MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mungaphunzire Zambiri Kuchokera kwa Achikulire
Kodi mwangoikidwa kumene kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu? N’kutheka kuti muli ndi luso kapena maphunziro enaake omwe anzanu amene ali paudindo womwewo alibe. Komabe dziwani kuti mukhoza kuphunzira zambiri kuchokera kwa abale amenewa komanso ena omwe anasiya kutumikira paudindowu chifukwa cha ukalamba, matenda kapena maudindo a m’banja.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZILEMEKEZA ABALE ACHIKULIRE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
1. Kodi M’bale Richards anasonyeza bwanji kuti amalemekeza M’bale Bello?
2. Kodi Ben analakwitsa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tikutero?
3. Kodi Ben anaphunzirapo chiyani pa chitsanzo cha Elisa?
4. Kaya ndinu m’bale kapena mlongo, kodi mungasonyeze bwanji kuti mumalemekeza Akhristu omwe amadziwa zambiri, nanga mungatani kuti muziphunzira kuchokera kwa iwo?