Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 August tsamba 3
  • Limbani Mtima Pamene Mapeto Akuyandikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Limbani Mtima Pamene Mapeto Akuyandikira
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo​—Kulimba Mtima
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Kukhala Olimba Mtima Sikovuta Kwambiri
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • ‘Limba Mtima Ndipo Ugwire Ntchitoyi’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Ndithandizeni Ndikhale Wolimba Mtima
    Imbirani Yehova Mosangalala
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 August tsamba 3

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Limbani Mtima Pamene Mapeto Akuyandikira

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI?: Posachedwapa padzikoli padzachitika zinthu zochititsa mantha ndipo tidzafunika kukhala olimba mtima komanso kusonyeza kuti timadalira kwambiri Yehova kuposa kale lonse. Chisautso chachikulu chidzayamba ndi kuwonongedwa kwa zipembedzo zonyenga. (Mt 24:21; Chv 17:16, 17) Pa nthawi yovuta imeneyo, n’kutheka kuti tizidzalengeza uthenga wamphamvu wachiweruzo. (Chv 16:21) Gogi wa ku Magogi adzatiukira. (Eze 38:10-12, 14-16) Pofuna kuteteza anthu ake, Yehova adzayambitsa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ (Chv 16:14, 16) Kuti tidzakhale olimba mtima kwambiri zimenezi zikamadzachitika, tikuyenera kukhala okhulupirika panopa tikamakumana ndi mayesero.

MMENE TINGACHITIRE ZIMENEZI:

  • Tiyenera kumatsatira mfundo zapamwamba za Yehova molimba mtima.​—Yes 5:20

  • Tiyenera kupitirizabe kulambira Yehova limodzi ndi Akhristu anzathu.​—Ahe 10:24, 25

  • Tiyenera kutsatira mwamsanga malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa.​—Ahe 13:17

  • Tiziganizira mmene Yehova anapulumutsira anthu ake m’mbuyomu.​—2Pe 2:9

  • Tizipemphera komanso kudalira Yehova.—Sl 112:7, 8

ONERANI MBALI INA YA VIDIYO YAKUTI KUTSOGOLOKU TIDZAFUNIKA KULIMBA MTIMA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Mbali ina ya vidiyo yakuti ‘Kutsogoloku Tidzafunika Kulimba Mtima.’ Mlongo Ali ku Nyumba ya Ufumu, ndipo akuda nkhawa ataona mpingo watsopano umene azisonkhana nawo mpingo wawo ukagawidwa n’kuphatikizidwa ndi mpingo wina.

    Kodi n’chifukwa chiyani zinali zovuta kuti ofalitsa ena amvere malangizo a akulu mpingo wawo utagawidwa n’kuphatikizidwa ndi mipingo ina?

  • Mbali ina ya vidiyo yakuti ‘Kutsogoloku Tidzafunika Kulimba Mtima.’ Mlongo Ali ku Nyumba ya Ufumu, ndipo akuda nkhawa ataona mpingo watsopano umene azisonkhana nawo mpingo wawo ukagawidwa n’kuphatikizidwa ndi mpingo wina.

    Kodi kulimba mtima kumagwirizana bwanji ndi kumvera?

  • Mbali ina ya vidiyo yakuti ‘Kutsogoloku Tidzafunika Kulimba Mtima.’ Wachinyamata akuda nkhawa pambuyo poganizira chithunzi chosonyeza Aramagedo chomwe chili m’buku lakuti “Ufumu wa Mulungu Ukulamulira.”

    N’chifukwa chiyani tidzafunika kulimba mtima pa Aramagedo?

  • Mbali ina ya vidiyo yakuti ‘Kutsogoloku Tidzafunika Kulimba Mtima.’ Yehosafati ndi anthu ena a ku Yuda afika kumene kunali adani awo ndipo angopeza kuti adani onse aphedwa.

    Tizikonzekera panopa zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo pomwe tidzafunike kulimba mtima

    Kodi ndi nkhani iti ya m’Baibulo imene ingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu chakuti Yehova adzatipulumutsa?​—2Mb 20:1-24

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena