CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Sauli Anali Wodzichepetsa Poyamba
Sauli anali wodzichepetsa ndipo anazengereza kuti avomere ufumu (1Sa 9:21; 10:20-22; w20.08 10 ¶11)
Sauli sankachita zinthu mwaphuma anthu ena akamulankhula mwachipongwe (1Sa 10:27; 11:12, 13; w14 3/15 9 ¶8)
Sauli ankatsatira malangizo a mzimu woyera wa Yehova (1Sa 11:5-7; w95 12/15 10 ¶1)
Kudzichepetsa kudzatithandiza kuti tiziona mwayi wathu wa utumiki komanso zomwe timakwanitsa kuchita kuti ndi mphatso zochokera kwa Yehova. (Aro 12:3, 16; 1Ak 4:7) Ndiponso ngati tili odzichepetsa, tidzapitiriza kudalira Yehova kuti azititsogolera.