Malangizo kwa Oyang’anira Sukulu
MU MPINGO uliwonse, mkulu amasankhidwa kukhala woyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Ngati mwapatsidwa udindo umenewu, muyenera kusonyeza kuti mumasangalala nayo sukuluyo ndipo sonyezani chidwi ndi mmene wophunzira aliyense akupitira patsogolo. Mzimu umenewo udzathandiza ambiri kupindula ndi sukuluyi pampingo panu.
Mbali yofunika kwambiri paudindo wanu ndiyo kuchititsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu pampingo panu mlungu uliwonse. M’malo moganizira ophunzira okha amene ali ndi mbali zawo, kumbukirani kuti palinso omvera. Chititsani sukuluyo m’njira yolimbikitsa mpingo wonse. Perekani zikumbutso zothandiza zokhudza zolinga za sukulu zotchulidwa pamasamba 5 mpaka 8 m’buku lino.
Khalani ndi chidwi mwa ophunzira onse, kaya munawapatsa mbali zoŵerenga, nkhani zokambirana, kapena nkhani zokamba wekha. Athandizeni kuti asamaone mbali zimene amapatsidwa ngati nkhani chabe, komanso ngati mwayi wopitira patsogolo mu utumiki wawo kwa Yehova. Inde, khama limene amasonyeza lidzawathandiza kwambiri kupita patsogolo. Koma n’kofunikanso kuti muzisonyeza kuti mumawafunira zabwino, mwa kuwathandiza kumvetsa phindu lake la malangizo operekedwa, komanso kufotokoza mmene angawagwiritsire ntchito. Kuti muchite zimenezo, mvetserani nkhani iliyonse mosamala kuti mupereke malangizo othandiza.
Onetsetsani kuti mukuyamba ndi kumaliza sukulu panthaŵi yake. Sonyezani chitsanzo chabwino mwa kusunga nthaŵi yoperekedwa yokambira ndemanga zanu. Ngati wophunzira wadya nthaŵi, inuyo kapena wina wokuthandizani apereke chizindikiro. Pamenepo wophunzirayo amalize sentensi imene akunenayo ndipo achoke papulatifomu. Ngati wina papulogalamuyo adya nthaŵi, fupikitsani ndemanga zanu, ndiyeno kambiranani ndi mbaleyo pambuyo pa msonkhano.
Ngati inuyo mulipo, chititsani sukulu. Koma ngati inu palibe, achititse mkulu wina amene bungwe la akulu linamusankhiratu. Ngati mukufuna wokuthandizani kukonza ndandanda, kulemba masilipi a nkhani ndi kuwagaŵira, kapena kupeza oloŵa m’malo mwa ena m’pulogalamuyo, bungwe la akulu lisankhe mtumiki wotumikira woti azikuthandizani mbali zimenezi.
Kulemba Ophunzira. Limbikitsani ofalitsa onse kuti alembetse m’sukulu. Anthu ena amene amayanjana ndi mpingo mokangalika angalembetse ngati akugwirizana ndi ziphunzitso za Baibulo ndipo akukhala ndi moyo mogwirizana ndi mfundo za makhalidwe abwino zachikristu. Munthu akanena kuti akufuna alembetse m’sukulu, muyamikireni. Ngati munthuyo sanakhalebe wofalitsa, inuyo ngati woyang’anira sukulu, mumuunikire ziyeneretso za sukuluyo. Mungachite bwino kukambirana naye pamaso pa amene amachita naye phunziro la Baibulo (kapena pamaso pa kholo lake lokhulupirira). Ziyeneretso zimenezi n’zofanana ndi za munthu wofuna kukhala wofalitsa wosabatizidwa. Zimapezeka pamasamba 97 mpaka 99 m’buku la Olinganizidwa Kukwaniritsa Utumiki Wathu. Khalani ndi ndandanda yolondola ya onse amene analembetsa m’sukulu.
Kugwiritsa Ntchito Fomu Yolangizira. Fomu yolangizira ya wophunzira aliyense ili m’buku lake la sukulu, pamasamba 79 mpaka 81. Malinga ndi zimene mitundu ya ‘kala’ ikusonyeza, mfundo yolangizira iliyonse kuyambira 1 mpaka 17 mungaigwiritse ntchito pamene wophunzira apatsidwa mbali ya kuŵerenga. Ngati ili nkhani yokambirana, mungagwiritse ntchito mfundo yolangizira iliyonse kupatulapo 7, 52, ndi 53. Pa nkhani zokamba wekha mungagwiritse ntchito mfundo zonse zolangizira kupatulapo 7, 18, ndi 30.
Pamene mugaŵira mfundo yolangizira monga woyang’anira sukulu, lembani deti ndi pensulo m’danga lili m’munsi mwa mawu akuti “Deti Logaŵira” pa mfundo yolangizirayo m’buku la wophunzira. Wophunzirayo akakamba nkhani yake, m’funseni pambali ngati anachita “Zochita” zimene zili kumapeto kwa nkhani yofotokoza mfundo yolangizirayo. Ngati anachita, chongani m’kabokosi kali pafomupo. Ngati mwaona kuti afunika asamalirebe mfundo imodzimodziyo, musalembe pa “Deti Lomaliza.” Mungalembe pamenepo kokha pamene wamaliza mfundoyo ndipo afunika kupita pa ina. Komanso, patsamba 82 m’buku la wophunzira, kumanzere kwa mtundu wa makambirano amene wagwiritsa ntchito, muyenera kulemba deti limene wakamba nkhani iliyonse. Malowo pa fomu yolangizira ndi pandandanda ya makambirano, akusonyeza kuti mafomuwo mukhoza kuwagwiritsa ntchito kaŵiri. Ophunzirawo ayenera kukhala ndi mabuku awo pasukulu.
Nthaŵi zonse gaŵirani mfundo yolangizira imodzi yokha. Pogaŵira mfundozo, ndi bwino kutsatira mmene azindandalikira pafomu. Komabe, ngati ophunzira ena akuoneka kuti akuchita bwino kwambiri, mungawalimbikitse kuti aziŵerenga ndi kuyesera mfundo zina paokha. Ndiyeno mungawagaŵire mfundo zimene mukuona kuti zingawathandize kwambiri kupita patsogolo kuti adzakhale okamba nkhani ndi aphunzitsi aluso.
Ngakhale wophunzira atakhala m’sukuluyo zaka zambiri, angapindule kwambiri mwa kuŵerenga ndi kugwiritsa ntchito malangizo a m’phunziro lililonse. Pofuna kuthandiza ophunzira amene ali ndi zosoŵa zapadera, mungasankhe maluso a kulankhula amene angalimbikirepo m’malo mongotsatira mmene awandandalikira pa fomu yolangizira.
Kupereka Malangizo. Popereka malangizo, gwiritsani ntchito zitsanzo za m’Baibulo ndi mfundo zake za makhalidwe abwino. Ophunzira ayenera kuona kuti malangizo amene mukupereka, komanso mzimu umene mukuwaperekera, mukuyendera malangizo abwino koposa a m’Mawu a Mulungu.
Kumbukirani kuti ndinu ‘wantchito mnzawo’ wa abale ndi alongo anu. (2 Akor. 1:24) Mofanana ndi iwo, inunso muyenera kuyesetsa nthaŵi zonse kulankhula ndi kuphunzitsa mwaluso. Phunzirani panokha buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, gwiritsani ntchito malangizo ake, ndipo perekani chitsanzo chabwino kwa ena kuti iwonso achite chimodzimodzi.
Mmene mukutero, chitani zotheka kuti muthandize ophunzira kukhala aŵerengi abwino, okamba nkhani mogwira mtima, ndi aphunzitsi aluso. Kuti muchite zimenezo, yesetsani kupereka chithandizo chofunika chilichonse kuti ophunzirawo awadziŵe bwino maluso a kulankhula osiyanasiyana, chifukwa chake ali ofunika, ndi mmene angawapezere. Buku lino lalembedwa m’njira yokuthandizani kuchita zimenezo. Komabe, pali zambiri zimene mungawathandize nazo m’malo mongoŵerenga mawu a m’bukuli. Fotokozani mfundo za mawuwo ndi mmene angazigwiritsire ntchito.
Ngati wophunzira wachita bwino pa mfundo ina, muyamikireni. Fotokozani mwachidule chimene chachititsa mfundoyo kukhala yogwira mtima kapena kufunika kwa mmene waisamalira. Ngati afunikira kulimbikirabe pamfundoyo, onetsetsani kuti wamvetsa chifukwa chake. Fotokozani mmene angachitire. Lankhulani molunjika, komanso mwachikondi.
Kumbukirani kuti kulankhula pamaso pa gulu kumakhala chinthu chovuta kwa anthu ambiri. Anthu ena akaona kuti sanachite bwino, sakhala ndi mtima wofuna kupitiriza. Tengerani chitsanzo cha Yesu amene sanathyole “bango lophwanyika” kapena kuzimitsa “nyali yofuka.” (Mat. 12:20) Ganizirani mmene malangizo anu angam’khudzire wophunzirayo malinga ndi mmene mukumudziŵira. Popereka malangizo, onani ngati wophunzirayo ali watsopano kapena ndi wofalitsa wofikapo. Kuyamikira kochokera pansi pa mtima komanso koyenerera kumalimbikitsa anthu kuyesetsa mmene angathere.
Chitani ndi wophunzira aliyense mwaulemu. Aroma 12:10 amatiuza kuti: “Mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” Limeneli ndi langizo loyeneradi mlangizi wa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu! Ngati wophunzirayo ndi wachikulire kwa inu, tsatirani langizo la pa 1 Timoteo 5:1, 2. Komabe mosasamala kanthu za msinkhu wa munthu, ngati malangizo owongolera kachitidwe ka zinthu aperekedwa mwachikondi, kaŵirikaŵiri amalandiridwa mosavuta.—Miy. 25:11.
Popereka malangizo, unikani kwa wophunzirayo cholinga cha sukuluyi. Cholingacho sindicho kuyamikiridwa kuti mwachita bwino ndi kuuzidwa kupita pa mfundo ina ayi; kapena kukhala wokamba nkhani kapena mphunzitsi woti ena azimusirira ayinso. (Miy. 25:27) Chimene timafuna ndi kugwiritsa ntchito mphatso yathu ya kulankhula potamanda Yehova ndi kuthandiza ena kuti amudziŵe ndi kumukonda. Cholinga cha sukuluyi ndicho kutiphunzitsa kuchita mwaluso ntchito yofotokozedwa pa Mateyu 24:14 ndi 28:19, 20. Abale obatizidwa amene amachita bwino, m’kupita kwa nthaŵi amapatsidwa udindo wosamalira “gulu la Mulungu” monga okamba nkhani za onse ndi aphunzitsi.—1 Pet. 5:2, 3.
Pamene mugaŵira ophunzira mfundo yolangizira yotsatira, apempheni kuti ayambe msanga kuŵerenga nkhani ya m’buku lawo yofotokoza mfundoyo. Alimbikitseni kukagwiritsa ntchito zimene akaŵerenge pokonzekera mbali zawo m’sukulu, pokambirana ndi anthu tsiku ndi tsiku, poyankha pamsonkhano, ndi mu utumiki wa kumunda.
Kugaŵira Nkhani. Gaŵirani nkhani kukali milungu itatu kapena kuposerapo. Nkhani zonse ziyenera kugaŵiridwa mwa kulemba ngati kungatheke.
Nkhani zolangiza mpingo zipatsidwe kwa akulu, makamaka aja amene angazikambe bwino, komaso atumiki otumikira amene ali aphunzitsi aluso.
Pofuna kudziŵa nkhani zimene mungagaŵire abale kapena alongo, tsatirani malangizo ali pa ndandanda ya sukulu. Ngati abale alipo ochepa koma alongo ndi ambiri amene amakamba nkhani za ophunzira, samalani kuti abale azikhala ndi mipata yokwanira yokamba nkhani zina zosakhala zoŵerenga chabe.
Ganizirani mikhalidwe ya munthu pamene mukugaŵira nkhani. Kodi n’kofunikiradi kuti mugaŵire nkhani m’sukulu mkulu kapena mtumiki wotumikira tsiku limene alinso ndi nkhani pa Msonkhano wa Utumiki, kapena mlungu umodzimodzi umene alinso ndi nkhani ya onse pampingo? Kodi n’kofunikiradi kugaŵira mlongo nkhani patsiku limene mwagaŵiranso mwana wake wamng’ono nkhani, amene angam’fune kuti amuthandize pankhani yake? Makamaka wachichepere kapena wophunzira Baibulo wosabatizidwa, kodi nkhani imene mwam’patsa ndi yomuyenerera? Onetsetsani kuti nkhani imene mwaperekayo ikugwirizana ndi mfundo yolangizira imene wophunzirayo akuisamalira.
Pa nkhani zopatsidwa kwa alongo, wophunzirayo kaŵirikaŵiri adzasankha yekha mtundu wa makambirano wogwirizana ndi malangizo ali pamasamba 78 ndi 82. Mugaŵireni womuthandiza mmodzi, koma ngati angafune wina wowonjezera angasankhe amene angafune. Ngati wophunzira apempha kuti mum’patse wom’thandiza wakutiwakuti amene angachite bwino kwambiri pamakambirano amene wasankha, ndi bwino kuganizira pempho limenelo.
Makalasi Aang’ono. Ngati muli ndi ophunzira opitirira 50, ganizirani zokhazikitsa makalasi aang’ono a nkhani za ophunzira zokha. Malinga ndi mikhalidwe ya kwanuko, makonzedwe ameneŵa angakhale a nkhani zonse za ophunzira kapena ziŵiri zomalizira.
Kalasi yaing’ono iliyonse izikhala ndi mlangizi woyenerera, makamaka mkulu. Ngati kuli kofunikira, mtumiki wotumikira woyenerera bwino angagwirizire udindo umenewo. Bungwe la akulu n’limene liyenera kusankha alangizi ameneŵa. Chitani zinthu mogwirizana ndi alangizi ameneŵa kuti muzitha kutsatira bwino mbali zimene ophunzira akuzisamalira kulikonse kumene angakambire nkhani yawo yotsatira.
Makalasi Apadera Akuŵerenga. Bungwe la akulu likaona kuti ambiri mumpingo akufunika chithandizo kuti azitha kuŵerenga bwino chinenero cha mpingowo, angakhazikitse kalasi imeneyi ngati mbali ina ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Kalasiyi ingakhale yophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba, kapena ingangokhala yophunzitsa kuŵerenga bwino basi.
Makalasiŵa asachitike nthaŵi imodzi ndi nkhani za ophunzira mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Kuti muwathandize mokwanira, padzafunikira nthaŵi yokwanira imene siingapezeke panthaŵi ya Sukulu ya Utumiki. Akulu angaone zofunikira ndi malo kumene ingamachitikire. Malinga ndi mkhalidwewo, angakonze dongosolo lokhala ndi kalasi ya kagulu kapena kumawaphunzitsa mmodzimmodzi payekha.
Padzafunikiranso mphunzitsi woyenerera. Zingakhale bwino ngati udindowo ungapatsidwe kwa mbale amene amaŵerenga bwino komanso wochidziŵa bwino chinenerocho. Ngati mbale woteroyo palibe, akulu angapemphe mlongo wokhoza m’mbali zimenezo komanso wachitsanzo chabwino. Mlongoyo ayenera kumavala chophimba kumutu pophunzitsa.—1 Akor. 11:3-10; 1 Tim. 2:11, 12.
Buku lakuti Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba latuluka m’zinenero zambiri. Lalembedwa ndi cholinga chophunzitsa maluso oyambirira a kuŵerenga ndi kulemba. Mungagwiritsenso ntchito mabuku ena ophunzirira, malinga ndi mmene ophunzirawo adziŵira kuŵerenga. Pamene ophunzira apitako patsogolo ndithu, alimbikitseni kuti ayambe kumakamba nkhani za mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Monga woyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, mungachite zambiri kuti mpingo upindule. Muzikonzekera bwino, ndipo mogwirizana ndi uphungu wa pa Aroma 12:6-8, samalirani udindo wanu ngati chuma chimene Mulungu wakuikizani.