26 Selomoti ameneyu pamodzi ndi abale ake ankayangʼanira zinthu zonse zimene anaziyeretsa kuti zikhale zopatulika.+ Amene anaziyeretsa anali Mfumu Davide,+ atsogoleri a nyumba za makolo,+ atsogoleri a magulu a anthu 1,000, a magulu a anthu 100 ndi atsogoleri a asilikali.