88 Nyama zonse zoperekedwa za nsembe yachiyanjano+ zinalipo ng’ombe 24 zamphongo, nkhosa 60 zamphongo, mbuzi 60 zamphongo, ndi ana a nkhosa 60 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinaperekedwa pamwambo+ wotsegulira guwa lansembe, pambuyo poti ladzozedwa.+