Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 September tsamba 11
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri mu Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri mu Utumiki
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri Mu Utumiki​—Muzifunsa Mafunso
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muziwafika Pamtima
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Muzilola Kuti Yehova Azikuthandizani Kudzera M’pemphero
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 September tsamba 11

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzilola Kuti Atumiki Anzanu Azikuthandizani

Yehova watipatsa ‘gulu lonse’ la abale ndi alongo athu kuti azitithandiza. (1Pe 5:9) Iwo angatithandize kuthana ndi mavuto omwe timakumana nawo mu utumiki. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anathandizidwa ndi Akula ndi Purisikila, Sila, Timoteyo ndi enanso.​—Mac 18:1-5.

Kodi atumiki anzanu angakuthandizeni bwanji mu utumiki? Angakuthandizeni kudziwa zomwe mungayankhe munthu wina akanena zinthu zosonyeza kuti sakufuna kuti mukambirane naye, mmene mungachitire maulendo obwereza, kapenanso mmene mungayambitsire komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Ngati mukuona kuti mukufunika thandizo, ganizirani za munthu wina mumpingo wanu amene angakuthandizeni, ndipo m’pempheni. N’zosakayikitsa kuti nonse mudzapindula komanso mudzasangalala kwambiri.​—Afi 1:25.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRITSA NTCHITO ZOMWE YEHOVA WATIPATSA KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA​—ABALE ATHU, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha mu vidiyo yakuti “Muzigwiritsa Ntchito Zomwe Yehova Watipatsa Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Abale Athu.” Anita ali ndi mlongo wina ndipo akuphunzira Baibulo ndi Jane.

    Kodi Anita anayesa kuchita chiyani pofuna kulimbikitsa Jane kuti akapezeke pamsonkhano wa mpingo?

  • Chithunzi cha mu vidiyo yakuti “Muzigwiritsa Ntchito Zomwe Yehova Watipatsa Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Abale Athu.” Mayi Mwira ali limodzi ndi Anita ndipo akumufotokozera Jane kuti anali mu bandi.

    N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha ofalitsa anzathu kuti tikhale limodzi tikamachititsa phunziro la Baibulo?

  • Chithunzi cha mu vidiyo yakuti “Muzigwiritsa Ntchito Zomwe Yehova Watipatsa Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Abale Athu.” Mayi Mwira akuphunzira Baibulo ndi Jane pa nthawi imene Anita anachoka.

    Ndi udindo wa mpingo wonse kuthandiza munthu kuti akhale wophunzira wa Yesu

    Kodi Jane ndi Mayi Mwira ankakonda zinthu zofanana ziti?

  • Kodi atumiki anzanu angakuthandizeni kukhala ndi maluso otani mu utumiki?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena