi wachidule ndipo tikukambirana ndi anthu mmene angakhalire ndi banja losangalala. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimapangitsa kuti mabanja ambiri asamasangalale?” [Yembekezani ayankhe.] Musonyezeni nkhani imene ili patsamba 15 mu Nsanja ya Olonda ya September 1, ndipo kambiranani funso loyambirira komanso lemba limodzi limene likupezeka pa ndime zimenezi. Mugawireni magaziniyo ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda September 1
“Anthu ambiri amadabwa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti tizikumana ndi mavuto ambiri. Kodi inuyo munayamba mwaganizirapo za funso limeneli? [Yembekezani ayankhe.] N’zosangalatsa kuti Baibulo linalonjeza kuti nthawi ina mavuto onsewa adzatha. [Werengani Chivumbulutso 21:4.] Magaziniyi ikufotokoza zinthu 5 zimene zikuchititsa kuti anthu azikumana ndi mavuto ambiri chonchi. Ikufotokozanso zimene Baibulo limanena za mmene Mulungu adzathetsere mavutowa.”
Galamukani! September
“Anthu ena amakhala ndi maganizo oti palibe vuto ngati anthu amene sanakwatirane atamagonana. Kodi inuyo maganizo anu ndi otani? Kodi mumaona kuti ndi zoyenera kuti anthu amene sanakwatirane azigonana? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena. [Werengani 1 Akorinto 6:18] Magazini iyi ikufotokoza mmene Mulungu amaonera nkhani imeneyi.” Muonetseni mwininyumbayo nkhani yomwe yayambira patsamba 4.