Kodi a Mboni za Yehova Amachita Bwanji Zinthu ndi Anthu Amene Anachoka M’chipembedzo Chawo?
Timayesetsa kusonyeza wina aliyense chikondi, kukomera mtima komanso ulemu. Ngati wa Mboni za Yehova wafooka kapena wasiya kuchita zinthu zokhudzana ndi kulambira, timayesetsa kulankhula naye n’kumutsimikizira kuti timamukonda. Komanso timamuthandiza kuti ayambirenso kukonda Mulungu.—Luka 15:4-7.
Nthawi zina, zochita za munthu zingapangitse kuti achotsedwe mumpingo. (1 Akorinto 5:13) Koma popeza abale ndi alongo athu timawakonda kwambiri, timayesetsa kuthandiza munthu amene wachita tchimo n’cholinga choti zisafike poti achotsedwe. Koma ngakhale atachotsedwa, timamusonyezabe chikondi ndi ulemu mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena.—Maliko 12:31; 1 Petulo 2:17.
N’chifukwa chiyani munthu amachotsedwa mumpingo?
Baibulo limanena momveka bwino kuti Mkhristu akachita tchimo lalikulu ndipo sakufuna kusintha, akuyenera kuchotsedwa mumpingo. (1 Akorinto 5:11-13) Baibulo limatiuza momveka bwino machimo akuluakulu amene angachititse kuti munthu achotsedwe mumpingo. Mwachitsanzo, limatchula zinthu monga chigololo, kumwa mowa mwauchidakwa, kupha munthu, kuchitira ena nkhanza m’banja komanso kuba.—1 Akorinto 6:9, 10; Agalatiya 5:19-21; 1 Timoteyo 1:9, 10.
Komabe, munthu akachita tchimo lalikulu sikuti timangofikira kumuchotsa mumpingo ayi. Choyamba, akulu mumpingoa amayesetsa kumuthandiza kuti asinthe khalidwe lake. (Aroma 2:4) Iwo amayesetsa kukambirana naye ndipo amachita zimenezi modekha, moleza mtima komanso mokoma mtima. (Agalatiya 6:1) Kukambirana naye mwanjira imeneyi kungamuthandize kuzindikira kuti analakwitsa ndipo angakhale wofunitsitsa kulapa. (2 Timoteyo 2:24-26) Koma ngati akupitiriza kuchita zinthu zimene Baibulo limanena kuti ndi zoipa ndipo sakulapa, ngakhale kuti akulu ayesetsa kumuthandiza mobwerezabwereza, akuyenera kuchotsedwa mumpingo. Zikatero, akulu amalengeza kumpingo kuti munthuyo salinso wa Mboni za Yehova.
Kodi kuchotsa munthu amene sakufuna kusiya kuchita machimo kuli ndi ubwino wotani? Ubwino woyamba ndi wakuti mpingo umaonetsetsa kuti ukutsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino zimene zimathandiza kuti mpingowo ukhale woyera. Komanso mpingo umatetezeka chifukwa sutengera makhalidwe oipa a munthu wochimwayo. (1 Akorinto 5:6; 15:33; 1 Petulo 1:16) Kuwonjezera pamenepo, zimathandizanso amene wachotsedwayo kuti asiye kuchita machimo n’kusintha.—Aheberi 12:11.
Kodi a Mboni za Yehova amachita bwanji zinthu ndi anthu amene achotsedwa mumpingo?
Baibulo limanena kuti Akhristu akuyenera ‘kusiya kugwirizana ndi aliyense’ amene wachotsedwa mumpingo, “ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi.” (1 Akorinto 5:11) Choncho siticheza ndi munthu amene wachotsedwa mumpingo. Koma sikuti timamupewa pa chilichonse. Timamusonyeza ulemu. Timamulandira ndi manja awiri akabwera kumisonkhano yathu, ndipo kumeneko wa Mboni za Yehova aliyense angathe kumupatsa moni.b Munthuyo angathenso kupempha akulu kuti amuthandize mwauzimu kuti abwezeretsedwe mumpingo.
Kodi chimachitika n’chiyani ngati mwamunac wachotsedwa mumpingo koma mkazi wake komanso ana ake aang’ono adakali a Mboni za Yehova? Chibale cha anthuwo sichitha, koma anthu a Mboniwo amangosintha mmene amachitira zinthu ndi bambowo zokhudzana ndi kulambira. Popeza kuti akukhala limodzi, mkazi ndi anawo amapitiriza kuchitira limodzi ndi bambowo zinthu zatsiku ndi tsiku zokhudza moyo wawo wa banja ndipo akuyenera kumakondana.
Munthu amene anachotsedwa mumpingo angathe kupempha akulu kuti akacheze naye ndipo akuluwo angathe kukambirana naye mfundo za m’Malemba komanso kumulimbikitsa mokoma mtima kuti alape n’kubwerera kwa Mulungu. (Zekariya 1:3) Ngati atasiya makhalidwe oipawo ndipo akusonyeza kuti akufunitsitsa kuyambiranso kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wake, amaloledwa kubwereranso mumpingo ndipo amalandiridwa ndi manja awiri. Mpingo ‘umamukhululukira ndi mtima wonse ndiponso kumutonthoza’ ngati mmene Akhristu a ku Korinto anachitira, munthu wochimwa atasiya kuchita machimo.—2 Akorinto 2:6-8.
Kodi anthu amene anachotsedwapo m’mbuyomu panopa akumva bwanji?
Tamvani zimene ananena a Mboni za Yehova ena omwe anachotsedwapo mumpingo koma kenako anaganiza zobwerera kwa Mulungu.
“Nditasankha zoti ndibwerere mumpingo, ndinkaganiza kuti akulu akandiuza kuti ndifotokoze zonse zimene ndinkachita pa zaka zonse zimene ndinali wochotsedwa. Koma sanachite zimenezo, m’malomwake anangondiuza kuti, ‘Tikufuna kuti uziganizira kwambiri zimene ukuyenera kuchita panopa kupita m’tsogolo.’ Atandiuza zimenezi mtima wanga unakhala m’malo.”—Maria, United States.
“Abale ndi alongo anasangalala kwambiri nditabwezeretsedwa. Ndinaona kuti ankandiona kuti ndine wofunika kwambiri. Abale ndi alongo anga mumpingo anandithandiza kuti ndiziona kuti Yehova anandikhululukira ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndiziganizira zakutsogolo osati zimene zinachitika kumbuyo. Akulu ankandithandiza nthawi zonse kuti ndikhalenso pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Ankanditonthoza komanso kundithandiza kuti ndiziona kuti Yehova amandionabe kuti ndine wofunika ndiponso amandikonda.”—Malcom, Sierra Leone.
“Ndikusangalala kuti Yehova amakonda anthu ake moti amaonetsetsa kuti gulu lake ndi loyera. Ngakhale kuti anthu ena akhoza kumaganiza kuti kuchotsa munthu mumpingo ndi nkhanza, koma ndi zoyenera komanso ndi njira yomusonyezera chikondi. Ndikuyamikira kwambiri Atate wathu wakumwamba chifukwa ndi Mulungu wachikondi komanso wokhululuka.”—Sandi, United States.
a Ngakhale kuti m’chitsanzochi tikunena za mwamuna, mfundo zake zikugwiranso ntchito kwa mkazi. Amene anachotsedwa mumpingo timawalandira ndi manja awiri akabwera kumisonkhano yathu.
b Akulu ndi amuna okhulupirika komanso odziwa zambiri amene amaphunzitsa mfundo za m’Malemba komanso kuweta anthu a Yehova powathandiza ndiponso kuwalimbikitsa. Akuluwa akamagwira ntchito imeneyi salandira malipiro aliwonse.—1 Petulo 5:1-3.
c Zikafika poipa kwambiri, munthu angathe kuchoka mumpingo komanso kumachita zinthu zomwe zingasokoneze mpingowo ndi kufooketsa Akhristu, kapena angamalimbikitse ena kuti azichita zinthu zoipa. Zimenezi zikachitika, timatsatira lamulo la m’Baibulo lakuti tipewe “kumupatsa moni” munthu wotereyu.—2 Yohane 9-11.