Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/14 tsamba 2
  • Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Nahumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Nahumu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Mfundo Zazikulu za M’mabuku a Nahumu, Habakuku, ndi Zefaniya
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Chipulumutso Nchothekera Pamene Mulungu Abwezera Chilango
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Zimene Zili M‘buku la Nahumu
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Kodi Mukudziwa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
km 9/14 tsamba 2

Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Nahumu

1. Kodi buku la m’Baibulo la Nahumu lingatithandize bwanji?

1 Mabwinja a mzinda wakale wa Nineve ndi umboni wakuti zimene Nahumu analosera zinachitikadi. Yehova anabwezera adani ake ndipo ngakhale amene ankaoneka ngati oopsa sanapulumuke. (Nah. 1:2, 6) Kuphunzira bwinobwino ulosi wa Nahumu kungatithandize kudziwa zimene tiyenera kuchita tikakhala mu utumiki.

2. Kodi tingatani kuti anthu aziona kuti uthenga wathu ndi wolimbikitsa?

2 Muzinena Zolimbikitsa Komanso Zopatsa Chiyembekezo: Kupanda kuliwerenga bwinobwino, buku la Nahumu limaoneka ngati limangonena za uthenga wa chiweruzo choopsa chimene Yehova ananena kuti adzapereka kwa anthu a mumzinda wa Nineve. Mzindawu unali likulu la dziko la Siriya. (Nah. 1:1; 3:7) Komatu uthenga umenewu unali nkhani yabwino kwa anthu a Yehova. Nahumu, yemwe dzina lakeli limatanthauza “Munthu Wolimbikitsa,” anatsimikizira Ayuda kuti sipapita nthawi ndipo adani awo awonongedwa. Anawatsimikiziranso kuti Yehova ndi “malo achitetezo pa tsiku la nsautso.” (Nah. 1:7) Ifenso tikamalalikira timauza anthu uthenga wabwino ndipo timawalimbikitsa kuti azidalira Yehova kuti ndi amene angadzawapulumutse.—Nah. 1:15.

3. Kodi tingatsanzire bwanji Nahumu pa nkhani yogwiritsa ntchito zitsanzo komanso mafanizo?

3 Muzigwiritsa Ntchito Zitsanzo Komanso Mafanizo: Yehova anauzira Nahumu kuti alembe uthenga wokhudza mzinda wa Nineve. Mu uthengawu ananena kuti mzinda wa Nineve udzawonongedwa mofanana ndi mmene Asuri anawonongera mzinda wa Thebes kapena kuti No-amoni. (Nah. 3:8-10) Ifenso tikamauza anthu mmene dziko loipali lidzawonongedwere, tizitchula maulosi a m’Baibulo amene amasonyeza kuti Yehova amakwaniritsa chilichonse chimene wanena. Mwachitsanzo, Ababulo ndi Amedi ataukira mzinda wa Nineve mu 632 B.C.E., mvula yamphamvu inachititsa kuti mtsinje wa Tigirisi usefukire n’kugwetsa mbali ina ya mpanda wolimba wa mzindawu. Pasanapite nthawi mzinda wa Nineve unalandidwa, ngati mmene Yehova analoserera.—Nah. 1:8; 2:6.

4. Kodi tingatani kuti tikakhala mu utumiki tizilankhula zomveka bwino komanso zosavuta kumva?

4 Muzigwiritsa Ntchito Mawu Osavuta Komanso Muzifotokoza Momveka Bwino: Nahumu ankafotokoza nkhani m’njira yoti omvera ake ankakhala ngati akuona zimene zikunenedwazo. Mfundo zake zinkakhala zomveka bwino. (Nah. 1:14; 3:1) Ifenso tiyenera kugwiritsa ntchito mawu osavuta kumva. (1 Akor. 14:9) Pa ulendo woyamba, fotokozani momveka bwino chimene mwabwerera. Mukamaphunzira Baibulo ndi munthu, mufotokozereni momveka bwino kufunika koti azikhulupirira kwambiri Yehova komanso Mawu ake. Fotokozaninso momveka bwino mmene angagwiritsire ntchito zimene akuphunzirazo pa moyo wake.—Aroma 10:14.

5. Kodi zimene Nahumu analosera zimatilimbikitsa bwanji?

5 Buku la m’Baibulo la Nahumu limachita kusonyezeratu kuti Nahumu ankakhulupirira kwambiri zoti malonjezo a Yehova amakwaniritsidwa. Pamene dziko la Satanali latsala pang’ono kuwonongedwa, timalimbikitsidwa ndi mawu amene Mulungu ananena akuti: “Sipadzakhalanso nsautso.”—Nah. 1:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena