CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 25-26
Chinthu Chofunika Kwambiri M’chihema
Likasa linali chinthu chofunika kwambiri m’chihema komanso mumsasa wonse wa Aisiraeli. Mtambo umene unkakhala pakati pa akerubi awiri pamwamba pa chivundikiro chophimba machimo cha Likasa unkaimira kukhalapo kwa Mulungu. Chaka chilichonse pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, mkulu wa ansembe ankalowa m’Malo Oyera Koposa n’kudontheza magazi a ng’ombe yamphongo ndiponso a mbuzi patsogolo pa chivundikiro kuti aphimbe machimo a Aisiraeli. (Le 16:14, 15) Zimenezi zinkaimira pamene Yesu, yemwe ndi Mkulu wa Ansembe wamkulu, anakaonekera kwa Yehova kumwamba kuti apereke nsembe ya dipo.—Ahe 9:24-26.
Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi madalitso amene tingapeze chifukwa cha dipo.
MALEMBA
MADALITSO
chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha
kukhululukidwa machimo athu
chikumbumtima choyera
Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipeze madalitso amenewa?