Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lachisanu, July 18

[Anatipanga] kukhala mafumu ndi ansembe kuti titumikire Mulungu wake ndi Atate wake.​—Chiv. 1:6.

Pali ophunzira ochepa a Khristu adzozedwa ndi mzimu woyera, okwana 144,000 omwe ali pa ubwenzi wapadera ndi Yehova. Anthu amenewa adzatumikira ngati ansembe kumwamba limodzi ndi Yesu. (Chiv. 1:6; 14:1) Malo Oyera a chihema amaimira kuti iwowa atengedwa kukhala ana auzimu a Mulungu pa nthawi imene ali padziko lapansi. (Aroma 8:15-17) Malo Oyera Koposa amaimira kumwamba, komwe Yehova amakhala. “Nsalu,” imene inkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa imaimira thupi la Yesu limene linali ngati chotchinga chomulepheretsa kupita kumwamba kukatumikira ngati Mkulu wa Ansembe wapamwamba m’kachisi wauzimu. Yesu atapereka thupi lake ngati nsembe yopulumitsira anthu, anatsegula njira yoti Akhristu onse odzozedwa akakhale ndi moyo kumwamba. Iwonso amafunika kusiya thupi lomwe ali nalo padzikoli kuti akalandire mphoto yawo kumwamba.—Aheb. 10:19, 20; 1 Akor. 15:50. w23.10 28 ¶13

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Loweruka, July 19

Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni.—Aheb. 11:32.

Gidiyoni anayankha modekha pamene amuna a ku Efuraimu ankamuimba mlandu. (Ower. 8:1-3) Iye sanayankhe mokwiya. Iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa powamvetsera komanso kulankhula nawo mokoma mtima, zomwe zinachititsa kuti mitima ya anthuwo ikhale m’malo. Akulu anzeru amatsanzira Gidiyoni pomvetsera mosamala komanso kuyankha modekha akamaimbidwa mlandu. (Yak. 3:13) Akamachita zimenezi amathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere. Pamene anthu anayamba kutamanda Gidiyoni chifukwa chopambana pankhondo yolimbana ndi Amidiyani, iye anathandiza anthuwo kuti apereke ulemerero kwa Yehova. (Ower. 8:22, 23) Kodi abale audindo angatsanzire bwanji Gidiyoni? Iwo ayenera kupereka ulemerero kwa Yehova chifukwa cha zimene akwanitsa kuchita. (1 Akor. 4:6, 7) Mwachitsanzo, ngati mkulu akutamandidwa chifukwa cha luso lophunzitsa lomwe ali nalo, iye angathandize anthuwo kuti aziganizira kumene kukuchokera mfundo zomwe amaphunzitsazo, komwe ndi m’Mawu a Mulungu, kapena maphunziro omwe gulu la Yehova limapereka. Nthawi ndi nthawi, akulu ayenera kumadzifufuza kuti aone ngati akuchititsa anthu kuti azitamanda iwowo m’malo mwa Yehova. w23.06 4 ¶7-8

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lamlungu, July 20

Maganizo anga ndi osiyana ndi maganizo anu.​—Yes. 55:8.

Ngati zimene tapempha sizikuchitika tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndikupemphazi ndi zoyenera?’ Nthawi zambiri anthu timaganiza kuti timadziwa zomwe ndi zoyenera kwa ifeyo. Koma zomwe timapempha zikhoza kukhala zosathandiza kwenikweni. Tikamapempherera vuto linalake, pakhoza kukhala njira ina yabwino yothetsera vutolo kusiyana ndi imene tikupempha. Ndipo zinthu zina zomwe tingapemphe zingakhale zosagwirizana ndi zimene Yehova amafuna. (1 Yoh. 5:14) Mwachitsanzo, taganizirani za makolo omwe anapempha Yehova kuti mwana wawo apitirizebe kukhala m’choonadi. Zimene anapemphazi zikhoza kuoneka ngati zoyenera. Koma Yehova sakakamiza munthu aliyense kuti azimutumikira. Amafuna kuti aliyense azisankha kumutumikira, ngakhalenso ana. (Deut. 10:12, 13; 30:19, 20) M’malomwake makolowo angapemphe Yehova kuti awathandize kuti azimufika pamtima mwanayo n’cholinga choti azikonda Yehova komanso kukhala naye pa ubwenzi.—Miy. 22:6; Aef. 6:4. w23.11 21 ¶5; 23 ¶12

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena