Lachinayi, July 17
Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse, ndipo ndi m’bale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.—Miy. 17:17.
Mariya, yemwe anali mayi ake a Yesu, ankafunika kulimbikitsidwa. Iye sanali pabanja, koma mngelo anamuuza kuti adzakhala ndi pakati. Analinso asanalerepo mwana, koma ankafunika kusamalira mwana yemwe adzakhale Mesiya. Komanso popeza anali asanagonepo ndi mwamuna, kodi akanamufotokozera bwanji Yosefe, yemwe ankayembekezera kukhala naye pabanja? (Luka 1:26-33) Kodi Mariya anapeza bwanji mphamvu? Iye anadalira ena kuti amuthandize. Mwachitsanzo, anapempha Gabirieli kuti amufotokozere zambiri zokhudza utumikiwu. (Luka 1:34) Pambuyo pake, iye anapita kwa wachibale wake, dzina lake Elizabeti, yemwe ankakhala “kudera lamapiri” la Yuda. Ulendo umenewu unali wothandiza kwambiri. Elizabeti anayamikira Mariya ndipo mouziridwa ndi Yehova, anamufotokozera ulosi wokhudza mwana yemwe adzabadweyo. (Luka 1:39-45) Mariya ananena kuti Yehova ‘wamuchitira zamphamvu ndi dzanja lake.’ (Luka 1:46-51) Yehova anapatsa mphamvu Mariya pogwiritsa ntchito Gabirieli ndi Elizabeti. w23.10 14-15 ¶10-12
Lachisanu, July 18
[Anatipanga] kukhala mafumu ndi ansembe kuti titumikire Mulungu wake ndi Atate wake.—Chiv. 1:6.
Pali ophunzira ochepa a Khristu adzozedwa ndi mzimu woyera, okwana 144,000 omwe ali pa ubwenzi wapadera ndi Yehova. Anthu amenewa adzatumikira ngati ansembe kumwamba limodzi ndi Yesu. (Chiv. 1:6; 14:1) Malo Oyera a chihema amaimira kuti iwowa atengedwa kukhala ana auzimu a Mulungu pa nthawi imene ali padziko lapansi. (Aroma 8:15-17) Malo Oyera Koposa amaimira kumwamba, komwe Yehova amakhala. “Nsalu,” imene inkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa imaimira thupi la Yesu limene linali ngati chotchinga chomulepheretsa kupita kumwamba kukatumikira ngati Mkulu wa Ansembe wapamwamba m’kachisi wauzimu. Yesu atapereka thupi lake ngati nsembe yopulumitsira anthu, anatsegula njira yoti Akhristu onse odzozedwa akakhale ndi moyo kumwamba. Iwonso amafunika kusiya thupi lomwe ali nalo padzikoli kuti akalandire mphoto yawo kumwamba.—Aheb. 10:19, 20; 1 Akor. 15:50. w23.10 28 ¶13
Loweruka, July 19
Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni.—Aheb. 11:32.
Gidiyoni anayankha modekha pamene amuna a ku Efuraimu ankamuimba mlandu. (Ower. 8:1-3) Iye sanayankhe mokwiya. Iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa powamvetsera komanso kulankhula nawo mokoma mtima, zomwe zinachititsa kuti mitima ya anthuwo ikhale m’malo. Akulu anzeru amatsanzira Gidiyoni pomvetsera mosamala komanso kuyankha modekha akamaimbidwa mlandu. (Yak. 3:13) Akamachita zimenezi amathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere. Pamene anthu anayamba kutamanda Gidiyoni chifukwa chopambana pankhondo yolimbana ndi Amidiyani, iye anathandiza anthuwo kuti apereke ulemerero kwa Yehova. (Ower. 8:22, 23) Kodi abale audindo angatsanzire bwanji Gidiyoni? Iwo ayenera kupereka ulemerero kwa Yehova chifukwa cha zimene akwanitsa kuchita. (1 Akor. 4:6, 7) Mwachitsanzo, ngati mkulu akutamandidwa chifukwa cha luso lophunzitsa lomwe ali nalo, iye angathandize anthuwo kuti aziganizira kumene kukuchokera mfundo zomwe amaphunzitsazo, komwe ndi m’Mawu a Mulungu, kapena maphunziro omwe gulu la Yehova limapereka. Nthawi ndi nthawi, akulu ayenera kumadzifufuza kuti aone ngati akuchititsa anthu kuti azitamanda iwowo m’malo mwa Yehova. w23.06 4 ¶7-8