Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 April tsamba 6
  • Nyimbo za Ufumu Zimatithandiza Kukhala Olimba Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyimbo za Ufumu Zimatithandiza Kukhala Olimba Mtima
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Tizitamanda Yehova Mosangalala Poimba Nyimbo
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Mfundo Zothandiza Pophunzira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Nyimbo Zatsopano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kodi Mwakonzekera Kuimbira Yehova Pamisonkhano?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 April tsamba 6

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Nyimbo za Ufumu Zimatithandiza Kuti Tikhale Olimba Mtima

M’bale Erich Frost wakhala pafupi ndi piano

Paulo ndi Sila ali m’ndende ankatamanda Mulungu poimba nyimbo. (Mac. 16:25) Nawonso Akhristu anzathu omwe anali kundende ya Sachsenhausen, pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi ku Germany komanso ena omwe anali mu ukapolo ku Siberia, ankaimba nyimbo za Ufumu. Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti nyimbo zimalimbikitsa kwambiri Akhristu pa nthawi ya mavuto.

Posachedwapa buku la nyimbo la mutu wakuti Imbirani Yehova Mosangalala, liyamba kupezeka m’zinenero zambiri. Choncho tikangopeza bukuli, tiyesetse kuloweza mawu a nyimbozi. Tingamayeserere kuimba pa nthawi ya kulambira kwa pabanja. (Aef. 5:19) Tikamachita zimenezi, mzimu woyera udzatithandiza kukumbukira nyimbozi pa nthawi imene tili m’mavuto. Nyimbo za Ufumu zimatithandizanso kuti tiziganizira kwambiri za zinthu zimene tikuyembekezera. Choncho zingatilimbikitse tikakumana ndi mavuto. Komanso pa nthawi imene zinthu zili bwino tingathe ‘kuimba mosangalala’ chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima. (1 Mbiri 15:16; Sal. 33:1-3) Ndiye tiyeni tiyesetse kuti tizizidziwa bwino nyimbo zathu za Ufumu.

ONERANI VIDIYO YAKUTI NYIMBO IMENE INALIMBIKITSA AKAIDI. KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene zinachititsa kuti M’bale Frost alembe nyimbo?

  • Kodi nyimboyi inalimbikitsa bwanji abale omwe anali ku ndende ya Sachsenhausen?

  • Kodi nyimbo za Ufumu zingatilimbikitse bwanji pa zochita zathu zatsiku ndi tsiku?

  • Kodi ndi nyimbo za Ufumu ziti zimene mukufuna kuti muziloweze?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena