Kukonzekera Bwino N’kofunika Kuti Tiziphunzitsa Mwaluso
Yesu anafunsidwa ndi anthu awiri za moyo wosatha ndipo iye anayankha aliyense mogwirizana ndi zimene zinali mumtima mwa munthu aliyense. (Luka 10:25-28; 18:18-20) Choncho ngakhale kuti timadziwa kale zomwe timaphunzitsa, tiyenera kuzikonzekera bwino ndipo tiziganizira wophunzirayo. Tingachite bwino kudzifunsa kuti: Kodi ndi mfundo ziti zimene zingamuvute kuzimvetsa kapena kuzikhulupirira? Ndi malemba ati amene tingawerenge naye? Ndi ndime zingati zimene tingaphunzire naye? Ndingagwiritse ntchito zitsanzo, mfundo komanso mafunso ati kuti amvetse? Popeza Yehova ndi amene amakulitsa mbewu zimene timafesa, tiyenera kumupempha kuti atithandize ifeyo komanso wophunzira wathu.—1 Akor. 3:6; Yak. 1:5.