Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2015 Itithandiza Kuti Tiziphunzitsa Mwaluso
1 Davide analemba kuti: “Mawu a pakamwa panga ndi kusinkhasinkha kwa mtima wanga, zikukondweretseni, inu Yehova, Thanthwe langa ndi Wondiwombola.” (Sal. 19:14) Nafenso tikufuna kuti mawu athu azisangalatsa Yehova chifukwa timaona kuti ndi mwayi kulankhula mfundo za choonadi pa misonkhano ya mpingo ndiponso mu utumiki. Njira ina imene Yehova amatiphunzitsira kuti tizilalikira mogwira mtima, ndi kudzera m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Sukuluyi imachitika mlungu uliwonse m’mipingo yoposa 111,000 padziko lonse. Yathandiza abale ndi alongo osiyanasiyana kuti aziphunzitsa komanso kuti azilalikira uthenga wabwino mwaluso, mogwira mtima ndiponso mopanda mantha.—Mac. 19:8; Akol. 4:6.
2 M’chaka cha 2015, nkhani zina zizidzachokera m’kabuku kakuti, Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani? Komanso nthawi yokambira nkhani Na. 1 ndi mfundo zazikulu, yasintha. Ndime zotsatirazi zikufotokoza zokhudza kusinthaku komanso malangizo atsopano a mmene abale ndi alongo azikambira nkhani za m’Sukulu.
3 Mfundo Zazikulu: Mfundo zazikulu zizichitika mphindi 8. Wokamba mfundozi azifotokoza kwa mphindi ziwiri mfundo imodzi yolimbikitsa yomwe wapeza m’machaputala a mlunguwo. Kuti akambe zolimbikitsa komanso kuti asadye nthawi, ayenera kukonzekera bwino. Kenako kwa mphindi 6 zotsalazo, omvera azifotokoza mfundo zolimbikitsa zomwe apeza m’machaputala a mlunguwo. Woyankha aliyense asamapitirire masekondi 30. Kukonzekera bwino komanso kuganizira ena kungatithandize kuti tizitha kunena mfundo yolimbikitsa m’masekondi 30 amenewa. Zingathandizenso kuti anthu ena apereke ndemanga zolimbikitsa zomwe apeza. Tikamachita zimenezi timakhala tikuphunziranso kuchita zinthu mwadongosolo.
4 Nkhani Na. 1: Wokamba nkhaniyi aziwerenga Baibulo kwa mphindi zosapitirira zitatu ndipo ayenera kukonzekera bwino. Angachite zimenezi powerenga mavesiwo mokweza. Ayeneranso kuonetsetsa kuti akuwerenga bwino komanso akutchula mawu moyenera n’cholinga choti asasinthe tanthauzo la zimene zalembedwazo. Mtumiki aliyense wa Yehova ayenera kuyesetsa kuti aziwerenga bwino chifukwa kuwerenga n’kofunika kwambiri kuti tizitha kuphunzitsa bwino. N’zosangalatsa kuti ana ambiri amawerenga bwino. Tikuyamikira makolo chifukwa chothandiza ana awo kudziwa kuwerenga.
5 Nkhani Na. 2: Nkhaniyi iziperekedwa kwa alongo ndipo aziikamba ngati chitsanzo kwa mphindi 5. Mlongo yemwe wapatsidwa nkhaniyi ayenera kuikamba mogwirizana ndi mutu womwe wapatsidwa. Ngati nkhaniyo yachokera m’kabuku kakuti, Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani? wokambayo ayenera kuikamba mogwirizana ndi zimene zimachitikadi m’gawo la mpingo wawo. Angawerengenso malemba owonjezera omwe akuona kuti akugwirizana ndi mutu wa nkhaniyo. Woyang’anira sukulu azisankha mlongo wina womuthandiza kukamba nkhaniyo.
6 Nkhani Na. 3: Nkhaniyi izikambidwa ndi m’bale kapena mlongo kwa mphindi 5. Ngati yemwe wapatsidwa nkhaniyi ndi mlongo, ayenera kuikamba potsatira malangizo omwe ali mu nkhani Na. 2. Ngati yaperekedwa kwa m’bale, iyenera kukhala nkhani yokambira mpingo wonse. M’baleyo ayenera kusankha malemba omwe akufuna kukawawerenga komanso kufotokoza zimene tikuphunzira pa nkhaniyo.
7 Njira Yatsopano Yokambira Nkhani Na. 3 Ngati Yaperekedwa kwa M’bale: Ngati nkhaniyi yachokera m’kabuku kakuti, Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani? iyenera kukambidwa ngati chitsanzo cha kulambira kwa pabanja kapena cha mu utumiki. Woyang’anira sukulu azisankha munthu wothandiza m’bale yemwe akukamba nkhaniyi komanso mmene chitsanzocho chikhalire. Wothandizayo akhoza kukhala munthu wa m’banja lake kapena m’bale wina mumpingomo. M’baleyo angawerengenso malemba ena omwe akugwirizana ndi nkhaniyo. Nthawi zina, nkhaniyi iziperekedwa kwa mkulu. Zikatere mkuluyo ndi amene azisankha munthu womuthandiza komanso mmene chitsanzo chake chikhalire. N’zosakayikitsa kuti mpingo udzalimbikitsidwa kwambiri kuona mkulu akusonyeza luso lophunzitsa.
Muzitsatira malangizo omwe mwapatsidwa
8 Kupereka Malangizo: Pambuyo pa nkhani iliyonse, woyang’anira sukulu azigwiritsa ntchito buku lakuti Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu popereka malangizo othandiza komanso kuyamikira zomwe wophunzirayo wachita. Azichita zimenezi kwa mphindi ziwiri. Woyang’anira sukulu akamaitana wokamba nkhani, asamanene mfundo yomwe m’bale kapena mlongo wapatsidwa kuti atsatire. Wophunzira akamaliza kukamba nkhani yake, woyang’anira sukuluyo azimuyamikira, azinena mfundo yomwe wophunzirayo anapatsidwa komanso azitchula zomwe wophunzirayo wachita bwino. Azinenanso zimene wophunzirayo akufunika kukonza zomwe walephera kutsatira pokamba nkhani yake.
9 Fomu yolangizira ya wophunzira ikupezeka patsamba 79 mpaka 81 m’buku la Sukulu ya Utumiki. Wophunzira akamaliza kukamba nkhani yake, woyang’anira sukulu azilemba zofunikira m’buku la wophunzirayo ndipo kenako azionana naye n’kumufunsa ngati anapanga ‘zochita’ zomwe zili pa mfundo yomwe anapatsidwa kuti atsatire. Woyang’anira sukulu akhozanso kuyamikira kapena kupereka malangizo ena kwa wophunzirayo pambuyo pa misonkhano kapena pa nthawi ina. Wophunzirayo aziona kuti cholinga cha zonsezi ndi kumuthandiza kuti apite patsogolo mwauzimu.—1 Tim. 4:15.
10 Ngati wophunzira wadya nthawi, woyang’anira sukulu ayenera kupereka chizindikiro chomudziwitsa kuti nthawi yake yatha, mwina poimba kabelu kapena kuchita zinthu zina. Zikatere wophunzirayo ayenera kungomalizitsa chiganizo chomwe wayamba kale n’kuchoka papulatifomu.—Onani tsamba 282 m’ndime 4 m’buku la Sukulu ya Utumiki.
11 Aliyense amene ali woyenerera kulowa mu sukuluyi akhoza kulembetsa kwa woyang’anira sukulu. (Onani buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 282 ndime 6.) Zimene timaphunzira m’sukuluyi zimatithandiza kuti tizilalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino molimba mtima, mwaulemu komanso mwachikondi. N’zosakayikitsa kuti Yehova amasangalala kwambiri ndi anthu amene aphunzitsidwa m’sukuluyi chifukwa amathandizira kuti dzina lake lilemekezeke.—Sal. 148:12, 13; Yes. 50:4.