24 Ndinamva phokoso la mapiko awo, lokhala ngati phokoso la madzi ambiri,+ ndiponso ngati phokoso la Wamphamvuyonse. Zikamayenda, zinali kuchita phokoso ngati la chipwirikiti cha anthu,+ ngati phokoso la pamsasa.+ Zikaima chilili, zinali kutsitsa mapiko awo.