Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp21 No. 3 tsamba 15
  • Zomwe Mungasankhe Zingakhudze Tsogolo Lanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Mungasankhe Zingakhudze Tsogolo Lanu
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI TINGAKONDE BWANJI YEHOVA NDIPONSO KUMVERA MAWU AKE?
  • Tsogolo Lanu Lili M’manja Mwanu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
  • Mungathe Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • “Anthu Ofatsa Adzalandira Dziko Lapansi”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
  • Mawu Oyamba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
wp21 No. 3 tsamba 15
Munthu akuonetsa mnzake zinazake pafoni kumalo odyera.

Zomwe Mungasankhe Zingakhudze Tsogolo Lanu

Zaka 3,500 zapitazo, Yehova Mulungu anauza atumiki ake zomwe angachite kuti akhale ndi tsogolo labwino. Iye anati: “Ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero pamaso panu. Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu. Choncho inuyo ndi mbadwa zanu musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.”​—Deuteronomo 30:19.

Anthuwa ankafunika kusankha zinthu mwanzeru kuti akhale ndi tsogolo labwino. Ndi zimene nafenso tiyenera kuchita. Baibulo limafotokoza kuti zimenezi zingatheke “mwa kukonda Yehova Mulungu wanu [ndiponso] kumvera mawu ake.”​—Deuteronomo 30:20.

KODI TINGAKONDE BWANJI YEHOVA NDIPONSO KUMVERA MAWU AKE?

MUZIPHUNZIRA BAIBULO: Kuti muzikonda Yehova, choyamba mukufunika kuphunzira za iye kuchokera m’Baibulo. Mukamatero mudzaona kuti Mulungu ndi wachikondi ndiponso kuti amakufunirani zabwino. Mulungu amafuna kuti muzipemphera kwa iye chifukwa “amakuderani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Baibulo limanena kuti mukamayesetsa kuyandikira Mulungu, “iyenso adzakuyandikirani.”​—Yakobo 4:8.

MUZICHITA ZIMENE MWAPHUNZIRA: Kumvera Mulungu kumatanthauza kutsatira malangizo ake anzeru omwe amapezeka m’Baibulo. Mukatero, ‘mudzakhala ndi moyo wopambana, ndipo mudzachita zinthu mwanzeru.’​—Yoswa 1:8.

Kuti mudziwe zambiri, pitani pawebusaiti yathu ya jw.org, pomwe mungathe kuwerenga Baibulo la pa intaneti kapena mungapemphe kuti wa Mboni za Yehova azikuphunzitsani Baibulo kwaulere kuti mulimvetse bwino.

Mungachite bwino kwambiri kuyamba panopa kutsatira mfundo za m’Baibulo kuti mukhale ndi tsogolo labwino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena