Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 September tsamba 13
  • Muzikumbukira Yehova Nthawi Zonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzikumbukira Yehova Nthawi Zonse
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Maganizo a Yehova Ndi Otani pa Nkhaniyi?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndikudwala Chonchi?
    Galamukani!—1997
  • Abulahamu Anali Munthu Wachikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Sangalalani Chifukwa Chogwira Ntchito Mwakhama
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 September tsamba 13

MOYO WATHU WACHIKRISTU

Muzikumbukira Yehova Nthawi Zonse

Ngati ntchito ikusowa, zikhoza kukhala zovuta kuika zinthu zokhudza Ufumu komanso chilungamo cha Mulungu pa malo oyamba m’moyo mwathu. Tikhoza kuyesedwa kuti tivomere ntchito imene ingatichititse kuti tisamakhale ndi nthawi yokwanira yotumikira Yehova kapenanso yosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Komabe tizikhulupirira kuti Yehova amasonyeza mphamvu zake “kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2Mb 16:9) Palibe chilichonse chimene chingalepheretse Atate wathu wachikondi kutithandiza komanso kutipatsa zonse zomwe timafunikira. (Aro 8:32) Choncho tikamaganizira za mtundu wa ntchito imene tikufuna kugwira, tizidalira kwambiri Yehova ndipo cholinga chathu chizikhala kupitirizabe kumutumikira.​—Sl 16:8.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRA NTCHITO NDI MOYO WONSE NGATI KUTI MUKUGWIRIRA YEHOVA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzigwira Ntchito Ndi Moyo Wonse Ngati Kuti Mukugwirira Yehova.” Thomas akuyang’anitsitsa Jason pamene akukana kulandira chiphuphu kuntchito.

    N’chifukwa chiyani Jason anakana kulandira chiphuphu?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzigwira Ntchito Ndi Moyo Wonse Ngati Kuti Mukugwirira Yehova.” Jason akukataya zinyalala za kuntchito.

    Kodi tingagwiritse ntchito bwanji lemba la Akolose 3:23?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzigwira Ntchito Ndi Moyo Wonse Ngati Kuti Mukugwirira Yehova.” Jason akuphunzira Baibulo ndi Thomas.

    Kodi chitsanzo chabwino cha Jason chinathandiza bwanji Thomas?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzigwira Ntchito Ndi Moyo Wonse Ngati Kuti Mukugwirira Yehova.” Jason ndi Thomas aweruka mwamsanga kuntchito kuti akapezeke kumisonkhano.

    Muzilola kuti Yehova azikuthandizani mukamasankha zochita

    Kodi tingagwiritse ntchito bwanji lemba la Mateyu 6:22?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena