Kodi Mwakonzekera Kuimbira Yehova Pamisonkhano?
1 Kukonzekera misonkhano kumaphatikizapo kukonzekera kuimba nyimbo zotamanda Yehova. Kodi mungakonzekere bwanji?
2 Muzimvetsa Zimene Nyimboyo Ikunena: Lemba limene pachokera nyimboyo komanso malemba ena opezeka kumapeto kwa nyimbo iliyonse, angakuthandizeni kuti mumvetse mfundo za m’Malemba zimene zili m’nyimboyo.
3 Muzikhala ndi Nthawi Yoimba: Ngati muli ndi wailesi ya CD, mlungu uliwonse mukamachita Kulambira kwa Pabanja, muzikhala ndi nthawi yophunzira nyimbo zatsopano. Muziimba nyimbo zimene zikaimbidwe pamisonkhano mlungu umenewo potsatira CD ya nyimbo zatsopanozi. Mungaphunzire kuimba zina mwa nyimbo zatsopanozi pomvetsera CD ya nyimbo za mawu yakuti: Sing to Jehovah—Vocal Renditions, Disc 1.
4 Kodi mwakonzekera kugwiritsa ntchito buku la nyimbo latsopano lakuti Imbirani Yehova? Bukuli tiyamba kuligwiritsa ntchito Lamlungu likubwerali pa phunziro la Nsanja ya Olonda ndipo kuti mudzakwanitse kuimba, yesetsani kukhala ndi nthawi yophunzira nyimbozi komanso kumvetsa uthenga wake.