CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Mukayikakayika Mpaka Liti?”
Eliya anauza Aisiraeli momveka bwino kuti anafunika kusankha zinthu mwanzeru (1Mf 18:21; w17.03 14 ¶6)
Baala sanali mulungu wamoyo (1Mf 18:25-29; ia 88 ¶15)
Yehova anasonyeza m’njira yodabwitsa kwambiri kuti ndi Mulungu weniweni (1Mf 18:36-38; ia 90 ¶18)
Eliya anauza anthuwo kuti ankafunika kumvera Chilamulo cha Yehova kuti asonyeze kuti anali ndi chikhulupiriro. (De 13:5-10; 1Mf 18:40) Masiku ano timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro komanso ndife odzipereka kwa Mulungu tikamamvera malamulo ake ndi mtima wonse.