5 Inu anthu anga, chonde kumbukirani zimene Balaki mfumu ya Mowabu ankafuna kuchita.+
Ndiponso zimene Balamu mwana wa Beori anamuyankha.+
Kumbukirani zimene zinachitika kuyambira ku Sitimu+ kukafika ku Giligala.+
Kumbukirani zimenezi kuti mudziwe ntchito zolungama za Yehova.”