MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zochita Zanga Zimathandiza Kuti Gulu Lathu Likhale ndi Mbiri Yabwino
Anthu amaona zimene a Mboni za Yehovafe timachita. (1Ak 4:9) Tingadzifunse kuti, ‘Kodi zochita ndi zolankhula zanga zimachititsa kuti Yehova alemekezedwe?’ (1Pe 2:12) Timayesetsa kuti tisachite chilichonse chimene chingawononge mbiri yabwino imene a Mboni za Yehova akhala nayo kwa zaka zambiri.—Mla 10:1.
Mu zochitika zotsatirazi, lembani zimene Mkhristu angachite komanso mfundo ya m’Baibulo imene ingamuthandize:
Munthu wosakhulupirira akakunyozani
Zovala zanu kapena galimoto yanu ikada, kapenanso pakhomo panu pakakhala posasamalika
Ngati m’dziko lanu akhazikitsa lamulo limene ndi lokondera kapena lovuta kulitsatira
Kodi abale ndi alongo amene amagwira ntchito yofufuza m’Dipatimenti Yolemba amachita zotani kuti gulu lathu likhale ndi mbiri yabwino?
ONERANI VIDIYO YAKUTI KUTHANDIZA ANTHU KUKONDA KOMANSO KULEMEKEZA CHOONADI, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:
Kodi chimakuchititsani chidwi n’chiyani mukaganizira khama limene gulu limachita poyesetsa kuti lifalitse nkhani zolondola?