Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/14 tsamba 7
  • Nyimbo Zatsopano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyimbo Zatsopano
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Tizitamanda Yehova Mosangalala Poimba Nyimbo
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Kodi Mwakonzekera Kuimbira Yehova Pamisonkhano?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Imbirani Yehova
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Mfundo Zothandiza Pophunzira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
km 12/14 tsamba 7

Nyimbo Zatsopano

1 Pamsonkhano wapachaka waposachedwapa, womwe unachitika pa 4 October 2014, analengeza zoti akufuna kukonzanso buku lathu la nyimbo lomwe tikugwiritsa ntchito panoli. Anthu amene anali pamsonkhanowu anasangalala kwambiri ndi chilengezochi. Anthuwa anakumbutsidwa kuti nyimbo zathu ndi zofunika kwambiri pa kulambira kwathu.—Sal. 96:2.

2 Koma mwina mungafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani bukuli likufunika kukonzedwanso?’ Pali zifukwa zingapo. Choyamba n’choti panopa tikumvetsa bwino tanthauzo la malemba ena kuposa poyamba ndipo chifukwa cha zimenezi mawu ena a m’buku la nyimbo yathu ayenera kusintha. (Miy. 4:18) Chifukwa china n’choti pakufunika kusintha mawu ena m’buku la nyimbo lachingelezi popeza Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi analikonzanso. Choncho mawu a m’buku la nyimboli ayenera kusinthidwa kuti agwirizane ndi Baibulo lokonzedwanso. Koma kuchita zimenezi ndi ntchito yaikulu choncho taona kuti tigwiritse ntchito mwayi umenewu kuti tiwonjezere nyimbo zina zatsopano m’bukuli.

3 Kodi tiyenera kudikira kuti buku latsopano lidzasindikizidwe kuti tidzayambe kuimba nyimbo zatsopanozi? Ayi. Ndife osangalala kukudziwitsani kuti posachedwapa nyimbo zatsopanozi zizipezeka pa webusaiti yathu ya jw.org. Nyimbo yatsopano ikatuluka, iziikidwa pa ndandanda ina ya Msonkhano wa Utumiki kuti ikhale nyimbo yotsekera misonkhano ndipo izilembedwa kuti “nyimbo yatsopano.”

4 Kodi Nyimbo Zatsopanozi Tingaziphunzire Bwanji? Nthawi zambiri kuphunzira nyimbo yatsopano kumakhala kovuta. Komabe m’malo ‘mongokhala chete’ pa misonkhano tiyenera kumaimba nyimbo zathu ngati mmene ankachitira munthu wina yemwe analemba nawo masalimo. (Sal. 30:12) Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti musavutike kuphunzira nyimbo zatsopanozi.

  • Nyimbo yatsopano ikaikidwa pa webusaiti yathu, muziimvetsera mobwerezabwereza. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muizolowere.

  • Muziwerenga mawu a nyimboyo ndipo muziyesetsa kuwaloweza.

  • Kenako yesani kuimba mawu ake potsatira malimba mpaka mutaidziwa.

  • Muziimba nyimbo zatsopanozi pa kulambira kwa pabanja mpaka aliyense atazizolowera.

5 Kutsogoloku, nyimbo yatsopano ikaikidwa kuti iimbidwe kumapeto kwa Msonkhano wa Utumiki, choyamba muziimvetsera yonse. Kenako muziimba potsatira malimba.

6 Ndi mwayi waukulu kuimba nyimbo pamisonkhano chifukwa timakhala tikulemekeza Yehova pamodzi ndi abale ndi alongo athu. Choncho, pa nthawi yoimba nyimbo, si bwino kumayendayenda kapena kutuluka panja popanda chifukwa chomveka.

7 Palinso njira ina imene tingasonyezere kuti timaona kuti ndi mwayi waukulu kuimba nyimbo pa misonkhano. Pa msonkhano wadera komanso wachigawo pamaikidwa nyimbo zoti timvetsere chigawo chilichonse chisanayambe. Chaka chilichonse, abale ndi alongo osiyanasiyana amapita ku Patterson, mumzinda wa New York, kawiri pachaka n’cholinga choti akakonze nyimbo zosangalatsa zimenezi. Choncho ndi bwino kumvera tcheyamani akanena kuti tikhale pansi kuti tizimvetsera nyimbozi. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kuti tikonzekere kumvetsera nkhani zomwe zikambidwe pa misonkhanoyo.—Ezara 7:10.

8 Timaliza misonkhano yathu ndi nyimbo yatsopano ya mutu wakuti, “Ufumu Umene Ukulamulira Kumwamba Ubwere.” Nyimboyi inaimbidwanso pa msonkhano wapachaka uja ndipo inakonzedwa pokondwerera kuti patha zaka 100 Ufumu wa Mulungu ukulamulira.

9 Nyimbo zatsopanozi ndi zinthu “zabwino” zimene Yehova watipatsa. (Mat. 12:35a) Choncho tiyeni tiyesetse kuphunzira nyimbozi komanso kumaziimba kuchokera pansi pa mtima n’cholinga choti tizitamanda Mulungu wathu.—Sal. 147:1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena