4 Ndidzachita zimenezi chifukwa iwo andisiya+ ndiponso achititsa kuti malo ano ndisawazindikire.+ Pamalo ano iwo akupereka nsembe kwa milungu ina, imene iwowo, makolo awo komanso mafumu a Yuda sankaidziwa ndipo adzaza malo ano ndi magazi a anthu osalakwa.+