Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 February tsamba 8
  • Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikhulupirira Kwambiri Mlengi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikhulupirira Kwambiri Mlengi
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Fufuzani Umboni
    Galamukani!—2021
  • Mungapeze Thandizo
    Galamukani!—2020
  • Anasiya Tsankho
    Galamukani!—2020
  • Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 February tsamba 8

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikhulupirira Kwambiri Mlengi

Chilengedwe chimalengeza ulemerero wa Yehova. (Sal. 19:1-4; 139:14) Komabe dziko la Mdyerekezili limalimbikitsa mfundo zonyoza Mulungu pa nkhani ya mmene moyo unayambira. (Aroma 1:18-25) Kodi mungatani kuti mfundo zimenezi zisazike mizu m’maganizo ndiponso mumtima mwa ana anu? Muyenera kuwathandiza kuyambira ali aang’ono kuti azikhulupirira Yehova ndiponso kudziwa kuti iye amawakonda. (2 Akor. 10:4, 5; Aef. 6:16) Muzikambirana nawo kuti mudziwe maganizo awo pa nkhani zimene amaphunzira kusukulu. Kuti muziwafika pamtima, muzigwiritsa ntchito mabuku, webusaiti yathu ndiponso mavidiyo.​—Miy. 20:5; Yak. 1:19.

Bambo akuphunzitsa ana ake zokhudza chilengedwe; ana ali m’kalasi ndipo akuphunzira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina; Zimene Achinyamata Anzanu Amanena​​—⁠Kukhulupirira Kuti Kuli Mulungu

ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA​—KUKHULUPIRIRA KUTI KULI MULUNGU, NDIPO KENAKO KAMBIRANANI NAWO MAFUNSO AWA:

  • Kodi anthu ambiri amanena zotani pa nkhani ya kukhulupirira Mulungu?

  • Kodi kusukulu kwanu amaphunzitsa zotani pa nkhaniyi?

  • N’chiyani chimakutsimikizirani kuti Yehova alipodi?

  • Kodi mungathandize bwanji munthu kuzindikira kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse?

ZINTHU ZINA ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI

• Nkhani za pa JW.ORG: “Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo” (Ana azaka zosapitirira zitatu)

• Vidiyo: Khalani Bwenzi la Yehova​—“Yehova . . . Analenga Zinthu Zonse”

• Nkhani za mu Galamukani!: “Kodi Zinangochitika Zokha?”

• Zoti achinyamata achite pa JW.ORG: “N’chifukwa Chiyani Ndimakhulupirira Zoti Kuli Mulungu?”

• Nkhani za pa JW.ORG: “Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?” (pali magawo 4)

• Mavidiyo a pa JW Broadcasting: “Mmene Moyo Unayambira”

• Vidiyo Yachingelezi: The Wonders of Creation Reveal God’s Glory

• Kabuku Kachingelezi: Was Life Created?

• Buku Lachingelezi: Is There a Creator Who Cares About You?

Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?

Kabukuka kanapangidwira anthu amene sadziwa zambiri zokhudza Baibulo, makamaka anthu amene ali m’zipembedzo zomwe si zachikhristu. Ngati mukuphunzira buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa ndi munthu wotereyu, muziphunzira naye gawo limodzi la m’kabukuka kumayambiriro kapena kumapeto kwa phunziro lanu. Zimenezi zingamuthandize kuti adziwe zimene zili m’Baibulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena