Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 January tsamba 26-31
  • Muziphunzitsa Choonadi Mokoma Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muziphunzitsa Choonadi Mokoma Mtima
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI CHOONADI TINGACHIPEZE KUTI?
  • N’CHIFUKWA CHIYANI TIMALAKHULA ZOONA?
  • KODI TIZIPHUNZITSA BWANJI CHOONADI?
  • KODI TIZIPHUNZITSA CHOONADI PA NTHAWI ITI?
  • Kodi Mumatha Kuzindikira Choonadi?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Mupeze Mayankho a Mafunso Awa
    Pulogalamu ya Msonkhano Wadera Wokhala ndi Woyang’anira Dera wa 2025-2026
  • Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 January tsamba 26-31

MARCH 30–APRIL 5, 2026

NYIMBO NA. 76 Kodi Mumamva Bwanji?

Muziphunzitsa Choonadi Mokoma Mtima

“ Yehova Mulungu wa choonadi.”—SAL. 31:5.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zimene tingachite kuti tizilankhula zoona komanso tiziphunzitsa mfundo za choonadi m’njira yoti zizithandiza ena.

1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale m’banja la Yehova?

TIKAKUMANA ndi Mkhristu mnzathu kwa nthawi yoyamba, nthawi zambiri timakonda kufunsana kuti, “Kodi munayamba bwanji choonadi?” Ena amayankha kuti anabadwira m’choonadi. Pamene ena amanena kuti, “Ndangophunzira kumene.” Timayankha choncho chifukwa chakuti choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu chimakhudza chilichonse chimene timachita pa moyo wathu. Tikutero chifukwa chakuti tikhoza kukhala m’banja la Yehova pokhapokha ngati tasonyeza kuti timakonda choonadi n’kumachita zinthu mogwirizana ndi choonadicho. Zimenezi zikuphatikizapo kukhala oona mtima pa zimene timalankhula komanso kuchita.—Sal. 15:​1-3.

2. (a) Kodi anthu ankadziwa chiyani zokhudza Yesu? (b) Kodi mfundo za choonadi zimene Yesu ankaphunzitsa zikanawathandiza bwanji?

2 Nthawi zonse Yesu ankalankhula zoona. Adani ake anavomereza kuti iye ankalankhula zoona ngakhale kuti iwowo sankasangalala nazo. (Mat. 22:16) Ponena zokhudza mfundo za choonadi zimene ankaphunzitsa, Yesu anati: “Ndinabwera kudzagawanitsa anthu. Ndinabwera kudzachititsa kuti mwana wamwamuna atsutsane ndi bambo ake, mwana wamkazi atsutsane ndi mayi ake ndiponso kuti mkazi wokwatiwa atsutsane ndi apongozi ake aakazi.” (Mat. 10:35) Yesu sankafuna kuti anthu azitsutsa uthenga umene iye ndi otsatira ake ankalalikira koma ankadziwa kuti zimenezo zidzachitika. (Mat. 23:37) Iye ankadziwa kuti uthenga wake udzachititsa kuti anthu agawanike moti ena adzaukonda pamene ena adzadana nawo.—2 Ates. 2:​9-11.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Mofanana ndi Yesu timayesetsa kukhala oona mtima, n’kumalankhula zoona nthawi zonse ngakhale zitachititsa kuti anthu azidana nafe. Timalalikira komanso kuphunzitsa choonadi cha m’Baibulo ngakhale kuti anthu ena sangasangalale ndi zomwe tikuphunzitsazo. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitiyenera kuganizira nthawi komanso mmene tingalankhulire zinthu zoona, kuphatikizapo kulalikira uthenga wabwino? Ayi si choncho. Munkhaniyi choyamba tikambirana funso lakuti: Kodi choonadi tingachipeze kuti? Tikambirananso mafunso akuti: N’chifukwa chiyani tiyenera kuuza ena uthenga wabwino? Kodi tingawauze bwanji? Komanso kodi ndi nthawi iti imene tiyenera kuwauza? Mayankho a mafunsowa atithandiza kuti tizilankhula zoona komanso kuphunzitsa choonadi pogwiritsa ntchito mawu abwino ndiponso pa nthawi yoyenera.

KODI CHOONADI TINGACHIPEZE KUTI?

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti choonadi chimachokera kwa Yehova?

4 Choonadi chimachokera kwa Yehova. Zonse zimene amanena ndi zoona. Mwachitsanzo, iye amanena zoona pa nkhani ya zinthu zabwino komanso zoipa. (Sal. 19:9; 119:​142, 151) Zomwe wanena kuti zidzachitika, zimachitikadi. (Yes. 55:​10, 11) Nthawi zonse amakwaniritsa zimene walonjeza. (Num. 23:19) Ndipotu n’zosatheka kuti Yehova aname. (Aheb. 6:18) M’pake amadziwika kuti ndi “Mulungu wa choonadi.”—Sal. 31:5.

5. N’chifukwa chiyani n’zosavuta kudziwa “Mulungu wa choonadi?” Fotokozani. (Mac. 17:27)

5 Ngakhale kuti ena amanena kuti n’zovuta kudziwa “Mulungu wa choonadi,” zimene amanenazi si zoona. Chilengedwe chimapereka umboni wakuti iye aliko. (Aroma 1:20) Pamene ankalankhula kwa Agiriki ena ophunzira ku Atene, mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu amafuna kuti timupeze komanso kuti, “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Werengani Machitidwe 17:27.) Ndipo zoona zake n’zakuti Yehova amakokera kwa iye anthu odzichepetsa omwe akufunafuna choonadi.—Yoh. 6:44.

6. Kodi ndi mfundo zina ziti za choonadi zomwe zimapezeka m’Baibulo, nanga n’chifukwa chiyani mumayamikira kudziwa mfundo zimenezi?

6 Njira imodzi imene ingatithandize kumudziwa Yehova ndi kuphunzira Baibulo. Anthu omwe analemba bukuli anauziridwa ndi mzimu wa Mulungu. (2 Pet. 1:​20, 21) Choncho zonse zimene zili m’Baibulo ndi zoona ndipo tingazikhulupirire. Mwachitsanzo, tikhoza kukhulupirira zimene limanena zokhudza mmene chilengedwe komanso moyo padzikoli unayambira. (Gen. 1:​1, 26) Tingakhulupirirenso zimene limanena zokhudza chifukwa chake tonsefe timachimwa, kuvutika komanso kumwalira. (Aroma 5:12; 6:23) Tingakhulupirire kwambiri zimene limanena zoti Yehova, pogwiritsa ntchito Mwana wake, adzakonza zinthu zonse zimene Satana yemwe ndi “tate wake wa bodza” anawononga. (Yoh. 8:44; Aroma 16:20) Ndipo sitikayikira zimene Baibulo limalonjeza kuti Yesu adzawononga oipa, adzaukitsa akufa, adzakonza dzikoli komanso adzatithandiza kukhala angwiro. (Yoh. 11:​25, 26; 1 Yoh. 3:8) Apatu Yehova anatipatsa mwayi waukulu ndipo watipatsanso mwayi woti tiziphunzitsa ena choonadichi.—Mat. 28:​19, 20.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIMALAKHULA ZOONA?

7-8. N’chiyani chimatilimbikitsa kuti tizilankhula zoona? Perekani chitsanzo. (Maliko 3:​11, 12) (Onaninso zithunzi.)

7 Monga tafotokozera kale, tiyenera kumalankhula zoona ngati tikufuna kukhala m’banja la Yehova. Komabe kuti tizimusangalatsa, tiyenera kuchita zinanso kuwonjezera pa kulankhula zoona. Yehova amachitanso chidwi ndi zimene zimatipangitsa kulankhula zoona. Taganizirani zimene zinachitika Yesu ali padzikoli. (Werengani Maliko 3:​11, 12.) Pamene ankalalikira pafupi ndi nyanja ya Galileya kunabwera anthu ambiri. Pa anthu amenewa panalinso ena ogwidwa ndi ziwanda omwe ankadzigwetsa patsogolo pake n’kumakuwa kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” N’chifukwa chiyani ziwandazo zinkanena zoona zokhudza Yesu? N’kutheka zinkafuna kuti anthu amene ankamvetserawo azikhulupirire kenako ziwachititse kuti asamatumikire Yehova. N’zoona kuti ziwandazo zinalankhula zoona koma zolinga zawo zinali zoipa. Komabe sizinapusitse Yesu ndipo sanasangalale nazo. Moti Yesu anazilamula kuti zisamalalikire zokhudza iye.

8 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yehova amachita chidwi ndi zimene zikutipangitsa kulankhula zoona. N’zofunikanso kwambiri kuti cholinga chathu pophunzitsa anthu choonadi chizikhala choyenera ndipo tiziwachititsa kuti azilemekeza Yehova osati ifeyo.—Mat. 5:16; yerekezerani ndi Machitidwe 14:​12-15.

Zithunzi zosonyeza mlongo akuphunzira Baibulo ndi mayi wachitsikana. 1. Mlongoyo akufotokoza zokhudza iyeyo ndipo Baibulo lake walisiya patebulo. 2. Mlongoyo wanyamula Baibulo lake lomwe ndi lotsegula ndipo akumuonetsa wophunzira wake lemba.

Kodi mukamaphunzitsa ena choonadi mumafuna kuti aziganizira kwambiri za ndani? (Onani ndime 7 ndi 8)


9. Kodi tiyenera kupewa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

9 Taganiziraninso nthawi ina imene tiyenera kupewa kuchititsa ena kuti azititamanda. Tiyerekeze kuti m’bale wina waudindo watiuza nkhani inayake yachinsinsi ndipo ifeyo tauzanso anthu ena nkhaniyo. Kenako anthu amene tawauza aja atazindikira kuti timawauza zoona akhoza kugoma nafe n’kumaona kuti timadziwa zinthu zambiri zachinsinsi. Zimenezi zingachititse kuti azitiona kuti ndife ofunika kwambiri koma si mmene Mulungu angationere. (Miy. 11:13) Chifukwa chiyani? Chifukwa ngakhale kuti tawauza zinthu zachinsinsi komanso zoona, tawauza ndi cholinga cholakwika.

KODI TIZIPHUNZITSA BWANJI CHOONADI?

10. Kodi kulankhula ‘mokoma mtima’ kumatanthauza chiyani? (Akolose 4:6)

10 Werengani Akolose 4:6. Mtumwi Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Kolose kuti nthawi zonse mawu awo azisonyeza kuti ndi okoma mtima. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Mawu a Chigiriki omwe anawagwiritsa ntchito pa lembali amatanthauza kuti zolankhula zathu ziyenera kukhala zothandiza ena, zosonyeza kuti ndife okoma mtima komanso zimene angasangalale nazo.

11-12. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala tikamaphunzitsa choonadi? Perekani chitsanzo. (Onaninso zithunzi.)

11 Tiyenera kutsatira malangizo a Paulo akuti zolankhula zathu zizisonyeza kuti ndife okoma mtima pamene tikuphunzitsa choonadi. Baibulo limayerekezera mfundo zake za choonadi ndi lupanga lakuthwa lomwe lingathe kulekanitsa moyo ndi mzimu. M’mawu ena, zingathandize ifeyo komanso anthu ena kuzindikira maganizo amumtima mwathu komanso zolinga zathu. (Aheb. 4:12) Koma ngati sitingagwiritse ntchito Baibulo mwaluso tikhoza kukhumudwitsa ena komanso kukangana ndi anthu. Kodi zimenezi zingachitike bwanji?

12 Tiyerekeze kuti pamene tikulalikira takumana ndi munthu wina wamtima wabwino yemwe amalambira zifaniziro komanso amakondwerera Khirisimasi ndi Isitala limodzi ndi banja lake. Pogwiritsa ntchito Baibulo mwina tingamusonyeze kuti n’kupusa kulambira zifaniziro zopanda moyo komanso kuti Khirisimasi ndi Isitala ndi zikondwerero zachikunja. (Yes. 44:​14-20; 2 Akor. 6:​14-17) Ngati tingachite zimenezi pa ulendo woyamba, tikhoza kukhala kuti tikulankhula zoona koma sitingakhale kuti tikugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mwaluso.

Zithunzi zosonyeza banja likulalikira bambo wina amene ali pakhonde la nyumba yake pamene banja lake likukongoletsa m’nyumba ndi maluwa a Khirisimasi. 1. Banjalo likuonetsa bamboyo nkhani yakuti “Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Khirisimasi?” imene ili pa webusaiti ya jw.org. Bamboyo wapinda manja ake ndipo akumvetsera koma sakusangalala. 2. Banjalo likuonetsa bamboyo nkhani yakuti “Zimene Mungachite Kuti Mukhale Bambo Wabwino” imene ili pa webusaiti ya jw.org. Bamboyo akumvetsera uku akumwetulira.

Kodi mungatani kuti muziphunzitsa choonadi mwaluso? (Onani ndime 11 ndi 12)a


13. Kodi tingatani kuti mawu athu akhale okoma ngati kuti tawathira mchere?

13 Paulo ananenanso kuti mawu athu ayenera kukhala okoma ngati kuti tawathira mchere. Iye sankatanthauza kuti tizikhotetsa mfundo za choonadi kapena kuzibisa. M’malomwake anatilimbikitsa kuti tizigwiritsa ntchito mawu okhala ngati ‘tawathira mchere’ kuti tiziphunzitsa anthu choonadi m’njira yakuti ‘azimva kukoma.’ (Yobu 12:11) Koma nthawi zina kuchita zimenezi kungakhale kovuta. Pa nkhani ya chakudya chenicheni, mwina tingaganize kuti chakudya chomwe chatikomera ifeyo, chingakomerenso anthu ena. Mofanana ndi zimenezi, tingaganize kuti aliyense akhoza kusangalala ndi mmene tikulankhulira, koma zimenezi si zoona. Mwachitsanzo, anthu a m’zikhalidwe zina amakonda kulankhula mwachindunji maganizo awo ngakhale pamene akulankhula ndi anthu akuluakulu. Pamene anthu a m’zikhalidwe zina akhoza kuona kuti njira imeneyi si yabwino komanso n’kupanda ulemu. Paulo ananena kuti tiyenera kudziwa ‘mmene tingayankhire munthu aliyense.’ Zimenezi zikusonyeza kuti zolankhula zathu siziyenera kukhala zongokomera ifeyo kapena zogwirizana ndi chikhalidwe chathu, koma zizikhala zosangalatsa kwa amene akutimvetsera.

KODI TIZIPHUNZITSA CHOONADI PA NTHAWI ITI?

14. Kodi Yesu ali padzikoli anaphunzitsa ophunzira ake zonse zomwe ankadziwa? Fotokozani.

14 Yesu ankalankhula ndi otsatira ake mokoma mtima ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri. (Maliko 6:34) Koma panalinso zina zoti aphunzire. Yesu sanawaphunzitse zonse zimene iyeyo ankadziwa. Iye ankadziwa zinthu zimene ophunzirawo akanakwanitsa kuzimvetsa. Ankadziwanso kuti sinali nthawi yabwino yoti aphunzire mfundo zina za choonadi. Ndipotu ananena kuti pa nthawiyo ophunzirawo sakanamvetsa mfundozo. (Yoh. 16:12) Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?

15. Kodi anthu omwe tikuphunzira nawo Baibulo tiyenera kuwafotokozera zonse zomwe tikudziwa pa nthawi imodzi? Fotokozani. (Miyambo 25:11) (Onaninso chithunzi.)

15 Chitsanzo cha Yesu chikusonyeza kuti kudziwa mfundo za choonadi sikutanthauza kuti tiyenera kuphunzitsa anthu zonse zomwe tikudziwa pa nthawi imodzi. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu? Tiyenera kuganizira mmene zinthu zilili pa moyo wa anthu omwe tikuwaphunzitsa. Taganiziraninso za munthu uja amene amakondwerera Khirisimasi ndi Isitala limodzi ndi banja lake. Timadziwa kuti zikondwerero zimenezi zinayamba ndi zipembedzo zabodza ndipo Mulungu sasangalala nazo. Ndiye tiyerekeze kuti mwayamba kuphunzira Baibulo ndi munthu kutatsala mlungu umodzi kapena iwiri kuti Khirisimasi ichitike. Kodi tingasonyeze kuti ndife okoma mtima ngati titamuuza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya zikondwerero zachikunja, n’kumayembekezera kuti asiya kukondwerera Khirisimasi nthawi yomweyo? N’zoona kuti ophunzira ena sachedwa kuyamba kugwiritsa ntchito zonse zomwe aphunzira m’Baibulo. Komabe ena zimawatengera nthawi kuti asinthe mmene amaganizira komanso mmene amachitira zinthu. Tingathandize ophunzira Baibulo athu kupita patsogolo ngati titawauza zomwe akufunika kudziwa pa nthawi yoyenera, kapena kuti pa nthawi imene angazimvetse.—Werengani Miyambo 25:11.

Banja limene lili pa chithunzi choyamba lija likuphunzira kabuku kakuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale” ndi bambo uja kunyumba kwake. Maluwa a Khirisimasi ali pambali pawo.

Muzitsanzira Yesu posankha nthawi yabwino yophunzitsa choonadi komanso kuchuluka kwa zimene mungaphunzitse (Onani ndime 15)


16. Kodi tingathandize bwanji amene tikuwaphunzitsa Baibulo kuti ‘apitirize kuyenda m’choonadi?’

16 Chimodzi mwa zinthu zomwe zimatithandiza kukhala osangalala kwambiri ndi kuthandiza anthu kuti aphunzire mfundo zoona zokhudza Yehova. Tingawathandize kuti ‘apitirize kuyenda m’choonadi’ pochita zotsatirazi: Tizipitiriza kuwasonyeza chitsanzo chabwino. (3 Yoh. 3, 4) Tizionetsetsa kuti zimene timachita pa moyo wathu zikusonyeza kuti timakhulupirira malonjezo opezeka m’Mawu a Mulungu, timalankhula zoona tili ndi zolinga zabwino komanso timalankhula mokoma mtima pa nthawi yoyenera tikamaphunzitsa choonadi. Ndiponso tizichititsa kuti anthu azitamanda Yehova osati ifeyo. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timatumikira Yehova, Mulungu wa choonadi.

KODI MWAPHUNZIRA CHIYANI PA MALEMBA OTSATIRAWA?

  • Machitidwe 17:27

  • Akolose 4:6

  • Miyambo 25:11

NYIMBO NA. 160 “Uthenga Wabwino”

a MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pachithunzi choyambirira, m’bale waona maluwa a Khirisimasi m’nyumba ya munthu yemwe akumulalikira ndipo akumuonetsa nkhani yofotokoza kuti Khirisimasi ndi chikondwerero chachikunja. Pachithunzi chachiwiri, m’bale akusonyeza mwininyumba nkhani yomwe ili ndi mfundo zothandiza abambo. Kodi ndi njira iti yomwe ili yabwino panjira ziwirizi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena