Mfundo Zothandiza Pophunzira
Muziloweza “Nyimbo Zauzimu”
Lorraine wa ku U.S.A. ananena kuti, “Ndikayamba kudziona ngati wachabechabe, Yehova amandilimbikitsa pogwiritsa ntchito nyimbo za pa JW Broadcasting®.”
Akhristu akhala akugwiritsa ntchito “nyimbo zauzimu” polambira. (Akol. 3:16) Ngati mutaphunzira komanso kuloweza nyimbozi zingakuthandizeni ngakhale pamene mulibe buku kapena chipangizo chamakono. Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti muzitha kuloweza nyimbozi.
Muziwerenga mawu ake mosamala kuti mumvetse tanthauzo lake. Munthu amatha kukumbukira mawu ngati wamvetsa tanthauzo lake. Pa jw.org pamapezeka mawu a nyimbo zathu kuphatikizapo za Broadcasting komanso za ana. Pitani pamene alemba kuti Laibulale, kenako Nyimbo.
Muzilemba mawu a nyimboyo pamanja. Mukamachita zimenezo m’pamene mawu a nyimboyo amakhazikika m’maganizo mwanu.—Deut. 17:18.
Muziyeserera motulutsa mawu. Muziwerenga komanso kuimba mawu a nyimboyo mobwerezabwereza.
Dziyeseni kuti muone ngati mwaloweza. Muziyesa kukumbukira mawu a nyimboyo popanda kuonera, kenako muziona ngati mwawaloweza.