Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 December tsamba 5
  • Tizitamanda Yehova Mosangalala Poimba Nyimbo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizitamanda Yehova Mosangalala Poimba Nyimbo
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Imbirani Yehova Zitamando
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Nyimbo za Ufumu Zimatithandiza Kukhala Olimba Mtima
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nyimbo Zatsopano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Mfundo Zothandiza Pophunzira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 December tsamba 5
Khalani Bwenzi la Yehova Nyimbo 84: Timadzipereka

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizitamanda Yehova Mosangalala Poimba Nyimbo

Paulo ndi Sila ali m’ndende, anatamanda Yehova poimba nyimbo. (Mac. 16:25) Sitikukayikira kuti nyimbo zimene anaimba zinawathandiza kuti apitirize kupirira. Nanga bwanji masiku ano? Nyimbo zimene timaimba polambira komanso nyimbo zina zomwe zimaimbidwa ndi gulu lathu, zimatilimbikitsa komanso kutithandiza kuti tikhalebe okhulupirika tikakumana ndi mayesero. Kuposa pamenepo, nyimbozi zimatamanda Yehova. (Sal. 28:7) Timalimbikitsidwa kuti tiziyesetsa kuloweza mawu a zina mwa nyimbozi. Kodi inuyo munayesapo kuchita zimenezi? Tikhoza kumagwiritsa ntchito nthawi ya kulambira kwa pabanja kuti tiphunzire komanso kuloweza mawu a nyimbo zathu.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ANA ANATAMANDA YEHOVA POIMBA NYIMBO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Atsikana awiri akuimba m’chipinda chojambulira mawu

    Kodi kuimba nyimbo za Ufumu kungatithandize bwanji?

  • Mlongo akukonzeratu zinthu ana odzaimba asanabwere

    Kodi a m’dipatimenti yojambula amakonzekera bwanji akamafuna kujambula nyimbo?

  • Banja likuimba pa nthawi ya kulambira kwa pabanja

    Kodi ana komanso makolo awo amakonzekera bwanji nthawi yojambula nyimbo isanafike?

  • Ana akuimba

    Kodi ndi nyimbo za Ufumu ziti zimene inuyo mumakonda, nanga n’chifukwa chiyani mumazikonda?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena