8 Zamoyo zinayizo,+ chilichonse chinali ndi mapiko 6.+ Zinali ndi maso thupi lonse ngakhalenso kunsi kwa mapiko.+ Zamoyo zimenezi sizinali kupuma usana ndi usiku. Zinali kunena kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova+ Mulungu, Wamphamvuyonse,+ amene analipo, amene alipo,+ ndi amene akubwera.”