Loweruka, July 19
Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni.—Aheb. 11:32.
Gidiyoni anayankha modekha pamene amuna a ku Efuraimu ankamuimba mlandu. (Ower. 8:1-3) Iye sanayankhe mokwiya. Iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa powamvetsera komanso kulankhula nawo mokoma mtima, zomwe zinachititsa kuti mitima ya anthuwo ikhale m’malo. Akulu anzeru amatsanzira Gidiyoni pomvetsera mosamala komanso kuyankha modekha akamaimbidwa mlandu. (Yak. 3:13) Akamachita zimenezi amathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere. Pamene anthu anayamba kutamanda Gidiyoni chifukwa chopambana pankhondo yolimbana ndi Amidiyani, iye anathandiza anthuwo kuti apereke ulemerero kwa Yehova. (Ower. 8:22, 23) Kodi abale audindo angatsanzire bwanji Gidiyoni? Iwo ayenera kupereka ulemerero kwa Yehova chifukwa cha zimene akwanitsa kuchita. (1 Akor. 4:6, 7) Mwachitsanzo, ngati mkulu akutamandidwa chifukwa cha luso lophunzitsa lomwe ali nalo, iye angathandize anthuwo kuti aziganizira kumene kukuchokera mfundo zomwe amaphunzitsazo, komwe ndi m’Mawu a Mulungu, kapena maphunziro omwe gulu la Yehova limapereka. Nthawi ndi nthawi, akulu ayenera kumadzifufuza kuti aone ngati akuchititsa anthu kuti azitamanda iwowo m’malo mwa Yehova. w23.06 4 ¶7-8
Lamlungu, July 20
Maganizo anga ndi osiyana ndi maganizo anu.—Yes. 55:8.
Ngati zimene tapempha sizikuchitika tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndikupemphazi ndi zoyenera?’ Nthawi zambiri anthu timaganiza kuti timadziwa zomwe ndi zoyenera kwa ifeyo. Koma zomwe timapempha zikhoza kukhala zosathandiza kwenikweni. Tikamapempherera vuto linalake, pakhoza kukhala njira ina yabwino yothetsera vutolo kusiyana ndi imene tikupempha. Ndipo zinthu zina zomwe tingapemphe zingakhale zosagwirizana ndi zimene Yehova amafuna. (1 Yoh. 5:14) Mwachitsanzo, taganizirani za makolo omwe anapempha Yehova kuti mwana wawo apitirizebe kukhala m’choonadi. Zimene anapemphazi zikhoza kuoneka ngati zoyenera. Koma Yehova sakakamiza munthu aliyense kuti azimutumikira. Amafuna kuti aliyense azisankha kumutumikira, ngakhalenso ana. (Deut. 10:12, 13; 30:19, 20) M’malomwake makolowo angapemphe Yehova kuti awathandize kuti azimufika pamtima mwanayo n’cholinga choti azikonda Yehova komanso kukhala naye pa ubwenzi.—Miy. 22:6; Aef. 6:4. w23.11 21 ¶5; 23 ¶12
Lolemba, July 21
Pitirizani kulimbikitsana.—1 Ates. 4:18.
N’chifukwa chiyani kutonthoza ena kumasonyeza kuti tili ndi chikondi? Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo linanena kuti mawu akuti “kutonthoza” omwe Paulo anagwiritsa ntchito amatanthauza “kuima pafupi ndi munthu kuti timulimbikitse pamene wakumana ndi vuto lalikulu.” Choncho tikatonthoza m’Khristu mnzathu yemwe wakumana ndi vuto, timamuthandiza kuti aimirire n’kupitiriza kuyenda panjira yokalandira moyo. Nthawi iliyonse yomwe tatonthoza m’bale kapena mlongo, timasonyeza kuti timakonda Akhristu anzathu. (2 Akor. 7:6, 7, 13) Kutonthoza ena n’kogwirizananso ndi chifundo. N’chifukwa chiyani tikutero? Mtima wachifundo ndi umene umalimbikitsa munthu kuti atonthoze ena komanso kuwathandiza. Choncho timayamba ndi kukhala ndi chifundo, kenako timatonthoza ena. Paulo anagwirizanitsa chifundo cha Yehova ndi zimene amachita potonthoza ena. Iye ananena kuti Yehova ndi “Bambo wachifundo chachikulu ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse.”—2 Akor. 1:3. w23.11 9-10 ¶8-10