CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 92-101
Mukhoza Kumachitabe Zambiri Ngakhale Muli Okalamba
Mtengo wa kanjedza umatha kukhala zaka zoposa 100 koma n’kumaberekabe zipatso. Nawonso achikulire akhoza kumachitabe zambiri mofanana ndi mtengo umenewu
Achikulire akhoza kumachita zotsatirazi:
Kupempherera ena
Kuphunzira Baibulo
Kusonkhana komanso kupereka ndemanga
Kuuza ena zomwe zinawachikira pa moyo wawo
Kulalikira ndi mtima wonse