29 Edomu+ ali kumeneko. Kulinso mafumu ake ndi atsogoleri ake onse amene ngakhale kuti anali amphamvu, anaikidwa mʼmanda limodzi ndi anthu amene anaphedwa ndi lupanga. Anthu amenewanso adzagona limodzi ndi anthu osadulidwa+ komanso anthu amene akutsikira kudzenje.