July
Lachiwiri, July 1
Anayenda mʼdziko lonse nʼkumachita zabwino ndiponso kuchiritsa anthu.—Mac. 10:38.
Zonse zimene Yesu ananena, kuchita komanso zozizwitsa zake, zinasonyeza bwino mmene Atate wake amaganizira komanso mmene amamvera. (Yoh. 14:9) Kodi tingaphunzire chiyani pa zozizwitsa za Yesu? Yesu ndi Atate wake amatikonda kwambiri. Ali padzikoli, Yesu anasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu pogwiritsa ntchito mphamvu zake zodabwitsa pothandiza omwe ankavutika. Pa nthawi ina anthu awiri osaona anamufuulira kuti awathandize. (Mat. 20:30-34) Onani kuti Yesu “atagwidwa ndi chifundo,” anawachiritsa. Monga mmene agwiritsidwira ntchito palembali, mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “atagwidwa ndi chifundo,” amanena za chifundo chachikulu chomwe munthu amamva kuchokera pansi pa mtima. Chifundo chimenechi, chomwe chimasonyeza chikondi, ndi chimene chinachititsa Yesu kuti adyetse anjala komanso achiritse wakhate. (Mat. 15:32; Maliko 1:41) Sitikayikira kuti Yehova, yemwe ndi Mulungu “wachifundo chachikulu,” komanso Mwana wake amatikonda kwambiri ndipo amakhudzidwa tikamavutika. (Luka 1:78; 1 Pet. 5:7) Iwo ndi ofunitsitsa kudzachotsa mavuto onse omwe anthu amakumana nawo. w23.04 3 ¶4-5
Lachitatu, July 2
Inu amene mumakonda Yehova, muzidana ndi zoipa. Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika. Amawapulumutsa m’manja mwa oipa.—Sal. 97:10.
Tingachite zinthu zina zomwe zingatithandize kupewa maganizo ndi mfundo zoipa zomwe ndi zofala m’dziko la Satanali. Kuwerenga komanso kuphunzira Baibulo kungatithandize kuti tiziganizira zinthu zabwino. Kupezeka pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito yolalikira kungatetezenso maganizo athu. Tikatero, Yehova amatilonjeza kuti sadzalola kuti tiyesedwe kufika pamene sitingathe kupirira. (1 Akor. 10:12, 13) Tonsefe tiyenera kumapemphera kwambiri kuposa kale kuti tikhalebe okhulupirika m’masiku otsiriza ovutawa. Yehova amafuna kuti ‘tizimukhuthulira zonse zamumtima mwathu.’ (Sal. 62:8) Muzitamanda Yehova ndipo muzimuyamikira chifukwa cha zonse zimene amachita. Muzimupempha kuti azikuthandizani kukhala wolimba mtima polalikira. Muzimuchonderera kuti akuthandizeni kulimbana ndi mavuto komanso mayesero alionse omwe mukukumana nawo. Musamalole kuti chilichonse kapena aliyense akulepheretseni kupemphera kwa Yehova nthawi zonse. w23.05 7 ¶17-18
Lachinayi, July 3
Tiyeni tiganizirane . . . , tilimbikitsane.—Aheb. 10:24, 25.
N’chifukwa chiyani timapita kumisonkhano ya mpingo? Chifukwa chachikulu ndi kutamanda Yehova. (Sal. 26:12; 111:1) Timapitanso kumisonkhano n’cholinga choti tizilimbikitsana munthawi yovutayi. (1 Ates. 5:11) Tikakweza dzanja lathu n’kuyankha, timakwaniritsa zolinga ziwiri zimenezi. Koma pa nkhani yopereka ndemanga, tingakumane ndi mavuto ena. Tingamachite mantha kuyankha, kapena tingamafunitsitse kuyankha koma mwina sitingapatsidwe mwayi woyankha monga mmene timafunira. Ndiye kodi tingatani pa mavuto amenewa? Timapeza yankho m’kalata imene mtumwi Paulo analembera Aheberi. Pofotokoza kufunika kosonkhana, iye ananena kuti tiziganizira kwambiri ‘zolimbikitsana.’ Tikazindikira kuti ena angalimbikitsidwe ngakhale ndi yankho lachidule losonyeza chikhulupiriro chathu, sitingachite mantha kuyankha. Ndipo ngakhale kuti sitingapatsidwe mwayi woyankha pafupipafupi, tingakhale osangalala kuti enanso mumpingo akhala ndi mwayi wopereka ndemanga.—1 Pet. 3:8. w23.04 20 ¶1-3
Lachisanu, July 4
[Pitani] ku Yerusalemu . . . n’kukamanganso nyumba ya Yehova.—Ezara 1:3.
Panaperekedwa chilengezo choti Ayuda omwe anali akapolo kwa zaka 70 ku Babulo, akanatha kubwerera kwawo ku Isiraeli. (Ezara 1:2-4) Yehova yekha ndi amene akanachititsa kuti zimenezi zitheke. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Ababulo sankamasula akapolo. (Yes. 14:4, 17) Koma mzinda wa Babulo unali utagonjetsedwa ndipo mfumu yatsopano inauza Ayuda kuti akhoza kuchoka m’dzikolo. Myuda aliyense, makamaka mitu ya mabanja, ankafunika kusankha zochita kuti achoke ku Babulo kapena ayi. Komatu kusankha zochita pa nkhaniyi sikunali kophweka. Ayuda ena anali achikulire kwambiri moti zikanakhala zovuta kuyenda ulendo wovutawu. Komanso Ayuda ambiri anabadwira ku Babulo komweko ndipo anali asanakhalepo kwina kulikonse. Choncho kwa iwowa, ku Isiraeli kunali kwawo kwa makolo awo. Ayuda enanso zinthu zinkawayendera bwino ku Babulo, choncho zikanakhala zovuta kusiya nyumba zawo zabwino komanso mabizinesi awo n’kumakakhala m’dziko lachilendo. w23.05 14 ¶1-2
Loweruka, July 5
Khalani okonzeka.—Mat. 24:44.
Baibulo limatilimbikitsa kuti tipitirize kukhala opirira, achifundo komanso achikondi. Pa Luka 21:19 pamati: “Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.” Pa Akolose 3:12 pamati: “Valani chifundo.” Ndipo pa 1 Atesalonika 4:9, 10 pamati: “Mulungu amakuphunzitsani kuti muzikondana. . . . Koma tikukulimbikitsani abale kuti mupitirize kuchita zimenezi kuposa mmene mukuchitira.” Mavesi onsewa analembera ophunzira omwe anali atasonyeza kale kuti anali opirira, achifundo komanso achikondi. Komabe, iwo ankafunika kupitiriza kusonyeza makhalidwewa. Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. Kuti tithe kuchita zimenezi, tiziganizira mmene Akhristu oyambirira anasonyezera makhalidwewa. Kenako tiziona mmene tingawatsanzirire, zomwe zingasonyeze kuti takonzekera chisautso chachikulu. Chisautso chachikulucho chikamadzayamba, tidzakhala titaphunzira kukhala opirira ndiponso titatsimikiza mtima kuti tizipirirabe. w23.07 3 ¶4, 8
Lamlungu, July 6
Kumeneko kudzakhala msewu waukulu, . . . Msewu Wopatulika.—Yes. 35:8.
Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” tiyenera kupitiriza kuyenda pa “Msewu Wopatulika” chifukwa umatithandiza kukhalabe m’Paradaiso wauzimu komanso udzatithandiza kupeza madalitso amene Ufumu udzabweretse m’tsogolo. (Yoh. 10:16) Kungoyambira mu 1919 C.E., amuna, akazi komanso ana mamiliyoni akhala akutuluka mu Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga, ndipo ayamba kuyenda pamsewu wophiphiritsawu. Ayuda atachoka ku Babulo, Yehova anaonetsetsa kuti wawachotsera zopinga zonse pa njira yawo. (Yes. 57:14) Nanga bwanji za “Msewu Wopatulika” wa masiku ano? Kwa zaka zambiri chisanafike chaka cha 1919, Yehova anagwiritsa ntchito amuna omwe ankamulemekeza kuti akonze njira yotulukira mu Babulo Wamkulu. (Yerekezerani ndi Yesaya 40:3.) Iwo anagwira ntchito yofunika yokonza msewu wauzimu ndipo zimenezi zinathandiza kuti anthu a maganizo abwino atuluke mu Babulo Wamkulu n’kulowa m’paradaiso wauzimu, momwe kulambira koona kunali kutabwezeretsedwa. w23.05 15-16 ¶8-9
Lolemba, July 7
Tumikirani Yehova mokondwera. Bwerani kwa iye mukufuula mosangalala.—Sal. 100:2.
Yehova amafuna kuti tizimutumikira mosangalala komanso mofunitsitsa. (2 Akor. 9:7) Ndiye kodi tiyenera kuyesetsa kupitiriza kukwaniritsa cholinga chinachake chauzimu ngakhale pamene tilibe mtima wofunitsitsa kutero? Taganizirani chitsanzo cha mtumwi Paulo. Iye anati: “Ndikumenya thupi langa n’kulichititsa kukhala ngati kapolo.” (1 Akor. 9:25-27) Paulo ankadzikakamiza kuchita zoyenera ngakhale pamene ankaona kuti sakufuna kuchita zimenezo. Kodi Yehova ankasangalala ndi zimene Paulo ankachita pomutumikira? Inde. Ndipotu iye anamudalitsa chifukwa cha khama lake. (2 Tim. 4:7, 8) Mofanana ndi zimenezi, Yehova amasangalala akationa tikuyesetsa kukwaniritsa cholinga chathu ngakhale pamene tilibe mtima wofunitsitsa kutero. Iye amasangalala chifukwa amadziwa kuti ngakhale kuti si nthawi zonse pamene timachita zinthuzo chifukwa chakuti zimatisangalatsa, timazichita chifukwa chakuti timamukonda iyeyo. Monga mmene Yehova anadalitsira Paulo ifenso adzatidalitsa chifukwa cha khama lathu. (Sal. 126:5) Ndipo tikamaona mmene Yehova akutidalitsira tingayambe kukhala ndi mtima wofunitsitsa. w23.05 29 ¶9-10
Lachiwiri, July 8
Tsiku la Yehova lidzabwera.—1 Ates. 5:2.
Mtumwi Paulo anayerekezera amene sadzapulumuka pa tsiku la Yehova ndi anthu amene akugona. Iwo sakudziwa zimene zikuchitika kapenanso kuti nthawi ikudutsa. Choncho, sangazindikire zinthu zofunika zomwe zikuchitika kapenanso kuchitapo kanthu. Masiku ano, anthu ambiri akugona mwauzimu. (Aroma 11:8) Iwo sakhulupirira umboni woti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ komanso kuti chisautso chachikulu chiyamba posachedwapa. Zochitika zikuluzikulu za m’dzikoli zingachititse kuti ena adzuke mwauzimu n’kuyamba kuchita chidwi ndi uthenga wa Ufumu. Komabe, ambiri amayambiranso kugona m’malo mokhalabe maso. Ngakhalenso ena omwe amakhulupirira kuti kuli tsiku lachiweruzo, amaona kuti lili kutali kwambiri. (2 Pet. 3:3, 4) Koma ifeyo tsiku lililonse timazindikira kuti malangizo akuti tikhalebe maso ndi ofunika kwambiri. (1 Ates. 5:6) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi maganizo odekha komanso osatekeseka? Kukhala ndi maganizo otere, kungatithandize kuti tisamalowerere ndale kapena zochitika za m’dzikoli. Pamene tsiku la Yehova likuyandikira, tizikakamizidwa kwambiri kuti tizichita nawo zinthu zimenezi. Komabe, sitiyenera kuda nkhawa kuti tidzatani tikadzakumana ndi zoterezi. Mzimu wa Mulungu udzatithandiza kukhala ndi maganizo odekha komanso osatekeseka ndipo tidzasankha zochita mwanzeru.—Luka 12:11, 12. w23.06 10 ¶6-7
Lachitatu, July 9
Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, chonde ndikumbukireni ndi kundipatsa mphamvu.—Ower. 16:28.
Kodi n’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukamva dzina lakuti Samisoni? N’kutheka kuti mumaganizira za munthu wamphamvu kwambiri. Zimenezotu ndi zoona. Komatu pa nthawi ina Samisoni anasankha zinthu molakwika, zomwe zinamubweretsera mavuto aakulu. Komabe Yehova ankaganizira zinthu zambiri zimene Samisoni anachita pomutumikira mokhulupirika ndipo analemba m’Baibulo kuti zizitithandiza. Yehova anagwiritsa ntchito Samisoni pochita zinthu zodabwitsa n’cholinga chofuna kuthandiza Aisiraeli, omwe anali anthu ake. Patapita zaka zambiri Samisoni atamwalira, Yehova anauzira mtumwi Paulo kuti alembe dzina la Samisoni pagulu la anthu omwe anasonyeza chikhulupiriro. (Aheb. 11:32-34) Chitsanzo cha Samisoni chingatilimbikitse. Iye ankadalira Yehova ngakhale pa nthawi zovuta kwambiri. Tingalimbikitsidwe komanso kuphunzira zambiri pachitsanzo chake. w23.09 2 ¶1-2
Lachinayi, July 10
Nthawi zonse muzipemphera kwa Mulungu.—Afil. 4:6.
Tingathe kupitiriza kukhala opirira ngati nthawi zonse timapemphera mochokera pansi pa mtima komanso kufotokozera Yehova nkhawa zathu. (1 Ates. 5:17) N’kutheka kuti panopa simukukumana ndi mayesero aakulu. Komabe, kodi mumapempha Yehova kuti akutsogolereni nthawi iliyonse imene mwakhumudwa, kusokonezeka maganizo kapena kupanikizika? Ngati nthawi zonse mumapempha Mulungu kuti akuthandizeni pa mavuto alionse, simudzazengereza kumupempha kuti akuthandizeni mukadzakumana ndi mavuto aakulu m’tsogolo. Komanso simudzakayikira kuti Yehova akudziwa bwino nthawi imene angakuthandizireni ndiponso mmene angachitire zimenezi. (Sal. 27:1, 3) Zingadzakhale zosavuta kupirira chisautso chachikulu ngati timapirira mayesero panopa. (Aroma 5:3) N’chifukwa chiyani tikutero? Abale ambiri amaona kuti kupirira mayesero omwe anakumana nawo, kunawathandiza kuti apirirenso mayesero otsatira. Izi zawathandiza kuti azikhulupirira kwambiri kuti Yehova ndi wokonzeka kuwathandiza. Zotsatira zake n’zakuti chikhulupirirocho chimawathandiza kuti azitha kupirira mayesero otsatira.—Yak. 1:2-4. w23.07 3 ¶7-8
Lachisanu, July 11
Ndavomera zimene wapempha.—Gen. 19:21.
Kudzichepetsa komanso kukoma mtima kumachititsa Yehova kuti akhale wololera. Mwachitsanzo, Yehova anasonyeza kuti ndi wodzichepetsa pamene ankafuna kuwononga anthu oipa ku Sodomu. Pogwiritsa ntchito angelo ake, Yehova anauza Loti kuti athawire kudera lamapiri. Koma Loti ankachita mantha kupita kumeneko. Choncho anachonderera Yehova kuti iye ndi banja lake athawire ku Zowari, tauni yaing’ono imene inkafunikanso kuwonongedwa. Yehova akanatha kuuza Loti kuti atsatirebe malangizo amene anamupatsa. M’malomwake anavomereza zimene Loti anapempha ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti asawononge mzinda wa Zowari. (Gen. 19:18-22) Patapita zaka zambiri, Yehova anasonyezanso chifundo kwa anthu a mumzinda wa Nineve. Iye anatumiza Yona kuti akalengeze kuti mzinda woipa wa Nineve uwonongedwa. Koma ataona kuti anthu a mumzindawo alapa, anawamvera chisoni ndipo sanawawononge.—Yona 3:1, 10; 4:10, 11. w23.07 21 ¶5
Loweruka, July 12
Anapha [Yehoasi] . . . koma sanamuike m’manda a mafumu.—2 Mbiri 24:25.
Kodi tikuphunzira chiyani pachitsanzo cha Yehoasi? Iye anali ngati mtengo wa mizu yosazama womwe umadalira mtengo wina kuti uime bwino. Choncho Yehoyada yemwe anali ngati mtengo womwe ankadalira atamwalira, Yehoasi anayamba kumvetsera anthu ampatuko ndipo anakhala wosakhulupirika kwa Yehova. Zimenezi zikusonyeza kuti sitiyenera kungodalira chitsanzo chabwino cha Akhristu anzathu ngakhalenso achibale athu kuti tiziopa Mulungu. Kuti tipitirize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, ifenso patokha tiyenera kumamukonda komanso kumulemekeza kwambiri pophunzira Mawu ake nthawi zonse, kuwaganizira mozama komanso kupemphera. (Yer. 17:7, 8; Akol. 2:6, 7) Yehova safuna zinthu zambiri kwa ife. Zimene amafuna zafotokozedwa palemba la Mlaliki 12:13, lomwe limati: “Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake chifukwa zimenezi ndi zimene munthu akuyenera kuchita.” Tikamaopa Mulungu, tidzatha kupirira mavuto amene tingakumane nawo n’kukhalabe olimba ndipo palibe chomwe chidzathe kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. w23.06 19 ¶17-19
Lamlungu, July 13
Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.—Chiv. 21:5.
Vesili, limayamba ndi mawu akuti: “Ndipo Mulungu amene wakhala pampando wachifumu anati.” (Chiv. 21:5a) Imeneyi ndi imodzi mwa nthawi zitatu pamene Yehova analankhula yekha m’masomphenya m’buku la Chivumbulutso. Choncho apa Yehova akutsimikizira yekha, osati kudzera mwa mngelo wamphamvu kapenanso Yesu. Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti mawu otsatirawo ndi odalirika kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yehova “sanganame.” (Tito 1:2) Izi zikusonyeza kuti zimene timawerenga pa Chivumbulutso 21:5, 6 ndi zodalirika kwambiri. Taganizirani mawu akuti: “Taonani.” (Chiv. 21:5) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “taonani” atchulidwa mobwerezabwereza m’buku la Chivumbulutso. Ndiye kodi mawu otsatira ndi oti chiyani? Mulungu akunena kuti: “Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.” N’zoona kuti Yehova akufotokoza zinthu zatsopano zimene adzachite m’tsogolo, koma kwa iye zimenezi n’zosakayikitsa moti akufotokoza ngati kuti zikuchitika.—Yes. 46:10. w23.11 3-4 ¶7-8
Lolemba, July 14
Anatuluka panja n’kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.—Mat. 26:75.
Mtumwi Petulo ankalakwitsa zinthu zina. Taganizirani zitsanzo zochepa izi. Pa nthawi ina, iye anadzudzula Yesu atafotokoza kuti adzavutika komanso kufa kuti akwaniritse ulosi wa m’Baibulo. (Maliko 8:31-33) Petulo ndi atumwi ena ankakangananso mobwerezabwereza pa nkhani yakuti wamkulu ndani. (Maliko 9:33, 34) Pa usiku womaliza Yesu asanaphedwe, Petulo anadula khutu la munthu wina. (Yoh. 18:10) Usiku womwewo, iye anachita mantha ndipo anakana Yesu katatu. (Maliko 14:66-72) Zimenezi zinachititsa kuti Petulo alire mopwetekedwa mtima kwambiri. Yesu sanasiye kukonda mtumwi wakeyu, yemwe anafooka kwambiri chifukwa cha zimene analakwitsa. Ataukitsidwa, iye anapereka mwayi kwa Petulo woti asonyeze kuti amamukondabe. Yesu anapempha Petulo kuti akhale wodzichepetsa n’kumaweta nkhosa zake. (Yoh. 21:15-17) Petulo anavomera kuchita zimenezi. Choncho pa tsiku la Pentekosite, iye anali ku Yerusalemu ndipo anali pagulu la anthu oyambirira kudzozedwa ndi mzimu woyera. w23.09 22 ¶6-7
Lachiwiri, July 15
Weta ana a nkhosa anga.—Yoh. 21:16.
Mtumwi Petulo analimbikitsa akulu anzake kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu.” (1 Pet. 5:1-4) Ngati ndinu mkulu, timadziwa kuti mumakonda abale ndi alongo anu ndipo mumafuna kuwasamalira. Komabe, nthawi zina mungamaone kuti mwatanganidwa kapena mwatopa kwambiri moti simungathe kukwaniritsa udindowu. Zikatere, kodi mungatani? Muzimuuza Yehova nkhawa zanu zonse. Petulo analemba kuti: “Ngati wina akutumikira ena, aziwatumikira modalira mphamvu imene Mulungu amapereka.” (1 Pet. 4:11) Abale ndi alongo anu angakumane ndi mavuto omwe sangatheretu panopa. Koma muzikumbukira kuti “m’busa wamkulu,” yemwe ndi Yesu Khristu, angawathandize kuposa wina aliyense. Iye angawathandize panopa komanso m’dziko latsopano. Mulungu amangofuna kuti akulu azikonda abale awo, kuwasamalira komanso kukhala “zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” w23.09 29-30 ¶13-14
Lachitatu, July 16
Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu anzeru ndi opanda pake.—1 Akor. 3:20.
Tizipewa kuchita zinthu potengera nzeru za anthu. Tikamaona zinthu potengera nzeru za anthu, tingasiye kutsatira mfundo za Yehova. (1 Akor. 3:19) Nthawi zambiri “nzeru za m’dzikoli” zimachititsa kuti anthu asamamvere Mulungu. Akhristu ena a ku Pegamo ndi Tiyatira anayamba kumaona nkhani yokhudza kulambira mafano komanso chiwerewere ngati mmene anthu ambiri m’mizindayo ankaonera. Yesu anadzudzula mwamphamvu mipingo imeneyi chifukwa cholekerera khalidwe la chiwerewere. (Chiv. 2:14, 20) Masiku anonso timakakamizidwa kuti tiziona zinthu molakwika. Achibale kapenanso anzathu angatikakamize kapena kutilimbikitsa kuti tichite zinthu zimene zingachititse kuti tisamvere Yehova. Mwachitsanzo, iwo angamatiuze kuti palibe vuto kuchita zomwe tikufuna komanso kuti mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino n’zachikale. Nthawi zina tingamaone kuti malangizo amene Yehova amatipatsa ndi osathandiza. Mwinanso mpaka tikhoza kuyesedwa kuti ‘tipitirire zinthu zolembedwa.’—1 Akor. 4:6. w23.07 16 ¶10-11
Lachinayi, July 17
Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse, ndipo ndi m’bale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.—Miy. 17:17.
Mariya, yemwe anali mayi ake a Yesu, ankafunika kulimbikitsidwa. Iye sanali pabanja, koma mngelo anamuuza kuti adzakhala ndi pakati. Analinso asanalerepo mwana, koma ankafunika kusamalira mwana yemwe adzakhale Mesiya. Komanso popeza anali asanagonepo ndi mwamuna, kodi akanamufotokozera bwanji Yosefe, yemwe ankayembekezera kukhala naye pabanja? (Luka 1:26-33) Kodi Mariya anapeza bwanji mphamvu? Iye anadalira ena kuti amuthandize. Mwachitsanzo, anapempha Gabirieli kuti amufotokozere zambiri zokhudza utumikiwu. (Luka 1:34) Pambuyo pake, iye anapita kwa wachibale wake, dzina lake Elizabeti, yemwe ankakhala “kudera lamapiri” la Yuda. Ulendo umenewu unali wothandiza kwambiri. Elizabeti anayamikira Mariya ndipo mouziridwa ndi Yehova, anamufotokozera ulosi wokhudza mwana yemwe adzabadweyo. (Luka 1:39-45) Mariya ananena kuti Yehova ‘wamuchitira zamphamvu ndi dzanja lake.’ (Luka 1:46-51) Yehova anapatsa mphamvu Mariya pogwiritsa ntchito Gabirieli ndi Elizabeti. w23.10 14-15 ¶10-12
Lachisanu, July 18
[Anatipanga] kukhala mafumu ndi ansembe kuti titumikire Mulungu wake ndi Atate wake.—Chiv. 1:6.
Pali ophunzira ochepa a Khristu adzozedwa ndi mzimu woyera, okwana 144,000 omwe ali pa ubwenzi wapadera ndi Yehova. Anthu amenewa adzatumikira ngati ansembe kumwamba limodzi ndi Yesu. (Chiv. 1:6; 14:1) Malo Oyera a chihema amaimira kuti iwowa atengedwa kukhala ana auzimu a Mulungu pa nthawi imene ali padziko lapansi. (Aroma 8:15-17) Malo Oyera Koposa amaimira kumwamba, komwe Yehova amakhala. “Nsalu,” imene inkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa imaimira thupi la Yesu limene linali ngati chotchinga chomulepheretsa kupita kumwamba kukatumikira ngati Mkulu wa Ansembe wapamwamba m’kachisi wauzimu. Yesu atapereka thupi lake ngati nsembe yopulumitsira anthu, anatsegula njira yoti Akhristu onse odzozedwa akakhale ndi moyo kumwamba. Iwonso amafunika kusiya thupi lomwe ali nalo padzikoli kuti akalandire mphoto yawo kumwamba.—Aheb. 10:19, 20; 1 Akor. 15:50. w23.10 28 ¶13
Loweruka, July 19
Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni.—Aheb. 11:32.
Gidiyoni anayankha modekha pamene amuna a ku Efuraimu ankamuimba mlandu. (Ower. 8:1-3) Iye sanayankhe mokwiya. Iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa powamvetsera komanso kulankhula nawo mokoma mtima, zomwe zinachititsa kuti mitima ya anthuwo ikhale m’malo. Akulu anzeru amatsanzira Gidiyoni pomvetsera mosamala komanso kuyankha modekha akamaimbidwa mlandu. (Yak. 3:13) Akamachita zimenezi amathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere. Pamene anthu anayamba kutamanda Gidiyoni chifukwa chopambana pankhondo yolimbana ndi Amidiyani, iye anathandiza anthuwo kuti apereke ulemerero kwa Yehova. (Ower. 8:22, 23) Kodi abale audindo angatsanzire bwanji Gidiyoni? Iwo ayenera kupereka ulemerero kwa Yehova chifukwa cha zimene akwanitsa kuchita. (1 Akor. 4:6, 7) Mwachitsanzo, ngati mkulu akutamandidwa chifukwa cha luso lophunzitsa lomwe ali nalo, iye angathandize anthuwo kuti aziganizira kumene kukuchokera mfundo zomwe amaphunzitsazo, komwe ndi m’Mawu a Mulungu, kapena maphunziro omwe gulu la Yehova limapereka. Nthawi ndi nthawi, akulu ayenera kumadzifufuza kuti aone ngati akuchititsa anthu kuti azitamanda iwowo m’malo mwa Yehova. w23.06 4 ¶7-8
Lamlungu, July 20
Maganizo anga ndi osiyana ndi maganizo anu.—Yes. 55:8.
Ngati zimene tapempha sizikuchitika tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndikupemphazi ndi zoyenera?’ Nthawi zambiri anthu timaganiza kuti timadziwa zomwe ndi zoyenera kwa ifeyo. Koma zomwe timapempha zikhoza kukhala zosathandiza kwenikweni. Tikamapempherera vuto linalake, pakhoza kukhala njira ina yabwino yothetsera vutolo kusiyana ndi imene tikupempha. Ndipo zinthu zina zomwe tingapemphe zingakhale zosagwirizana ndi zimene Yehova amafuna. (1 Yoh. 5:14) Mwachitsanzo, taganizirani za makolo omwe anapempha Yehova kuti mwana wawo apitirizebe kukhala m’choonadi. Zimene anapemphazi zikhoza kuoneka ngati zoyenera. Koma Yehova sakakamiza munthu aliyense kuti azimutumikira. Amafuna kuti aliyense azisankha kumutumikira, ngakhalenso ana. (Deut. 10:12, 13; 30:19, 20) M’malomwake makolowo angapemphe Yehova kuti awathandize kuti azimufika pamtima mwanayo n’cholinga choti azikonda Yehova komanso kukhala naye pa ubwenzi.—Miy. 22:6; Aef. 6:4. w23.11 21 ¶5; 23 ¶12
Lolemba, July 21
Pitirizani kulimbikitsana.—1 Ates. 4:18.
N’chifukwa chiyani kutonthoza ena kumasonyeza kuti tili ndi chikondi? Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo linanena kuti mawu akuti “kutonthoza” omwe Paulo anagwiritsa ntchito amatanthauza “kuima pafupi ndi munthu kuti timulimbikitse pamene wakumana ndi vuto lalikulu.” Choncho tikatonthoza m’Khristu mnzathu yemwe wakumana ndi vuto, timamuthandiza kuti aimirire n’kupitiriza kuyenda panjira yokalandira moyo. Nthawi iliyonse yomwe tatonthoza m’bale kapena mlongo, timasonyeza kuti timakonda Akhristu anzathu. (2 Akor. 7:6, 7, 13) Kutonthoza ena n’kogwirizananso ndi chifundo. N’chifukwa chiyani tikutero? Mtima wachifundo ndi umene umalimbikitsa munthu kuti atonthoze ena komanso kuwathandiza. Choncho timayamba ndi kukhala ndi chifundo, kenako timatonthoza ena. Paulo anagwirizanitsa chifundo cha Yehova ndi zimene amachita potonthoza ena. Iye ananena kuti Yehova ndi “Bambo wachifundo chachikulu ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse.”—2 Akor. 1:3. w23.11 9-10 ¶8-10
Lachiwiri, July 22
Tikhozanso kumasangalala tikakumana ndi mavuto.—Aroma 5:3.
Otsatira onse a Khristu amayembekezera kukumana ndi mavuto. Taganizirani zimene zinachitikira mtumwi Paulo. Polembera Akhristu a ku Tesalonika, iye anati: “Pamene tinali nanu limodzi, tinkakuuziranitu kuti tidzakumana ndi mavuto ndipo monga mmene mukudziwira, zimene tinkakuuzanizo ndi zimene zachitikadi.” (1 Ates. 3:4) Ndipo kwa Akhristu a ku Korinto, iye analemba kuti: “Abale, tikufuna muzidziwa za mavuto amene tinakumana nawo, . . . tinalibe chiyembekezo choti tikhala ndi moyo.” (2 Akor. 1:8; 11:23-27) Masiku anonso Akhristu angakumane ndi mavuto enaake. (2 Tim. 3:12) Nanga bwanji inuyo? Kodi mwakumana ndi mavuto chifukwa chokhulupirira komanso kutsatira Yesu? Mwina mumanyozedwa ndi anzanu kapena achibale. Mwinanso amakuchitirani nkhanza. Kodi mumakumana ndi mavuto kuntchito chifukwa choyesetsa kuchita zinthu moona mtima? (Aheb. 13:18) Kodi mumatsutsidwa ndi akuluakulu a boma chifukwa chouza ena za chiyembekezo chanu? Kaya tikumane ndi mavuto otani, Paulo anati tiyenera kukhalabe osangalala. w23.12 10-11 ¶9-10
Lachitatu, July 23
Mwandiputira mavuto aakulu.—Gen. 34:30.
Yakobo anapirira mavuto ambiri. Iye anali ndi banja lalikulu koma si nthawi zonse pamene ana ake ankagwirizana. Iwo anafika mpaka pogulitsa m’bale wawo Yosefe ku ukapolo. Awiri mwa ana a Yakobo, Simiyoni ndi Levi anachititsa manyazi banja lawo komanso ananyozetsa dzina la Yehova. Kuwonjezera pamenepo mkazi wokondedwa wa Yakobo, Rakele, anamwalira pamene ankabereka mwana wawo wachiwiri. Komanso chifukwa cha njala yaikulu, Yakobo anakakamizika kusamukira ku Iguputo ali wokalamba. (Gen. 34:30; 35:16-19; 37:28; 45:9-11, 28) Pa zinthu zonse zomwe zinamuchitikira, Yakobo sanasiye kukhulupirira Yehova komanso malonjezo ake. Nayenso Yehova anamusonyeza kuti ankasangalala naye. Mwachitsanzo, Yehova anadalitsa Yakobo pomupatsa chuma chambiri. Ndipo tangoganizani mmene iye anayamikirira Yehova atakumananso ndi Yosefe mwana wake, yemwe ankaganiza kuti anafa kalekale. Yakobo ankakwanitsa kupirira mavuto omwe ankakumana nawo chifukwa anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Gen. 30:43; 32:9, 10; 46:28-30) Ngati ifenso titakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, tingathe kupirira mavuto osayembekezereka amene tingakumane nawo. w23.04 15 ¶6-7
Lachinayi, July 24
Yehova ndi Mʼbusa wanga. Sindidzasowa kanthu.—Sal. 23:1.
Davide, yemwe analemba Salimo 23, anasonyeza kuti sankakayikira kuti Yehova amamukonda kwambiri. Iye anafotokoza zokhudza ubwenzi wolimba womwe unalipo pakati pa iyeyo ndi Yehova, yemwe anali M’busa wake. Davide ankamva kuti anali wotetezeka chifukwa ankalola kuti Yehova azimutsogolera ndipo ankamudalira pa chilichonse. Ankadziwa kuti Yehova azimusonyeza chikondi kwa moyo wake wonse. N’chifukwa chiyani iye sankakayikira zimenezi ngakhale pang’ono? Davide ankaona kuti Yehova amamusamalira chifukwa nthawi zonse ankamupatsa zimene ankafunikira. Ankadziwanso kuti Yehova ndi mnzake ndipo amasangalala naye. N’chifukwa chake sankakayikira kuti kaya akumana ndi zotani Yehova adzapitiriza kumusamalira. Popeza Davide ankakhulupirira kuti Yehova amamukonda komanso adzamusamalira, zinamuthandiza kuti asamade nkhawa, m’malomwake azisangalala.—Sal. 16:11. w24.01 29 ¶12-13
Lachisanu, July 25
Ine ndili limodzi ndi inu masiku onse mpaka mʼnyengo ya mapeto a nthawi ino.—Mat. 28:20.
Kungoyambira pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, anthu a Yehova m’mayiko ambiri akhala akugwira ntchito yolalikira popanda kusokonezedwa. Ndipotu ntchitoyi yakhala ikuyenda bwino kwambiri. Masiku ano, abale a m’Bungwe Lolamulira akupitirizabe kudalira malangizo ochokera kwa Khristu. Iwo amafuna kuti malangizo omwe amapereka kwa abale azikhala ogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Ndipo amagwiritsa ntchito oyang’anira madera komanso akulu kuti azipereka malangizowo kumipingo. Akulu odzozedwa ali ‘m’dzanja lamanja’ la Khristu. (Chiv. 2:1) N’zoona kuti akulu onse si angwiro ndipo amalakwitsa zinthu. Mose ndi Yoswa, nawonso nthawi zina ankalakwitsa zinthu, ngatinso mmene ankachitira atumwi. (Num. 20:12; Yos. 9:14, 15; Aroma 3:23) Komabe Khristu akutsogolera kapolo wokhulupirika komanso akulu, ndipo apitiriza kuchita zimenezi. Choncho, tili ndi zifukwa zokwanira zotichititsa kukhulupirira malangizo omwe Yesu amatipatsa kudzera mwa anthu omwe wasankha kuti azititsogolera. w24.02 23-24 ¶13-14
Loweruka, July 26
Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.—Aef. 5:1.
Masiku ano tingasangalatse Yehova, polankhula za iye mosonyeza kuti timayamikira komanso kumukonda. Tikamalalikira, timakumbukira kuti cholinga chathu chachikulu ndi kuthandiza anthu kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuwathandiza kuti nawonso azimuona kuti ndi Atate wawo wachikondi. (Yak. 4:8) Timasangalala kusonyeza anthu zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Yehova kuti ndi wachikondi, chilungamo, nzeru, mphamvu komanso ali ndi makhalidwe ena abwino. Timatamandanso Yehova ndi kumusangalatsa tikamayesetsa kumutsanzira. Tikamachita zimenezi, timakhala osiyana kwambiri ndi anthu a m’dziko loipali. Ena angamaone kuti ndife osiyana ndipo angamadabwe chifukwa chake zili choncho. (Mat. 5:14-16) Ndiyeno tikamachita nawo zinthu za tsiku ndi tsiku, tingathe kuwafotokozera chifukwa chake timachita zinthu mosiyana ndi iwowo. Zotsatira zake n’zakuti anthu amtima wabwino amayamba kukopeka ndi Mulungu wathu. Tikamatamanda Yehova m’njira zimenezi, timasangalatsa mtima wake.—1 Tim. 2:3, 4. w24.02 10 ¶7
Lamlungu, July 27
[Muzitha] kulimbikitsa . . . ndiponso kudzudzula.—Tito 1:9.
Kuti mukhale Mkhristu wolimba mwauzimu muyenera kuphunzira maluso amene angakuthandizeni. Malusowa angakuthandizeni kuti mukwaniritse bwino maudindo anu mumpingo, mupeze ntchito kuti muzipeza zofunika pa moyo wanu kapena wa banja lanu komanso kuti muzigwirizana ndi anthu ena. Mwachitsanzo, muziphunzira kuwerenga ndi kulemba bwino. Baibulo limanena kuti munthu amene amawerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku n’kumawaganizira mozama, amakhala wosangalala ndipo zinthu zimamuyendera bwino. (Sal. 1:1-3) Munthu akamawerenga Baibulo tsiku lililonse, amadziwa maganizo a Yehova ndipo izi zimamuthandiza kuti aziganiza bwino komanso azitsatira mfundo za m’Malemba. (Miy. 1:3, 4) Abale ndi alongo athu amafuna kuthandizidwa ndi amuna odziwa kuphunzitsa komanso kupereka malangizo ochokera m’Baibulo. Ngati mumawerenga komanso kulemba bwino, mukhoza kukonzekera ndemanga komanso nkhani zimene zingapindulitse anthu ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Mungathenso kulemba notsi zimenezi zingakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu komanso kulimbikitsa anthu ena. w23.12 26-27 ¶9-11
Lolemba, July 28
Amene ali wogwirizana ndi inu ndi wamkulu kuposa amene ali wogwirizana ndi dziko.—1 Yoh. 4:4.
Mukamachita mantha, muziganizira zimene Yehova adzachite m’tsogolo, Satana akadzachotsedwa. Pamsonkhano wachigawo wa 2014, panali chitsanzo cha zimene tingachite poganizira za chiyembekezo chathu. Mu chitsanzocho, bambo ankakambirana ndi banja lake mmene lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 lingamvekere ngati mavesiwa atakhala kuti akufotokoza mmene zidzakhalire m’Paradaiso. Anawerenga kuti: “M’dziko latsopano, idzakhala nthawi yapadera komanso yosangalatsa. Pakuti anthu adzakhala okonda anzawo, okonda kulambira Mulungu, odzichepetsa, ofatsa, otamanda Mulungu, omvera makolo, oyamikira, okhulupirika, okonda achibale awo, ofuna kugwirizana ndi anzawo, onena zabwino za anzawo, odziletsa, odekha, okonda zabwino, odalirika, oganizira za ena, osadzitukumula ndiponso osanyada, okonda Mulungu, m’malo mokonda zosangalatsa, ndiponso odziperekadi kwa Mulungu. Anthu amenewa usasiyane nawo.” Kodi mumakambirana ndi anthu a m’banja lanu kapena anzanu mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano? w24.01 6 ¶13-14
Lachiwiri, July 29
Umandisangalatsa kwambiri.—Luka 3:22.
N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amasangalala ndi anthu ake onse monga gulu. Baibulo limati: “Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Komabe nthawi zina ena angamakayikire n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amasangalala ndi ineyo pandekha?’ Ambiri mwa atumiki okhulupirika a Yehova akale nthawi zinanso ankavutika ndi maganizo ngati amenewa. (1 Sam. 1:6-10; Yobu 29:2, 4; Sal. 51:11) Baibulo limasonyeza kuti anthu omwe si angwiro akhoza kusangalatsa Yehova. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kukhulupirira Yesu Khristu komanso kubatizidwa. (Yoh. 3:16) Tikatero timasonyeza poyera kuti talapa machimo athu ndipo talonjeza kuti tizichita zimene Mulungu amafuna. (Mac. 2:38; 3:19) Yehova amasangalala akaona tikuchita zimenezi n’cholinga choti tikhale naye pa ubwenzi. Iye amasangalala nafe n’kumationa ngati anzake apamtima tikamapitiriza kuchita zimene tingathe pokwaniritsa zimene tinalonjeza podzipereka.—Sal. 25:14. w24.03 26 ¶1-2
Lachitatu, July 30
Ife sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.—Mac. 4:20.
Tingatsanzire ophunzira a Yesu, popitiriza kulalikira ngakhale pamene akuluakulu a boma aletsa ntchito yathu. Ifenso tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza kuti tikwaniritse utumiki wathu. Choncho tizimupempha kuti atithandize kukhala olimba mtima komanso atipatse nzeru. Tizimupemphanso kuti atithandize kupirira mavuto. Ambirife tikukumana ndi mavuto okhudza thanzi kapena maganizo, imfa ya okondedwa athu, mavuto a m’banja, kuzunzidwa kapenanso mavuto ena. Ndipo zinthu monga miliri komanso nkhondo zachititsa kuti zikhale zovuta kwambiri kulimbana ndi mavutowa. Choncho muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. Muzimuuza zimene zikuchitika pa moyo wanu ngati mmene mungachitire ndi mnzanu wapamtima. Muzikhulupirira kuti Yehova “adzachitapo kanthu.” (Sal. 37:3, 5) Kulimbikira kupemphera kungatithandize ‘kupirira mavuto.’ (Aroma 12:12) Yehova amadziwa zimene zikuchitikira atumiki ake ndipo ‘amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.’—Sal. 145:18, 19. w23.05 5-6 ¶12-15
Lachinayi, July 31
Nthawi zonse muzitsimikizira kuti chovomerezeka kwa Ambuye nʼchiti.—Aef. 5:10.
Tikafuna kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu, tiyenera “kuzindikira chifuniro cha Yehova” n’kuchita zinthu mogwirizana ndi zimenezo. (Aef. 5:17) Tikapeza mfundo za m’Baibulo zogwirizana ndi mmene zinthu zilili kwa ifeyo timakhala kuti tapeza maganizo a Yehova pa nkhaniyo. Ndiyeno tikamagwiritsa ntchito mfundozo, timasankha zochita mwanzeru. Satana, yemwe ndi mdani wathu “woipayo,” amafuna kuti tizitanganidwa ndi zinthu zam’dzikoli n’cholinga choti tisakhale ndi nthawi yotumikira Mulungu. N’zosavuta kuti Mkhristu aziika patsogolo chuma, maphunziro kapena ntchito m’malo motumikira Yehova. (1 Yoh. 5:19) Zikatero, munthuyo amakhala kuti wayamba kuganiza ngati anthu a m’dzikoli. N’zoona kuti zinthu zimenezi pazokha si zolakwika koma siziyenera kukhala pamalo oyamba. w24.03 24 ¶16-17