MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Tizisonyeza Ulemu Tikafika Pakhomo
Akhristufe tili ngati “choonetsedwa m’bwalo la masewera kudziko.” (1 Akor. 4:9) N’chifukwa chake sitiyenera kudabwa kuti anthu ena amatisunzumira pawindo kapena kutimvetsera ali m’nyumba zawo. Nyumba zina zimakhala ndi makamera omwe amathandiza kuti eninyumba aziona, kumva ndiponso mwina kujambula zimene tikulankhula. Ndiye tiyeni tione njira zina zimene tingasonyezere ulemu tikafika pakhomo la munthu amene tikufuna kumulalikira.—2 Akor. 6:3.
KHALIDWE LANU (Afil. 1:27):
Mungasonyeze ulemu kwa eninyumba popewa kusunzumira m’nyumba zawo. Simuyeneranso kudya, kumwa, kulankhula pafoni kapena kulemba mameseji mukafika pakhomo la munthu
ZOLANKHULA ZANU (Aef. 4:29):
Mukafika pakhomo, musamalankhule zilizonse zimene sizingasangalatse mwininyumbayo. Ofalitsa ena amasankha kusiya kaye kulankhulana n’cholinga choti aziganizira zimene akufuna kukambirana ndi mwininyumbayo