2 Yehova anati:
“Taonani! Madzi akubwera+ kuchokera kumpoto+ ndipo madzi ake ndi achigumula. Adzamiza dziko ndi zonse zokhala mmenemo.+ Adzamizanso mzinda ndi zonse zokhala mmenemo. Amuna adzalira mokuwa, ndipo aliyense wokhala m’dzikolo adzalira mofuula.+