CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 14-16
Mulungu Adzakhala “Zinthu Zonse kwa Aliyense”
Anthu amene ndi okhulupirika kwa Yehova adzakhala ndi tsogolo labwino kwambiri. Tikamafotokozera ena zinthu zosangalatsa zomwe tikuyembekezera sitikayikira kuti zidzachitikadi. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti aziyerekezera mmene zidzakhalire kumapeto Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu pamene Yehova adzakhale “zinthu zonse kwa aliyense.”
Ndi chiyembekezo chiti chomwe chimakusangalatsani kwambiri ndipo n’chifukwa chiyani?
N’chiyani chimakutsimikizirani kuti zimene Mulungu analonjeza zidzakwaniritsidwa?