Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ‘Nzeru za Mulungu N’zozama’
    Yandikirani Yehova
    • Mbalame zikuuluka.

      MUTU 17

      ‘Nzeru za Mulungu N’zozama’

      1, 2. Kodi cholinga cha Yehova chokhudza tsiku la 7 chinali chiyani, nanga panachitika vuto liti?

      YEHOVA atalenga anthu kumapeto kwa tsiku la 6, anaona kuti “zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.” (Genesis 1:31) Koma kuchiyambi kwa tsiku la 7, Adamu ndi Hava anasankha kumvera Satana ndipo anagalukira Yehova. Anthu, omwe anali apadera kwambiri pa zinthu zonse zimene Yehova analenga padzikoli, anachimwa, sanalinso angwiro ndipo anali oti adzafa. Zimenezitu zinali zomvetsa chisoni kwambiri.

      2 Zinaoneka ngati cholinga cha Yehova chokhudza tsiku la 7 chalephereka momvetsa chisoni. Tsikuli linali loti lidzatenga zaka masauzande ambiri ngati mmene zinalilinso ndi masiku ena 6 oyambirira aja. Yehova ananena kuti tsikuli likhale lopatulika ndipo linali loti likamadzatha, dziko lonse lapansi lidzakhala Paradaiso momwe muzidzakhala anthu angwiro. (Genesis 1:28; 2:3) Koma popeza kuti anthu sanamvere Mulungu, zomwe zinayambitsa mavuto aakulu, kodi zimenezi zikanatheka bwanji? Kodi Mulungu akanatani pamenepa? Zimene iye anachita zinasonyeza m’njira yapadera kwambiri kuti ndi wanzeru.

      3, 4. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene Yehova anachita ulamuliro wake utaukiridwa mu Edeni ndi chitsanzo choti ali ndi nzeru zogometsa? (b) Kodi kudzichepetsa kuyenera kutichititsa kumakumbukira mfundo iti tikamaphunzira zokhudza nzeru za Yehova?

      3 Yehova anachitapo kanthu nthawi yomweyo. Anapereka chilango kwa amene anasankha kuukira ulamuliro wakewo, ndipo pa nthawi imodzimodziyo, anasonyezanso kuti adzathetsa mavuto amene anali atangoyambika kumenewo. (Genesis 3:15) Njira imene Mulungu anasankha kuti agwiritse ntchito pothetsa mavutowo, inali yoti azidzachita zinthu pang’onopang’ono ndipo padzadutsa nthawi yaitali kwambiri mpaka pamene mavuto onse oyambitsidwa ndi oukira ulamuliro wake adzathetsedwe. Njirayi inali yosavuta koma yanzeru kwambiri moti tikhoza kuiphunzira komanso kuiganizira kwa moyo wathu wonse n’kumaonabe kuti ndi yosangalatsa. Ndiponso n’zosakayikitsa ngakhale pang’ono kuti njira imeneyi idzathandiza kuti cholinga cha Mulungu chikwaniritsidwe. Pogwiritsa ntchito njirayi Mulungu adzathetsa zoipa zonse, uchimo ndiponso imfa. Njirayi idzathandizanso kuti anthu okhulupirika akhale angwiro. Zonsezi zidzachitika tsiku la 7 lisanathe, moti ngakhale kuti ena anaukira ulamuliro wake, Yehova adzakhala kuti wakwaniritsa cholinga chake chokhudza dziko lapansi ndiponso anthu pa nthawi yake.

      4 Kunena zoona, timagoma kwambiri tikaganizira nzeru zimenezi. M’pake kuti mtumwi Paulo analemba kuti ‘nzeru za Mulungu n’zozama.’ (Aroma 11:33) Tikamaphunzira njira zosiyanasiyana zimene Mulungu wasonyezera kuti ndi wanzeru, tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumakumbukira kuti tikhoza kungodziwako kambali kakang’ono chabe ka nzeru zochuluka za Yehova. (Yobu 26:14) Choyamba tiyeni tikambirane zimene khalidwe logometsali limatanthauza.

      Kodi Nzeru za Mulungu N’chiyani?

      5, 6. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kudziwa zinthu ndi kukhala wanzeru, nanga Yehova amadziwa zinthu zochuluka bwanji?

      5 Kukhala wanzeru n’kosiyana ndi kudziwa zinthu. Makompyuta akhoza kusunga zinthu zambiri koma sitinganene kuti ndi anzeru. Komabe kudziwa zinthu n’kogwirizana ndi kukhala wanzeru. (Miyambo 10:14) Mwachitsanzo, ngati mukudwala matenda enaake aakulu, ndipo mukufuna malangizo amene angakuthandizeni kuti muchire, kodi mungafunse kwa munthu yemwe sadziwa kwenikweni zachipatala kapenanso sazidziwa n’komwe? Ayi. Choncho kudziwa zinthu molondola n’kofunika kwambiri kuti munthu akhaledi wanzeru.

      6 Yehova amadziwa zinthu zochuluka kwambiri. Popeza ndi “Mfumu yamuyaya,” iye yekha ndi amene wakhalako kwa zaka zambirimbiri kuyambira kalekale. (Chivumbulutso 15:3) Ndipo amadziwa chilichonse chimene chakhala chikuchitika. Baibulo limati: “Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona. Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino moti ifeyo tidzayankha kwa Mulunguyo pa zochita zathu.” (Aheberi 4:13; Miyambo 15:3) Popeza ndi Mlengi, Yehova amadziwa bwino zimene analenga, ndipo wakhala akuona zochita zonse za anthu kuyambira pachiyambi. Amadziwanso zonse zimene zili mumtima mwa munthu. (1 Mbiri 28:9) Popeza anatipatsa ufulu wosankha, Yehova amasangalala akaona kuti tasankha zochita mwanzeru. Ndiponso iye ndi “Wakumva pemphero,” choncho anthu mamiliyoni ambirimbiri akamapemphera pa nthawi imodzi, iye amamva mapemphero onsewo. (Salimo 65:2) Ndipo n’zosachita kufunsa kuti Yehova amakumbukira chilichonse ndipo saiwala.

      7, 8. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi womvetsa zinthu, wozindikira komanso wanzeru?

      7 Sikuti Yehova amangodziwa zinthu. Amaonanso kugwirizana kwa zinthu komanso mmene mfundo zonse zikusonyezera chithunzi chonse cha nkhaniyo. Amapeza mfundo zofunika, kuziganizira, n’kugamulapo chifukwa choti amasiyanitsa chabwino ndi choipa komanso zofunika ndi zosafunika. Ndiponso sikuti iye amangoona zimene zikuoneka zokha koma amaonanso zomwe zili mumtima. (1 Samueli 16:7) Choncho Yehova amamvetsa ndiponso amazindikira mmene zinthu zilili ndipo zimenezi ndi zoposa kungodziwa zinthu. Koma kukhala ndi nzeru kumaposa zonsezi.

      8 Munthu wanzeru ndi amene amadziwa mfundo zokhudza nkhani inayake, kuonetsetsa kuti wamvetsa mfundozo kenako n’kuzigwiritsa ntchito moyenera. N’chifukwa chake m’Baibulo mawu akuti “nzeru” amatanthauza “kugwira ntchito yomwe ikuyenda bwino.” Choncho Yehova amagwiritsa ntchito zimene akudziwa komanso luso lake lomvetsa zinthu kuti akwaniritse cholinga chake ndipo nthawi zonse zimamuyendera. Yehova amadziwa ndiponso kumvetsa chilichonse moti amasankha zochita mwanzeru kwambiri komanso amapeza njira yabwino yozikwaniritsira. Apatu amasonyeza kuti ndi wanzeru kwambiri. Yehova amasonyeza kuti zimene Yesu ananena ndi zoona. Iye anati: “Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Zinthu zonse zimene Yehova analenga zimasonyeza kuti iye ndi wanzeru.

      Chilengedwe Chimasonyeza Kuti Yehova Ndi Wanzeru

      9, 10. (a) Kodi Yehova ali ndi nzeru zotani, nanga amazisonyeza bwanji? (b) Kodi selo limasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wanzeru?

      9 Kodi munachitapo chidwi ndi mmisiri amene amapanga zinthu zokongola zimene zimagwira ntchito bwino? Mmisiri woteroyo amasonyeza kuti ndi wanzeru kwambiri. (Ekisodo 31:1-3) Yehova ndi amene amapatsa munthu nzeru ndipo iye ndi wanzeru kuposa aliyense. Mfumu Davide inanena za Yehova kuti: “Ndimakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha. Ntchito zanu ndi zodabwitsa, ine ndikudziwa bwino zimenezi.” (Salimo 139:14) Zoonadi, tikamaphunzira kwambiri zokhudza mmene thupi la munthu linapangidwira, m’pamenenso timagoma kwambiri ndi nzeru za Yehova.

      10 Mwachitsanzo, moyo wanu unayamba pamene selo limodzi la dzira la amayi anu lomwe linakhwima linaphatikizana ndi umuna wa bambo anu. Pasanapite nthawi, selolo linayamba kugawikana. Inuyo, amene munakhalapo chifukwa cha kugawikana kumeneko, muli ndi maselo pafupifupi 100,000 biliyoni. Maselo amenewa ndi ang’onoang’ono kwambiri moti maselo pafupifupi 10,000 akhoza kukwanira pakanjere ka therere lobala. Komatu selo lililonse linapangidwa modabwitsa kwambiri. Selo lili ndi tinthu tambirimbiri m’kati mwake kuposa makina kapena fakitale ina iliyonse imene anthu apanga. Asayansi amati selo lili ngati mzinda umene uli ndi mpanda ndipo uli ndi mageti oyang’aniridwa bwino, olowera ndi otulukira. Mulinso misewu ndi magalimoto onyamula anthu, njira zolankhulirana, njira zopangira magetsi, malo otayira zinyalala ndi kukonzanso zinthu zogwiritsidwa kale ntchito, achitetezo komanso likulu la boma. Ndiponso m’maola ochepa chabe, selo likhoza kudzigawa pakati n’kukhala maselo awiri ofanana ndendende ndi loyamba lija.

      11, 12. (a) Kodi n’chiyani chimachititsa kuti maselo a mwana amene ali m’mimba azikhala osiyanasiyana, ndipo zimenezi zikugwirizana bwanji ndi Salimo 139:16? (b) Kodi ubongo wa munthu umasonyeza bwanji kuti ‘tinapangidwa modabwitsa’?

      11 Komabe sikuti maselo onse ndi ofanana. Maselo a mwana yemwe ali m’mimba mwa amayi ake akamapitiriza kugawikana, amayamba kugwira ntchito zosiyanasiyana. Ena amakhala maselo a mitsempha, ena a mafupa, a minofu, a magazi kapenanso a maso. Malangizo amene amathandiza kuti maselowa akhale osiyanasiyana chonchi amakhala mu DNA yomwe ili ngati laibulale ya selo. N’zochititsa chidwi kuti motsogoleredwa ndi mzimu, Davide anauza Yehova kuti: “Maso anu anandiona ngakhale pamene ndinali mluza. Ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.”​—Salimo 139:16.

      12 Ziwalo zina zathupi la munthu n’zovuta kwambiri kuzimvetsa. Mwachitsanzo, taganizirani za ubongo. Asayansi ena amati ubongo ndi wovuta kwambiri kuumvetsa pa zinthu zonse zimene anazitulukira m’chilengedwe. Uli ndi maselo a mitsempha pafupifupi 100 biliyoni omwe ndi ochuluka mwina kufanana ndi nyenyezi zimene zili mu mlalang’amba wathuwu. Lililonse la maselo amenewa limapanga nthambi masauzande ambirimbiri zomwe zimalumikizana ndi maselo ena. Asayansi amanena kuti ubongo wa munthu ukhoza kusunga zinthu zonse zimene zili m’malaibulale onse apadzikoli, mwinanso kuposa pamenepo. Ngakhale kuti akhala akuphunzira zokhudza ubongo ‘wopangidwa modabwitsawu,’ asayansi amavomera kuti mwina sangamvetse zonse zokhudza mmene ubongowu umagwirira ntchito.

      13, 14. (a) Kodi nyerere ndiponso zinthu zina za m’chilengedwe zimasonyeza bwanji kuti ndi “zanzeru mwachibadwa,” nanga zimenezi zimatiphunzitsa chiyani za Mlengi? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zinthu monga ulusi wa kangaude zinapangidwa “mwanzeru”?

      13 Komabe, anthu ndi chitsanzo chimodzi chokha chosonyeza kuti Yehova analenga zinthu mwanzeru. Lemba la Salimo 104:24 limati: “Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova! Zonsezo munazipanga mwanzeru. Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.” Zinthu zonse za m’chilengedwe zimasonyeza kuti Yehova ndi wanzeru. Mwachitsanzo, nyerere ndi “zanzeru mwachibadwa.” (Miyambo 30:24) Zimachita zinthu mwadongosolo m’magulu amene zimakhala. M’magulu ena, nyererezi zimasunga nsabwe za zomera n’kumapeza chakudya kuchokera ku nsabwezo ngati kuti ndi ziweto zake. Nyerere zina zimakhala ngati alimi ndipo zimalima tizomera tinatake tomwe sitichita maluwa komanso sitikhala ndi masamba. Zinthu zambiri zinalengedwa m’njira yoti zizichita zinthu modabwitsa kwambiri. Mwachitsanzo, ntchentche ikamauluka imagadabuzika ndipo ngakhale ndege yamakono kwambiri singathe kuchita zimenezo. Palinso mbalame zimene zimasamuka motsogoleredwa ndi nyenyezi, mphamvu ya maginito ya dziko kapenanso mapu amene zili nawo m’mutu. Asayansi ya zinthu zamoyo amatha zaka zambirimbiri akuphunzira zinthu zogometsa zimene nyamazi zimachita. N’zodziwikiratu kuti amene anapatsa nzeru zinthu zimenezi ndi wanzeru kwambiri.

      14 Asayansi aphunzira zambiri kuchokera ku zinthu za m’chilengedwe ndipo zinthuzi zimasonyeza kuti Yehova ndi wanzeru. Moti pali asayansi ena omwe amapanga zinthu potengera zinthu za m’chilengedwe. Mwachitsanzo, mungachite chidwi ndi kukongola kwa ulusi wa kangaude. Koma munthu yemwe ndi injiniya angaone zoposa pamenepo. Amaona kuti ulusiwo ndi chinthu chokonzedwa mwaluso kwambiri. Ulusi wina wa kangaude womwe umaoneka ngati wosalimba ndi wolimba kwambiri kuposa chitsulo kapenanso ulusi wa zovala zimene zipolopolo sizingathe kuboola. Kodi ulusi wa kangaude ndi wolimba bwanji? Tiyerekeze kuti mwakulitsa ulusiwu mpaka kukhala waukulu ngati ukonde umene anthu amagwiritsa ntchito popha nsomba. Ulusi wa chonchi ukhoza kuimitsa ndege yomwe ikuuluka. Zoonadi, Yehova anapanga zinthu zonsezi “mwanzeru.”

      Zithunzi: Nzeru za Yehova zikuonekera m’zinthu zimene analenga. 1. Ulusi wa kangaude. 2. Nyerere zanyamula masamba. 3. Mbalame zikuuluka.

      Kodi ndani anakonza zoti zinthu zamoyo padzikoli zizikhala “zanzeru mwachibadwa”?

      Zinthu Zakumwamba Zimasonyezanso Nzeru za Mulungu

      15, 16. (a) Kodi nyenyezi zimasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wanzeru? (b) Kodi zimene Yehova amachita popatsa angelo ntchito yokwanira zimasonyeza bwanji kuti ndi wanzeru?

      15 Nzeru za Yehova zimaoneka m’zinthu zonse zimene anapanga. Nyenyezi zakumwamba, zimene tinakambirana kwambiri m’Mutu 5, zinaikidwa pamalo ake mwadongosolo. Chifukwa chakuti Yehova ndi wanzeru, anapanga “malamulo amene zinthu zakuthambo zimatsatira” moti nyenyezi zinaikidwa m’milalang’amba. (Yobu 38:33) Milalang’ambayo inaikidwa m’magulu ndipo magulu amenewo anaikidwanso m’magulu ena akuluakulu. M’pake kuti Yehova amanena kuti zinthu zakumwamba zimenezi ndi “gulu la nyenyezi.” (Yesaya 40:26) Komabe, pali gulu linanso limene limasonyeza bwino kuti Yehova ndi wanzeru.

      16 Monga tinaonera m’Mutu 4, Mulungu ali ndi dzina la udindo lakuti “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba” chifukwa choti iye ndi Mtsogoleri Wamkulu wa gulu lalikulu kwambiri la angelo. Zimenezi zikusonyeza kuti iye ndi wamphamvu kwambiri. Koma ndi umboni wosonyezanso kuti ndi wanzeru. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani mfundo iyi: Nthawi zonse Yehova ndi Yesu amakhala akugwira ntchito. (Yohane 5:17) Choncho n’zomveka kuganiza kuti angelo, omwe ndi atumiki a Wam’mwambamwamba, nawonso amakhala otanganidwa nthawi zonse. Ndipo kumbukirani kuti angelo ndi anzeru komanso amphamvu kwambiri kuposa anthu. (Aheberi 1:7; 2:7) Komatu kwa zaka mabiliyoni, Yehova wakhala akupatsa angelo onse ntchito yokwanira yomwe amaigwira mosangalala. Iwo “amamvera mawu ake komanso kuchita zimene wanena.” (Salimo 103:20, 21) Zimenezitu zikusonyeza kuti Yehova ali ndi nzeru zochuluka kwambiri.

      “Wanzeru Yekhayo”

      17, 18. N’chifukwa chiyani Baibulo limatchula Yehova kuti “wanzeru yekhayo,” nanga n’chifukwa chiyani timagoma ndi nzeru zake?

      17 Tikaganizira zonsezi, n’zosadabwitsa kuti Baibulo limasonyeza kuti Yehova ali ndi nzeru zopanda malire. Mwachitsanzo, limatchula Yehova kuti “wanzeru yekhayo.” (Aroma 16:27) Yehova yekha ndi amene ali ndi nzeru pa chilichonse. Nzeru zenizeni zimachokera kwa iye. (Miyambo 2:6) N’chifukwa chake Yesu, ngakhale kuti ndi wanzeru kwambiri pa zonse zimene Yehova analenga, sankadalira nzeru zake koma ankalankhula zimene Atate wake anamuuza.​—Yohane 12:48-50.

      18 Mtumwi Paulo anafotokoza kuti nzeru za Yehova ndi zapadera kwambiri. Iye anati: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zovuta kuzimvetsa, ndipo ndani angatulukire njira zake?” (Aroma 11:33) Poyamba ndi mawu akuti “ndithudi,” Paulo anasonyeza kuti anakhudzidwa kwambiri komanso anagoma ndi nzeru za Yehova. Mawu a Chigiriki amene anagwiritsa ntchito palembali omwe anawamasulira kuti “kuzama,” ndi ofanana kwambiri ndi mawu akuti “phompho.” Choncho zimene Paulo ananena zimatithandiza kuona m’maganizo zimene ankatanthauza. Tikamaganizira nzeru za Yehova, zimakhala ngati tikuyang’ana m’chidzenje chozama kwambiri chomwe pansi pake sitingathe kuonapo, chachikulu kwambiri moti sitingathe kudziwa bwino kukula kwake, ndiponso chokanika kuchifotokoza ngakhalenso kuchijambula bwinobwino. (Salimo 92:5) Kudziwa zimenezi kuyeneratu kutichititsa kuti tikhale odzichepetsa.

      19, 20. (a) N’chifukwa chiyani chiwombankhanga ndi chizindikiro choyenera cha nzeru za Mulungu? (b) Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amatha kuoneratu zinthu za m’tsogolo?

      19 Yehova ndi “wanzeru yekhayo” m’njira inanso: Ndi iye yekha amene angathe kudziwiratu za m’tsogolo. Kumbukirani kuti chiwombankhanga, chomwe chimaona patali, ndi chizindikiro cha nzeru za Yehova. Ziwombankhanga za mtundu winawake zimangolemera makilogalamu 5 okha, komatu maso ake amakhala akuluakulu kuposa a munthu wamkulu. Maso a chiwombankhanga ndi akuthwa kwambiri moti chili m’mwamba chimatha kuona kanthu kakang’ono kwambiri kamene kali pansi pamtunda wa mamita mahandiredi ochuluka, mwinanso makilomita kumene. Ponena za chiwombankhanga, Yehova anati: “Maso ake amaona kutali kwambiri.” (Yobu 39:29) Mofanana ndi zimenezi, Yehova akhoza ‘kuona kutali kwambiri,’ kapena kuti kudziwiratu zakutsogolo.

      20 M’Baibulo muli maulosi ambirimbiri amene amasonyeza kuti Yehova akhoza kudziwiratu za m’tsogolo. Linaneneratu amene adzapambane pa nkhondo zina, kuyamba ndiponso kutha kwa maulamuliro amphamvu padziko lonse komanso njira zimene akukuluakulu asilikali adzagwiritse ntchito pa nkhondo. Nthawi zambiri Baibulo linkaneneratu zimenezi kudakali zaka mahandiredi angapo.​—Yesaya 44:25 mpaka 45:4; Danieli 8:2-8, 20-22.

      21, 22. (a) N’chifukwa chiyani palibe chifukwa chomveka chonenera kuti Yehova amaoneratu zonse zimene mudzasankhe kuchita pa moyo wanu? Perekani chitsanzo. (b) Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova sagwiritsa ntchito mphamvu zake mopanda chikondi?

      21 Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu anaoneratu kale zimene mudzasankhe pa moyo wanu? Anthu ena amene amakhulupirira kuti Mulungu anakonzeratu zonse zimene zidzachitike m’tsogolo angayankhe kuti inde. Koma maganizo amenewa amachititsa kuti Yehova azioneka ngati alibe nzeru chifukwa amasonyeza kuti sangalamulire luso lake lotha kudziwiratu zam’tsogolo. Mwachitsanzo, ngati mutakhala ndi luso loimba, kodi nthawi zonse mungamangoimba? Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti simukuganiza bwino. Mofanana ndi zimenezi, Yehova ali ndi luso lotha kudziwiratu zam’tsogolo, koma sikuti amaligwiritsa ntchito nthawi zonse. Atamachita zimenezi, angakhale kuti sakulemekeza ufulu wosankha zochita umene anatipatsa. Komatu ufulu umenewu ndi mphatso yamtengo wapatali imene sadzatilanda.​—Deuteronomo 30:19, 20.

      22 Anthu amene amakhulupirira kuti Yehova anakonzeratu zonse zimene zimachitika, amamuimba mlandu kuti ndi amene amachititsa zoipa zonse ndipo amaganiza kuti iye amagwiritsa ntchito mphamvu zake mopanda chikondi. Komatu limeneli ndi bodza lamkunkhuniza. Baibulo limaphunzitsa kuti Yehova “ali ndi mtima wanzeru.” (Yobu 9:4) Izi sizikutanthauza kuti ali ndi mtima weniweni. Koma nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti mtima ponena za munthu weniweniyo kuphatikizapo zolinga zake komanso makhalidwe ake monga chikondi. Choncho mofanana ndi makhalidwe ake ena, nzeru za Yehova zimatsogoleredwa ndi chikondi.​—1 Yohane 4:8.

      23. Kodi tiyenera kuchita chiyani popeza Yehova ndi wanzeru kwambiri kuposa ifeyo?

      23 Nzeru za Yehova n’zodalirika kwambiri. Iye ndi wanzeru kwambiri kuposa ife. N’chifukwa chake Mawu ake amatilimbikitsa kuti: “Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usamadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzimukumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.” (Miyambo 3:5, 6) Tsopano tiyeni tiphunzire zambiri zokhudza nzeru za Yehova, kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu wanzeru zonse ameneyu.

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Yobu 28:11-28 N’chifukwa chiyani tinganene kuti nzeru za Mulungu ndi zamtengo wapatali, nanga kuganizira zimenezi kungatithandize bwanji?

      • Salimo 104:1-25 Kodi chilengedwe chimasonyeza bwanji nzeru za Yehova, nanga mumamva bwanji mukaganizira zimenezi?

      • Miyambo 3:19-26 Kodi n’chiyani chingamatichitikire tsiku lililonse ngati titamaganizira nzeru za Yehova komanso kuzigwiritsa ntchito?

      • Danieli 2:19-28 N’chifukwa chiyani Yehova akutchedwa Woulula zinsinsi, nanga tingatani ngati timaona kuti nzeru zake zopezeka m’maulosi a m’Baibulo ndi zamtengo wapatali?

  • “Mawu a Mulungu” Amasonyeza Kuti Iye Ndi Wanzeru
    Yandikirani Yehova
    • Wolemba Baibulo akulemba pampukutu.

      MUTU 18

      “Mawu a Mulungu” Amasonyeza Kuti Iye Ndi Wanzeru

      1, 2. Kodi ndi “kalata” iti imene Yehova anatilembera, ndipo n’chifukwa chiyani?

      KODI mukukumbukira nthawi yomaliza imene munalandira kalata yochokera kwa munthu amene mumam’konda yemwe amakhala kutali? Timasangalala kwambiri tikalandira kalata yochokera kwa munthu wotereyu yokhala ndi mawu ochokera pansi pa mtima. Timasangalala kumva kuti ali bwanji, zimene zikumuchitikira ndiponso zimene akufuna kuchita. Kulankhulana m’njira imeneyi kumachititsa kuti anthu azikondana kwambiri ngakhale kuti akukhala motalikirana.

      2 N’chifukwa chake timasangalala kwambiri kulandira uthenga wolembedwa wochokera kwa Mulungu amene timamukonda. Tinganene kuti Yehova anatilembera “kalata,” pamene anatipatsa Mawu ake, Baibulo. M’Mawu akewa amatiuza zokhudza iyeyo, zimene anachita, zimene akufuna kuchita komanso zina zambiri. Yehova anatipatsa Mawu ake chifukwa amafuna kuti tikhale anzake apamtima. Njira yolankhulira nafe imene Mulungu wathu wanzeru zonse anasankhayi, ndi yabwino kwambiri. Mmene Baibulo linalembedwera ndiponso zimene zili m’Baibulo, zimasonyeza kuti iye ndi wanzeru kwambiri.

      N’chifukwa Chiyani Anachita Kulemba?

      3. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito njira iti popereka Chilamulo kwa Mose?

      3 Ena angafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova sanagwiritse ntchito njira yochititsa chidwi kwambiri polankhula ndi anthu? Mwachitsanzo, bwanji sanalankhule nafe mwachindunji kuchokera kumwamba?’ Nthawi zina Yehova ankalankhuladi ndi anthu kuchokera kumwamba kudzera mwa angelo. Mwachitsanzo, anachita zimenezi pamene ankapereka Chilamulo kwa Aisiraeli. (Agalatiya 3:19) Mawu amene anachokera kumwambawo anali ochititsa mantha kwambiri moti Aisiraeli anapempha Yehova kuti asalankhule nawonso m’njira imeneyi, koma kudzera mwa Mose. (Ekisodo 20:18-20) Choncho Yehova analankhula ndi Mose ndipo anamuuza malamulo onse oposa 600 omwe anali m’Chilamulo.

      4. Fotokozani chifukwa chake njira yongouzana pakamwa sikanakhala yodalirika popereka malamulo a Mulungu ku mibadwo yonse.

      4 Koma kodi chikanachitika n’chiyani Chilamulocho chikanapanda kulembedwa? Kodi Mose akanatha kukumbukira mawu onse a m’Chilamulocho, chomwe chinali ndi mfundo zambirimbiri, n’kuwafotokozera Aisiraeli mosalakwitsa chilichonse? Nanga bwanji mibadwo yam’tsogolo? Kodi iwo akanangodalira zowauza ndi pakamwa? Imeneyo sikanakhala njira yodalirika yothandiza anthu kudziwa molondola malamulo a Mulungu. Taganizirani zomwe zingachitike ngati mutakhala ndi nkhani yoti mufotokozere anthu omwe ali pa mzere wautali. Mwafotokozera munthu woyambirira kuti nayenso afotokozere mnzake mpaka nkhaniyo ikafike kwa munthu wakumapeto. Zimene munthu womalizirayo angamve zingakhale zosiyana kwambiri ndi mmene nkhaniyo inalili poyamba. Koma Chilamulo cha Mulungu sichinakumane ndi vuto limeneli.

      5, 6. Kodi Yehova anauza Mose kuti achite chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo ndi mphatso yamtengo wapatali?

      5 Chifukwa cha nzeru zake, Yehova anasankha kuti mawu ake alembedwe. Anauza Mose kuti: “Ulembe mawuwa chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe komanso Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.” (Ekisodo 34:27) Chimenechi chinali chaka cha 1513 B.C.E. ndipo ndi chaka chimene Baibulo linayamba kulembedwa. Kwa zaka 1,610 zotsatira, Yehova “ankalankhula . . . m’njira zosiyanasiyana” kwa anthu pafupifupi 40 amene kenako analemba Baibulo. (Aheberi 1:1) Pa nthawi yomweyinso alembi odzipereka ankakopera zolembedwazo mosamala ndiponso molondola kwambiri kuti uthenga wa m’Baibulo usungike.​—Ezara 7:6; Salimo 45:1.

      6 Kunena zoona, Baibulo ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova. Kodi munalandirapo kalata yomwe inakusangalatsani kwambiri mwina chifukwa choti inakulimbikitsani moti munaisunga n’kumaiwerenga mobwerezabwereza? Ndi mmenenso zilili ndi “kalata” imene Yehova anatilemberayi. Chifukwa chakuti Yehova analemba mawu ake, timawawerenga nthawi zonse n’kumaganizira mozama zomwe tawerengazo. (Salimo 1:2) ‘Malembawa amatilimbikitsa’ nthawi iliyonse imene tikufunika kulimbikitsidwa.​—Aroma 15:4.

      N’chifukwa Chiyani Anagwiritsa Ntchito Anthu?

      7. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi wanzeru pogwiritsa ntchito anthu kuti alembe Mawu ake?

      7 Popeza ndi wanzeru, Yehova anagwiritsa ntchito anthu kuti alembe Mawu ake. Taganizirani izi: Yehova akanagwiritsa ntchito angelo kuti alembe Baibulo, kodi bwenzi likutifika pamtima ngati mmene zilili panopa? Angelo akanafotokoza zokhudza Yehova m’njira yapamwamba kwambiri ngati mmene iwowo amamudziwira. Akanafotokozanso zimene amachita posonyeza kudzipereka kwa iye ndiponso zokhudza anthu ena okhulupirika. Koma kodi zomwe angelo akanafotokozazo tikanatha kuzimvetsa? Pajatu angelo ndi angwiro, amadziwa zambiri komanso ndi amphamvu kuposa ifeyo.​—Aheberi 2:6, 7.

      8. Kodi Yehova analola kuti anthu amene analemba Baibulo achite chiyani? (Onaninso mawu am’munsi.)

      8 Pogwiritsa ntchito anthu kuti alembe Mawu ake, Yehova anatipatsa buku ‘louziridwa ndi Mulungu’ koma lofotokoza zinthu zowafika pamtima anthu. Buku lotereli ndi limenedi timafunikira. (2 Timoteyo 3:16) Koma kodi anachita bwanji zimenezi? Zikuoneka kuti nthawi zambiri, ankalola anthu amene ankalembawo kugwiritsa ntchito luso lawo loganiza posankha “mawu osangalatsa” ndiponso “olondola a choonadi.” (Mlaliki 12:10, 11) N’chifukwa chake nkhani za m’Baibulo zinalembedwa mosiyanasiyana ndipo zimasonyeza makhalidwe a wolembayo komanso mmene zinthu zinalili pa moyo wake.a Komabe anthu amenewa “analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Petulo 1:21) Choncho zimene analembazo ndi “mawu a Mulungu.”​—1 Atesalonika 2:13.

      “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu”

      9, 10. N’chifukwa chiyani uthenga wa m’Baibulo umatikhudza mtima kwambiri?

      9 Baibulo ndi losangalatsa komanso uthenga wake umatifika pamtima chifukwa choti linalembedwa ndi anthu. Olembawo anali anthu ngati ife tomwe. Popeza sanali angwiro, ankakumana ndi mayesero komanso mavuto omwe nafenso timakumana nawo. Nthawi zina mzimu wa Yehova unkawatsogolera kuti alembe mmene akumvera ndiponso mavuto amene akukumana nawo. (2 Akorinto 12:7-10) Choncho ankalemba mosonyeza kuti nkhaniyo ikuchitikira iwowo ndipo palibe mngelo yemwe akanachita zimenezi.

      10 Mwachitsanzo, taganizirani za Davide mfumu ya Isiraeli. Atachita machimo akuluakulu, analemba nyimbo yofotokoza mmene ankamvera ndipo anapempha Mulungu kuti amukhululukire. Iye analemba kuti: “Mundisambitse bwinobwino n’kuchotsa cholakwa changa, ndiyeretseni ku tchimo langa. Chifukwa zolakwa zanga ndikuzidziwa bwino, ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse. Taonani! Ndinabadwa ndili wochimwa, ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga. Musandichotse pamaso panu n’kunditaya. Ndipo musandichotsere mzimu wanu woyera. Nsembe zimene Mulungu amasangalala nazo ndi kudzimvera chisoni mumtima. Inu Mulungu, simudzakana mtima wosweka ndi wophwanyika.” (Salimo 51:2, 3, 5, 11, 17) Tikamawerenga zimenezi timachita kudziwiratu kuti Davide ankadzimvera chisoni kwambiri. Munthu yemwe si wangwiro yekha ndi amene akananena mawu ochokera pansi pa mtimawa.

      N’chifukwa Chiyani Limanena za Anthu?

      11. Kodi m’Baibulo muli nkhani zotani zomwe zinalembedwa “kuti zitilangize”?

      11 Palinso chinthu china chimene chimapangitsa Baibulo kukhala losangalatsa. Muli nkhani zambiri zomwe zimanena za anthu enieni, amene ankatumikira Mulungu komanso omwe sankamutumikira. Timawerenga zokhudza mavuto amene anakumana nawo ndiponso zinthu zosangalatsa zomwe zinawachitikira. Timaonanso zotsatira za zimene anasankha pa moyo wawo. Nkhanizi zinalembedwa “kuti zitilangize.” (Aroma 15:4) Pogwiritsa ntchito zitsanzo za anthu amenewa, Yehova amatiphunzitsa motifika pamtima. Taonani zitsanzo izi.

      12. Kodi nkhani za m’Baibulo zonena za anthu osakhulupirika zimatithandiza bwanji?

      12 Baibulo limatiuza za anthu osakhulupirika ndiponso oipa komanso zomwe zinawachitikira. Tikamawerenga nkhanizi, timaona mmene munthu amasonyezera makhalidwe oipa, choncho timamvetsa mosavuta. Mwachitsanzo, Baibulo likanatha kungofotokoza kuti si bwino kukhala wosakhulupirika kwa mnzathu. Koma kodi mumamva bwanji mukamawerenga mmene Yudasi anasonyezera kusakhulupirika popereka Yesu? (Mateyu 26:14-16, 46-50; 27:3-10) Nkhani ngati zimenezi zimatikhudza mtima kwambiri ndipo zimatithandiza kuzindikira makhalidwe oipa n’kumawapewa.

      13. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kuti timvetse zokhudza makhalidwe abwino n’kumawasonyeza?

      13 Baibulo limafotokozanso za atumiki a Mulungu ambiri okhulupirika. Timawerenga zokhudza kudzipereka ndiponso kukhulupirika kwawo. Timaona zitsanzo za anthu omwe anasonyeza makhalidwe amene timafunika kukhala nawo kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Mwachitsanzo, taganizirani za chikhulupiriro. Baibulo limafotokoza tanthauzo la chikhulupiriro ndiponso kuti n’chofunika kwambiri kuti tizisangalatsa Mulungu. (Aheberi 11:1, 6) Koma m’Baibulo mulinso zitsanzo za anthu amene anasonyeza chikhulupiriro. Taganizirani chikhulupiriro chimene Abulahamu anasonyeza pamene ankafuna kupereka nsembe Isaki. (Genesis, chaputala 22; Aheberi 11:17-19) Nkhani ngati zimenezi zimatithandiza kumvetsa bwino tanthauzo la “chikhulupiriro.” Choncho sikuti Yehova amangotiuza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino, koma amatipatsanso zitsanzo za anthu omwe anasonyeza makhalidwewa. Zimenezi zimasonyeza kuti iye ndi wanzeru kwambiri.

      14, 15. Kodi Baibulo limatiuza chiyani za mayi wina amene anafika pakachisi, ndipo nkhani imeneyi imatiphunzitsa chiyani za Yehova?

      14 Nkhani zokhudza anthu ena zimene zili m’Baibulo nthawi zambiri zimatithandiza kuti timudziwe bwino Yehova. Mwachitsanzo, taganizirani za nkhani yokhudza mayi wina yemwe Yesu anamuona pakachisi. Yesu anakhala pansi pafupi ndi mosungiramo zopereka ndipo ankaona anthu akuponya zopereka zawo. Pankafika anthu ambiri olemera n’kumapereka kuchokera ‘pa zochuluka zimene anali nazo.’ Koma Yesu anayamba kuyang’anitsitsa mkazi wina wamasiye yemwe analinso wosauka. Mayiyu anapereka “timakobidi tiwiri tating’ono, tochepa mphamvu kwambiri.”b Iye anali ndi ndalama zokhazi basi. Zimene Yesu ananena zinasonyeza mmene Yehova ankamuonera mayiyo. Iye anati: “Mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa ena onse amene aponya ndalama moponyera zoperekamo.” Mogwirizana ndi mawu amenewa, mkaziyu anaponya zambiri kuposa kuphatikiza pamodzi zimene ena onse anaponya.​—Maliko 12:41-44; Luka 21:1-4; Yohane 8:28.

      15 Kodi si zolimbikitsa kuti pa anthu onse amene anabwera kukachisi tsiku limenelo, mkazi wamasiyeyu ndi amene Yesu anachita naye chidwi komanso anatchulidwa m’Baibulo? Chitsanzo chimenechi chimatiphunzitsa kuti Yehova ndi Mulungu amene amayamikira. Amasangalala ndi zimene timamupatsa popanda kuziyerekezera ndi zochuluka zimene ena angathe kupereka. Apatu Yehova anagwiritsa ntchito njira yabwino kwambiri yotiphunzitsira mfundo ya choonadi yosangalatsayi.

      Zimene M’Baibulo Mulibe

      16, 17. Kodi Yehova anasonyezanso bwanji kuti ndi wanzeru tikaganizira zimene anasankha kuti zisalembedwe m’Mawu ake?

      16 Mukamalemba kalata yopita kwa munthu amene mumamukonda, n’zosatheka kulembamo mfundo zonse zimene muli nazo. Choncho mumasankha mwanzeru zoti mulembe. Nayenso Yehova anasankha zochitika komanso anthu oti nkhani zawo zilembedwe m’Mawu ake. Koma sikuti Baibulo limafotokoza mfundo zonse zokhudza nkhani zimenezi. (Yohane 21:25) Mwachitsanzo, Baibulo likamanena zokhudza chiweruzo chimene Mulungu anapereka, zimene limafotokoza sizingayankhe funso lililonse lomwe tingakhale nalo. Pamene Yehova anasankha kuti zinthu zina zisalembedwe m’Mawu ake, anasonyezanso kuti ndi wanzeru. N’chifukwa chiyani tikutero?

      17 Baibulo linalembedwa mwa njira yoti lizitithandiza kudziwa kuti ndife munthu wotani. Lemba la Aheberi 4:12 limati: “Mawu [kapena kuti uthenga] a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu . . . amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” Uthenga wa m’Baibulo umatifika pamtima n’kutithandiza kudziwa zimene timaganiza komanso zolinga zathu pochita zinthu. Anthu amene amawerenga Baibulo pongofuna kulipezera zifukwa, nthawi zambiri amakhumudwa chifukwa choti silinafotokoze zambiri pa nkhani inayake. Mwinanso angamakayikire ngati Yehova alidi wachikondi, wanzeru komanso wachilungamo.

      18, 19. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhumudwa ngati nkhani ina ya m’Baibulo yachititsa kuti tikhale ndi mafunso amene sitingapeze mayankho ake nthawi yomweyo? (b) Kodi timafunika kuchita chiyani kuti timvetse Mawu a Mulungu, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti umenewu ndi umboni wakuti Yehova ndi wanzeru kwambiri?

      18 Koma mosiyana ndi zimenezi, tikamaphunzira Baibulo mosamala kwambiri ndiponso tili ndi zolinga zabwino, timatha kumudziwa bwino Yehova mogwirizana ndi zimene Baibulo lonse limanena zokhudza iyeyo. Choncho sitikhumudwa ngati nkhani ina yachititsa kuti tikhale ndi mafunso amene sitingapeze mayankho ake nthawi yomweyo. Mwachitsanzo, ngati tikusonkhanitsa pamodzi mapisi a chithunzi chachikulu kuti tipangenso chithunzicho, mwina poyamba sitingapeze pisi ina kapenanso sitingadziwe kuti kapisi kena tikaike pati. Komatu, tikhoza kukhala kuti tasonkhanitsa mapisi okwanira amene angatithandize kudziwa mmene chithunzi chonsecho chimaonekera. Mofanana ndi zimenezi, tikamaphunzira Baibulo, pang’ono ndi pang’ono timayamba kudziwa kuti Yehova ndi wotani ngakhale kuti pangakhale zina zomwe sitinazidziwe. Ngakhale kuti poyamba sitingamvetse nkhani inayake kapenanso kuona kuti ikugwirizana bwanji ndi makhalidwe a Mulungu, zinthu zokhudza Yehova zimene taphunzira kale m’Baibulo zatithandiza kuona kuti nthawi zonse iye amachita zinthu mwachikondi komanso mwachilungamo.

      19 Choncho kuti timvetse Mawu a Mulungu, tiyenera kuwawerenga ndi kuwaphunzira tili ndi maganizo oyenera komanso mtima wofuna kuphunzira zinthu. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ndi wanzeru kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Anthu anzeru akhoza kulemba mabuku amene “anthu anzeru ndi ozindikira” okha ndi amene angawamvetse. Koma Yehova yekha, mwanzeru zake, ndi amene angathe kulemba buku limene angalimvetse ndi anthu a mitima yabwino okha.​—Mateyu 11:25.

      Buku la “Nzeru Zopindulitsa”

      20. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova yekha ndi amene angatiuze zoyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri, nanga m’Baibulo muli chiyani chimene chingatithandize?

      20 M’Mawu ake, Yehova amatiuza zoyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri. Popeza ndi Mlengi wathu, amadziwa bwino zimene timafunikira kuposa mmene ifeyo timadziwira. Munthu aliyense amafuna kukondedwa, kukhala wosangalala, kukhala ndi banja labwino komanso kukhala ndi anzake apamtima. Ndipo zimenezi sizinasinthe kuchokera pamene Baibulo linalembedwa. M’Baibulo muli “nzeru zopindulitsa” zomwe zingatithandize kukhala ndi moyo wabwino. (Miyambo 2:7) Gawo lililonse la bukuli lili ndi mutu umene ukusonyeza mmene tingagwiritsire ntchito malangizo a nzeru a m’Baibulo. Koma tiyeni tione chitsanzo chimodzi.

      21-23. Kodi ndi malangizo anzeru ati amene angatithandize kuti tisamapitirize kukwiyira ena komanso kuwasungira chakukhosi?

      21 Kodi munaonapo kuti anthu amene amasunga chakukhosi komanso amene amapitirizabe kukhala okhumudwa nthawi zambiri amadzivulaza okha? Tikamapitiriza kukwiyira munthu, zimakhala ngati tanyamula chimtolo cholemera. Maganizo athu onse amakhala pa zimenezo ndipo timasowa mtendere komanso sitikhala osangalala. Asayansi anapeza kuti munthu yemwe amapitiriza kukwiya akhoza kudwala matenda amtima komanso ena okhalitsa. Kalekale kwambiri asayansi asanatulukire zimenezi, Baibulo linapereka malangizo anzeru akuti: “Usapse mtima ndipo uzipewa kukwiya.” (Salimo 37:8) Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?

      22 Mawu a Mulungu amapereka malangizo anzeru awa: “Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.” (Miyambo 19:11) Kuzindikira ndi luso lotha kudziwa mfundo zina osangoti zokhazo zimene zikuonekeratu. Munthu wozindikira amathanso kumvetsa chifukwa chake mnzake analankhula kapena kuchita zinazake. Tikayesetsa kumvetsa zolinga za munthu, mmene akumvera komanso mmene zinthu ziliri pa moyo wake, zingatithandize kuti tisamuganizire zoipa kapena kumukwiyira.

      23 Baibulo limatipatsanso malangizo akuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.” (Akolose 3:13) Mawu akuti “pitirizani kulolerana” akusonyeza kuti tiyenera kukhala oleza mtima n’kumayesetsa kuti tisamakhumudwe ngakhale kuti anthu ena ali ndi makhalidwe enaake omwe satisangalatsa. Zimenezi zingatithandize kuti tizipitirizabe kuchita nawo zinthu m’malo mowakwiyira. Mawu akuti “kukhululukirana” angatanthauzenso kuti sitiyenera kupitiriza kukwiyira munthu. Mulungu wathu wanzeru amadziwa kuti timafunika kukhululukira ena pakakhala chifukwa chomveka chowakhululukira. Sikuti zimenezi zimangothandiza iwowo, koma zimathandizanso ifeyo kuti tikhale ndi mtendere wamumtima. (Luka 17:3, 4) Zonsezi zikusonyeza kuti m’Mawu a Mulungu muli nzeru zothandiza kwambiri.

      24. Kodi chimachitika n’chiyani tikamatsatira nzeru za Mulungu pa moyo wathu?

      24 Chifukwa chakuti amatikonda kwambiri, Yehova anakonza zoti azilankhula nafe. Anasankha njira yabwino kwambiri yochitira zimenezi yomwe ndi kutilembera “kalata” pogwiritsa ntchito anthu omwe ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera. M’kalata imeneyi timapezamo nzeru za Yehova ndipo nzeruzi ndi “zodalirika kwambiri.” (Salimo 93:5) Tikamazitsatira pa moyo wathu komanso kuuzako ena, timakhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu wathu wanzeru zonse. M’mutu wotsatira, tidzakambirana chitsanzo china chosonyeza kuti Yehova ali ndi nzeru zotha kuoneratu zam’tsogolo ndiponso kukwaniritsa zimene akufuna.

      a Mwachitsanzo, Davide yemwe anali m’busa, anagwiritsa ntchito zitsanzo za zimene zimachitika ku ubusa. (Salimo 23) Mateyu, yemwe poyamba anali wokhometsa msonkho, nthawi zambiri ankatchula manambala ndiponso kuchuluka kwa ndalama. (Mateyu 17:27; 26:15; 27:3) Luka, yemwe anali dokotala, anagwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti ankadziwa zachipatala.​—Luka 4:38; 14:2; 16:20.

      b Ndalama zimenezi zinali timalepitoni, ndalama ya Chiyuda yaing’ono kwambiri imene ankagwiritsa ntchito pa nthawiyo. Munthu ankangofunika kugwira ntchito 15 minitsi kuti alandire malepitoni awiri. Tindalama tiwiri timeneti tinali tosakwanira kugula ngakhale mpheta imodzi yomwe inali mbalame yotchipa kwambiri imene anthu osauka ankadya.

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Miyambo 2:1-6 Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipeze nzeru za m’Mawu a Mulungu?

      • Miyambo 2:10-22 Kodi kutsatira malangizo anzeru a m’Baibulo kungatithandize bwanji?

      • Aroma 7:15-25 Kodi mavesiwa akusonyeza bwanji kuti Mulungu anachita bwino kugwiritsa ntchito anthu kuti alembe Mawu ake?

      • 1 Akorinto 10:6-12 Kodi tingaphunzire chiyani pa zitsanzo zotichenjeza za m’Baibulo zokhudza Aisiraeli?

  • ‘Nzeru ya Mulungu Imaonekera mu Chinsinsi Chopatulika’
    Yandikirani Yehova
    • Abulahamu akuyang’ana kumwamba komwe kuli nyenyezi.

      MUTU 19

      ‘Nzeru ya Mulungu Imaonekera mu Chinsinsi Chopatulika’

      1, 2. Kodi ndi “chinsinsi chopatulika” chiti chimene tiyenera kufunitsitsa kuchidziwa, ndipo n’chifukwa chiyani?

      ANTHUFE tikakhala kuti tikudziwa kapena kumvetsa zinthu zina zimene ena sakuzidziwa, nthawi zambiri zimativuta kusunga chinsinsi. Komabe Baibulo limati: “Kusunga chinsinsi ndi ulemerero wa Mulungu.” (Miyambo 25:2) Yehova, yemwe ndi Wolamulira Wamkulu ndiponso Mlengi, saulula zinthu zina kwa anthu mpaka nthawi yake itafika.

      2 Komabe pali chinsinsi china chochititsa chidwi chimene Yehova anachiulula m’Mawu ake. Chimatchedwa kuti “chinsinsi chopatulika chokhudza chifuniro [cha Mulungu].” (Aefeso 1:9) Kudziwa chinsinsi chimenechi kungakuthandizeni kwambiri kuposa mmene zimakhalira tikangodziwa nkhani inayake yachinsinsi. Kungakuthandizeni kuti mudzapulumuke komanso kuti mumvetse bwino mfundo yoti Yehova ndi wanzeru kwambiri.

      Ankachiulula Pang’onopang’ono

      3, 4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ulosi wa pa Genesis 3:15 unali uthenga wachiyembekezo, ndipo unali ndi “chinsinsi chopatulika” chiti?

      3 Cholinga cha Yehova chinali choti dziko lonse lapansi lidzakhale Paradaiso momwe muzidzakhala anthu angwiro. Komabe Adamu ndi Hava atachimwa, zinaoneka ngati cholingachi chalephereka. Koma nthawi yomweyo Mulungu anapeza njira yoti adzathetsere vutoli. Ananena kuti: “Ndidzaika chidani pakati pa iwe [njoka] ndi mkaziyo, komanso pakati pa mbadwa yako ndi mbadwa yake. Mbadwa ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.”​—Genesis 3:15.

      4 Amenewatu anali mawu ovuta kuwamvetsa. Kodi mkaziyu anali ndani? Kodi njokayo inali ndani? Nanga ndi ndani amene anali “mbadwa” imene idzaphwanye mutu wa njoka? Mayankho amene Adamu ndi Hava akanakhala nawo pa mafunsowa anali ongoganizira. Komabe, zimene Mulungu ananenazi unali uthenga wachiyembekezo kwa ana okhulupirika a anthu awiri osakhulupirikawa. Ana awowo akanakhala otsimikizira kuti Yehova adzathetsa zoipa zonse, uchimo ndipo zofuna zake zidzachitika. Koma kodi zimenezi zinali zoti zidzachitika bwanji? Pamenepa m’pamene panagona chinsinsi. Baibulo limati chinsinsi chimenechi ndi “nzeru ya Mulungu yomwe ndi nzeru yobisika, imene inaonekera mu chinsinsi chopatulika.”​—1 Akorinto 2:7.

      5. Perekani chitsanzo chosonyeza chifukwa chake Yehova anaulula chinsinsi chake pang’onopang’ono.

      5 Popeza Yehova ndi “Woulula zinsinsi,” anakonza zoti pakapita nthawi adzaulule mfundo zofunikira zokhudza chinsinsi chimenechi. (Danieli 2:28) Koma anakonza zoti azidzachita zimenezi pang’onopang’ono. Mwachitsanzo, taganizirani zimene bambo wachikondi angayankhe mwana wake wamng’ono atamufunsa kuti, “Kodi adadi, ineyo ndinachokera kuti?” Bambo wanzeru amauza mwanayo zinthu zokhazo zimene angazimvetse. Koma mwanayo akamakula, bambo akewo amayamba kumuuza zambiri. Mofanana ndi zimenezi, Yehova amadziwa nthawi yabwino yoti aululire anthu ake mfundo zokhudza zimene iye akufuna kuchita.​—Miyambo 4:18; Danieli 12:4.

      6. (a) Kodi cholinga cha pangano n’chiyani? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anachita mapangano ndi anthu?

      6 Ndiye kodi Yehova ankaulula bwanji zimenezi? Ankaziulula pochita mapangano osiyanasiyana ndi anthu. N’kutheka kuti nthawi ina munasainiranapo pangano ndi munthu wina, kaya linali lokhudza kugula nyumba kapena kubwerekana ndalama. Pangano loterolo limatsimikizira mwalamulo kuti aliyense adzachita zimene mwagwirizana. Popeza mawu a Yehova ndi okwanira kutsimikizira kuti adzakwaniritsa zimene walonjeza, n’chifukwa chiyani ankafunika kuchita mapangano ndi anthu? N’zoonadi kuti nthawi zonse amakwaniritsa mawu ake, komabe mokoma mtima nthawi zina Yehova amachita pangano ndi anthu pofuna kutsimikizira kuti zimene wanena zidzachitikadi. Mapangano odalirikawa, amathandiza anthu omwe si angwirofe kuti tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti iye adzakwaniritsa zimene walonjeza.​—Aheberi 6:16-18.

      Anachita Pangano ndi Abulahamu

      7, 8. (a) Kodi Yehova anapanga pangano lotani ndi Abulahamu, ndipo zinathandiza anthu kudziwa chiyani zokhudza chinsinsi chopatulika? (b) Kodi Yehova anafotokoza zinthu ziti pang’onopang’ono poulula banja limene mbadwa yolonjezedwa idzachokere?

      7 Patatha zaka zoposa 2,000 kuchokera pamene anthu anathamangitsidwa m’Paradaiso, Yehova anauza mtumiki wake wokhulupirika Abulahamu kuti: “Ndidzachulukitsadi mbadwa zako ngati nyenyezi zakumwamba . . . Kudzera mwa mbadwa yako, mitundu yonse yapadziko lapansi idzapeza madalitso chifukwa chakuti wamvera mawu anga.” (Genesis 22:17, 18) Limeneli silinali lonjezo chabe. Pofuna kutsimikizira kuti adzakwaniritsadi zimenezi, pamenepa Yehova anapanga pangano ndi Abulahamu ndipo kenako analumbira. (Genesis 17:1, 2; Aheberi 6:13-15) N’zochititsa chidwi kuti Ambuye Wamkulu Koposa analonjeza mwalamulo kuti adzadalitsa anthu.

      ‘Ndidzachulukitsa mbadwa zako ngati nyenyezi zakumwamba’

      8 Pangano la Abulahamu linaulula zoti wolonjezedwayo adzakhala munthu, chifukwa Yehova anati adzakhala mbadwa ya Abulahamu. Koma kodi munthu wake ndi ndani? Patapita nthawi, Yehova anaulula kuti pa ana a Abulahamu, mbadwayo idzachokera mwa Isaki. Pa ana awiri a Isaki, Yakobo ndi amene anasankhidwa. (Genesis 21:12; 28:13, 14) Kenako, Yakobo ananena mawu awa okhudza mmodzi wa ana ake aamuna 12: “Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda, ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, mpaka Silo [kapena kuti, “Mwini Wake,” mawu a m’munsi] atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.” (Genesis 49:10) Tsopano zinadziwika kuti mbadwayo idzakhala mfumu ndipo idzachokera kwa Yuda.

      Anachita Pangano ndi Aisiraeli

      9, 10. (a) Kodi Yehova anachita pangano liti ndi Aisiraeli, nanga panganolo linkawateteza bwanji? (b) Kodi Chilamulo chinasonyeza bwanji kuti anthu ankafunikira dipo?

      9 M’chaka cha 1513 B.C.E., Yehova anachitanso zinthu zina zimene zinathandiza kuti mbali zina zokhudza chinsinsi chopatulika zidziwike. Anachita pangano ndi Aisiraeli omwe anali mbadwa za Abulahamu ndipo limeneli linali pangano la Chilamulo cha Mose. Ngakhale kuti panganoli silikugwiranso ntchito panopa, linali lofunika kwambiri kuti cholinga cha Yehova chobweretsa mbadwa yolonjezedwa chikwaniritsidwe. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani zinthu zitatu izi. Choyamba, Chilamulo chinali ngati khoma loteteza. (Aefeso 2:14) Malamulo olungama a m’Chilamulochi ankasiyanitsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina. Choncho Chilamulo chinateteza mzere wobadwira wa mbadwa yolonjezedwa. Zimenezi zinathandiza kuti mtundu wa Aisiraeli ukhalepobe mpaka nthawi imene Mulungu anatumiza Mesiya kuti adzabadwire mu fuko la Yuda.

      10 Chachiwiri, Chilamulo chinasonyeza bwino kuti anthu ankafunikira dipo. Popeza Chilamulo chinali changwiro, chinathandiza Aisiraeli kudziwa kuti anthu ochimwa sangathe kuchitsatira popanda kulakwitsa chilichonse. Choncho chinathandiza “kuti machimo aonekere, mpaka mbadwa imene inapatsidwa lonjezolo itafika.” (Agalatiya 3:19) Nsembe za nyama zimene Aisiraeli anauzidwa kuti azipereka sizinkaphimbiratu machimo a anthu. Mogwirizana ndi zimene Paulo ananena, “n’zosatheka kuti magazi a ng’ombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.” Choncho nsembe zimenezi zinkangoimira nsembe ya dipo ya Khristu. (Aheberi 10:1-4) Kwa Ayuda okhulupirika, pangano la Chilamulo linali ‘wowayang’anira amene anawatsogolera kwa Khristu.’​—Agalatiya 3:24.

      11. Kodi pangano la Chilamulo linathandiza mtundu wa Isiraeli kukhala ndi chiyembekezo chabwino chiti, koma n’chifukwa chiyani Aisiraeli ambiri sanakhale ndi chiyembekezo chimenechi?

      11 Chachitatu, pangano limeneli linathandiza Aisiraeli kuti akhale ndi chiyembekezo. Yehova anawauza kuti akadzakhala okhulupirika pa zimene anapangana naye, adzakhala ‘ufumu wa ansembe komanso mtundu woyera.’ (Ekisodo 19:5, 6) Patapita nthawi anthu oyambirira oti akakhale mafumu ndi ansembe kumwamba, anachokeradi mu mtundu wa Isiraeli. Komabe Aisiraeli ambiri sanatsatire pangano la Chilamulo ndipo anakana mbadwa yomwe inali Mesiya, choncho anataya mwayiwu. Ndiyeno kodi Yehova akanasankha ndani kuti alowe m’malo mwawo? Nanga pakanakhala kugwirizana kotani pakati pa anthu osankhidwawo ndi mbadwa yolonjezedwa? Mulungu anaulula mbali za chinsinsi chopatulika zimenezi pa nthawi yake.

      Anachita Pangano la Ufumu ndi Davide

      12. Kodi Yehova anachita pangano lotani ndi Davide, nanga linathandiza anthu kudziwa mfundo zina ziti zokhudza chinsinsi chopatulika cha Mulungu?

      12 M’zaka za m’ma 1,000 B.C.E., Yehova anaululanso zinthu zina zokhudza chinsinsi chopatulika pamene anachita pangano linanso. Analonjeza Davide, yemwe anali mfumu yokhulupirika kuti: ‘Ndidzachititsa kuti mbadwa yako, ikhale mfumu ndipo ndidzachititsa kuti ufumu wake ukhazikike. Ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.’ (2 Samueli 7:12, 13; Salimo 89:3) Tsopano zinadziwika kuti mbadwa yolonjezedwa idzabadwira m’banja la Davide. Koma kodi munthu wamba angalamulire mpaka kalekale? (Salimo 89:20, 29, 34-36) Nanga kodi angathe kupulumutsa anthu ku uchimo ndi imfa?

      13, 14. (a) Mogwirizana ndi Salimo 110, kodi Yehova anailonjeza chiyani Mfumu yake yodzozedwa? (b) Kodi ndi mfundo zina ziti zokhudza mbadwa yolonjezedwa zimene zinadziwika kudzera mwa aneneri a Yehova?

      13 Davide anauziridwa kulemba kuti: “Yehova anauza Ambuye wanga kuti: ‘Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.’ Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo. Iye wati: ‘Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale, mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki!’” (Salimo 110:1, 4) Mawu a Davidewa ankanena za mbadwa yolonjezedwa, kapena kuti Mesiya. (Machitidwe 2:35, 36) Mfumu imeneyi inali yoti izidzalamulira ili kumwamba “kudzanja lamanja” la Yehova, osati ili ku Yerusalemu. Zimenezi zinasonyeza kuti Mfumuyi sidzalamulira ku Isiraeli kokha koma padziko lonse lapansi. (Salimo 2:6-8) Apa mfundo zinanso zinadziwika. Onani kuti Yehova analumbira kuti Mesiya adzakhala “wansembe . . . mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.” Mofanana ndi Melekizedeki, yemwe anali mfumu ndiponso wansembe m’nthawi ya Abulahamu, mbadwa imene inkabwerayo inali yoti idzasankhidwa mwachindunji ndi Mulungu kuti ikhale Mfumu ndiponso Wansembe.​—Genesis 14:17-20.

      14 M’zaka zotsatira, Yehova anagwiritsa ntchito aneneri ake poulula mfundo zina zokhudza chinsinsi chake chopatulika. Mwachitsanzo, Yesaya anaulula kuti mbadwayo idzapereka moyo wake ngati nsembe. (Yesaya 53:3-12) Mika ananeneratu kumene Mesiya adzabadwire. (Mika 5:2) Ndipo Danieli analosera za nthawi yeniyeni imene Mesiya adzayambe utumiki wake komanso nthawi imene adzafe.​—Danieli 9:24-27.

      Chinsinsi Chopatulika Chinadziwika

      15, 16. (a) Kodi zinachitika bwanji kuti Mwana wa Yehova ‘abadwe kudzera mwa mkazi’? (b) N’chifukwa chiyani Yesu anali woyenera kulowa ufumu wa Davide, nanga ndi liti pamene anakhala mbadwa yolonjezedwa?

      15 Sizinkadziwika kuti maulosiwa adzakwaniritsidwa bwanji mpaka pamene mbadwayo inabwera. Lemba la Agalatiya 4:4 limati: “Nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake, amene anabadwa kudzera mwa mkazi.” M’chaka cha 2 B.C.E., mngelo anauza namwali wina wa Chiyuda dzina lake Mariya, kuti: “Mvetsera! Udzakhala woyembekezera n’kubereka mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina lakuti Yesu. Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzamupatsa mpando wachifumu wa Davide atate wake. . . . “Mzimu woyera udzafika pa iwe ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechi amene adzabadweyo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.”​—Luka 1:31, 32, 35.

      16 Kenako, Yehova anasamutsa moyo wa Mwana wake kuchoka kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya moti Mwanayo anabadwa kudzera mwa mkazi. Mariya sanali wangwiro. Koma Yesu sanatengere kupanda ungwiro kwa Mariya, chifukwa Yesuyo anali “Mwana wa Mulungu.” Komabe popeza makolo ake anali mbadwa za Davide, Yesu anali woyenera mwachibadwa ndiponso mwalamulo kulowa ufumu wa Davide. (Machitidwe 13:22, 23) Pamene Yesu ankabatizidwa m’chaka cha 29 C.E., Yehova anamudzoza ndi mzimu woyera, n’kunena kuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa.” (Mateyu 3:16, 17) Apa tsopano mbadwa ija inafika. (Agalatiya 3:16) Imeneyi inali nthawi yoti Mulungu aulule zinthu zinanso zokhudza chinsinsi chopatulika.​—2 Timoteyo 1:10.

      17. Kodi ndi mfundo ziti zokhudza lemba la Genesis 3:15 zimene zinadziwika?

      17 Pamene Yesu ankachita utumiki wake, anathandiza anthu kudziwa kuti njoka yotchulidwa pa Genesis 3:15 ndi Satana ndipo mbewu ya njokayo ndi otsatira a Satana. (Mateyu 23:33; Yohane 8:44) Patapita nthawi, zinadziwika mmene onsewa adzawonongedwere moti sadzapezekanso. (Chivumbulutso 20:1-3, 10, 15) Kenako zinadziwikanso kuti mkazi ndi “Yerusalemu wam’mwamba,” kapena kuti mkazi wa Mulungu. Imeneyi ndi mbali yakumwamba ya gulu la Yehova lopangidwa ndi angelo okhulupirika.a​—Agalatiya 4:26; Chivumbulutso 12:1-6.

      Pangano Latsopano

      18. Kodi cholinga cha “pangano latsopano” n’chiyani?

      18 Pa mfundo zonse zokhudza chinsinsi chopatulika zimene zinadziwika, mwina mfundo yapadera kwambiri inali imene Yesu anauza ophunzira ake usiku wake womaliza pamene ananena zokhudza “pangano latsopano.” (Luka 22:20) Mofanana ndi pangano la Chilamulo cha Mose, pangano latsopanoli linali loti lidzachititsa kuti pakhale ‘ufumu wa ansembe.’ (Ekisodo 19:6; 1 Petulo 2:9) Komabe anthu a m’pangano limeneli sanali Aisiraeli enieni koma “Isiraeli wa Mulungu,” yemwe ndi otsatira a Khristu okhulupirika omwenso ndi odzozedwa. (Agalatiya 6:16) Anthu a m’pangano latsopano amenewa limodzi ndi Yesu adzathandiza anthu okhulupirika kuti alandire madalitso.

      19. (a) Kodi n’chifukwa chiyani pangano latsopano linathandiza kuti pakhale ‘ufumu wa ansembe’? (b) N’chifukwa chiyani Akhristu odzozedwa amatchedwa kuti “cholengedwa chatsopano,” ndipo ndi angati adzalamulire limodzi ndi Khristu kumwamba?

      19 Koma kodi n’chifukwa chiyani pangano latsopano limathandiza kuti pakhale ‘ufumu wa ansembe’ umene udzadalitse anthu? N’chifukwa chakuti m’malo motsutsa ophunzira a Khristu kuti ndi ochimwa, panganoli limachititsa kuti machimo awo akhululukidwe pogwiritsa ntchito nsembe ya Khristuyo. (Yeremiya 31:31-34) Zikatero Yehova amawaona kuti ndi olungama, kapena kuti opanda uchimo, ndipo amawatenga kuti akhale ana ake n’kuwadzoza ndi mzimu woyera. (Aroma 8:15-17; 2 Akorinto 1:21) Choncho ‘amabadwanso mwatsopano n’kukhala ndi chiyembekezo chodalirika chimene anawasungira kumwamba.’ (1 Petulo 1:3, 4) Popeza anthu analengedwa kuti azikhala padzikoli osati kupita kumwamba, Akhristu odzozedwa ndi mzimu omwe adzapite kumwamba amatchedwa “cholengedwa chatsopano.” (2 Akorinto 5:17) Baibulo limanena kuti anthuwa, omwe ndi okwana 144,000, azidzalamulira anthu okhala padzikoli.​—Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-4.

      20. (a) Kodi ndi mfundo iti yokhudza chinsinsi chopatulika imene inadziwika mu 36 C.E.? (b) Kodi ndi ndani adzasangalale ndi madalitso amene Abulahamu analonjezedwa?

      20 Akhristu odzozedwa amenewa limodzi ndi Yesu amakhala ‘mbadwa ya Abulahamu.’b (Agalatiya 3:29) Oyamba amene anasankhidwa anali Ayuda. Koma m’chaka cha 36 C.E., mfundo inanso yokhudza chinsinsi chopatulika inadziwika: Anthu omwe si Ayuda nawonso adzakhala m’gulu la anthu okalamulira ndi Yesu. (Aroma 9:6-8; 11:25, 26; Aefeso 3:5, 6) Koma kodi Akhristu odzozedwa okha ndi amene adzasangalale ndi madalitso amene Abulahamu analonjezedwa? Ayi. Nsembe ya Yesu imathandiza dziko lonse. (1 Yohane 2:2) Patapita nthawi, Yehova anathandiza anthu kudziwa kuti “khamu lalikulu” la anthu omwe chiwerengero chawo n’chosadziwika, adzapulumuka dziko la Satana likamadzawonongedwa. (Chivumbulutso 7:9, 14) Anthu enanso ambirimbiri adzaukitsidwa ndipo akhoza kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale m’Paradaiso.​—Luka 23:43; Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 20:11-15; 21:3, 4.

      Nzeru za Mulungu Ndiponso Chinsinsi Chopatulika

      21, 22. Kodi chinsinsi chopatulika cha Yehova chimasonyeza bwanji nzeru zake?

      21 Chinsinsi chopatulika chinasonyeza “mbali zosiyanasiyana za nzeru za Mulungu” m’njira yodabwitsa kwambiri. (Aefeso 3:8-10) Yehova anasonyeza kuti alidi ndi nzeru zozama pokonza chinsinsichi n’kumachiulula pang’onopang’ono. Anadziwa kuti anthu sangathe kumvetsa zinthu zozamazi kamodzin’kamodzi. Ndipo chifukwa choti ankachiulula pang’onopan’gono, anapatsa anthu mwayi woti asonyeze kuti amamudalira kapena ayi.​—Salimo 103:14.

      22 Yehova anasonyezanso kuti ndi wanzeru kuposa aliyense pamene anasankha Yesu kuti akhale Mfumu. Mwana wa Yehova ameneyu ndi wodalirika kwambiri kuposa munthu kapena mngelo aliyense. Pamene anali munthu padzikoli, Yesu anakumana ndi mavuto osiyanasiyana choncho amamvetsa bwino mavuto a anthu. (Aheberi 5:7-9) Nanga bwanji anthu amene adzalamulire naye limodzi? Kwa zaka zambirimbiri, Yehova wakhala akudzoza amuna ndi akazi osiyanasiyana ochokera m’mitundu yonse ndiponso zilankhulo zonse. Palibe vuto limene tingakumane nalo lomwe aliyense wa anthu amenewa sanakumanepo nalo n’kuthana nalo. (Aefeso 4:22-24) Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri kulamuliridwa ndi mafumu ndi ansembe achifundo amenewa.

      23. N’chifukwa chiyani ndi mwayi waukulu kudziwa chinsinsi chopatulika, ndipo tiyenera kuchita chiyani?

      23 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chinsinsi chopatulika chimene dziko silinachidziwe ndiponso chinali chobisika kwa mibadwo yakale . . . chaululidwa kwa oyera ake.” (Akolose 1:26) Zoonadi, Akhristu odzozedwa, omwe ndi oyera a Yehova, amvetsa zinthu zambiri zokhudza chinsinsi chopatulika, ndipo amauzanso anthu mamiliyoni ambiri. Tonsefe tili ndi mwayi waukulu kwambiri. Yehova ‘watiululira chinsinsi chake chopatulika chokhudza chifuniro chake.’ (Aefeso 1:9) Tiyeni tiziuza ena chinsinsi chosangalatsachi kuti nawonso athe kuona nzeru zosaneneka za Yehova Mulungu.

      a “Chinsinsi chopatulika chokhudza kukhala odzipereka kwa Mulungu,” chinadziwikanso kudzera mwa Yesu. (1 Timoteyo 3:16) Kwanthawi yaitali sizinkadziwika ngati munthu angakhalebe wokhulupirika kwa Yehova pa chilichonse. Koma Yesu anasonyeza kuti zimenezi n’zotheka. Anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti Satana anamuyesa m’njira zosiyanasiyana.​—Mateyu 4:1-11; 27:26-50.

      b Yesu anachitanso “pangano la ufumu” ndi gulu lomweli. (Luka 22:29, 30) Apatu Yesu anapangana ndi anthu a mu “kagulu ka nkhosa” kameneka kuti adzalamulire naye limodzi kumwamba monga mbali yachiwiri ya mbadwa ya Abulahamu.​—Luka 12:32.

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Yohane 16:7-12 Kodi Yesu ankatsanzira bwanji Atate ake pa nkhani youlula mfundo za choonadi pang’onopang’ono?

      • 1 Akorinto 2:6-16 N’chifukwa chiyani anthu ambiri sakwanitsa kumvetsa zinsinsi zopatulika za Yehova, ndipo tingamvetse bwanji zinsinsi zimenezi?

      • Aefeso 3:10 Kodi masiku ano Akhristu ali ndi mwayi wotani wokhudza chinsinsi chopatulika cha Mulungu?

      • Aheberi 11:8-10 Kodi chinsinsi chopatulika chinathandiza bwanji anthu akale kukhala okhulupirika ngakhale kuti sankamvetsa mfundo zina?

  • “Ali ndi Mtima Wanzeru” Koma Ndi Wodzichepetsa
    Yandikirani Yehova
    • Bambo wagwada ndipo akuyang’ana mwana wake mosangalala.

      MUTU 20

      “Ali ndi Mtima Wanzeru” Koma Ndi Wodzichepetsa

      1-3. N’chiyani chimatitsimikizira kuti Yehova ndi wodzichepetsa?

      BAMBO akufuna kuphunzitsa mwana wake wamng’ono mfundo yofunika kwambiri. Akufunitsitsa kuti imufike pamtima. Kodi ayenera kumuphunzitsa bwanji? Kodi ayenera kuimirira momuopseza n’kumalankhula mwaukali? Kapena kodi ayenera kugwada kuti afanane ndi msinkhu wa mwanayo n’kumalankhula modekha komanso mokoma mtima? Kunena zoona, ngati bamboyo ndi wanzeru ndiponso wodzichepetsa angasankhe kulankhula naye mokoma mtima.

      2 Kodi Yehova ndi Bambo wotani? Wodzikuza kapena wodzichepetsa? Waukali kapena wodekha? Yehova amadziwa zonse ndipo ndi wanzeru kuposa aliyense. Komabe mwina mukudziwa kuti si nthawi zonse pamene munthu wodziwa zinthu ndiponso wanzeru amakhala wodzichepetsa. Paja Baibulo limanena kuti “kudziwa zinthu kumachititsa munthu kukhala wodzikuza.” (1 Akorinto 3:19; 8:1) Koma ngakhale kuti “ali ndi mtima wanzeru,” Yehova ndi wodzichepetsa. (Yobu 9:4) Zimenezi sizikutanthauza kuti ndi wotsika kapenanso si wamkulu, zikungotanthauza kuti si wodzikuza. N’chifukwa chiyani tikutero?

      3 Yehova ndi woyera. Choncho iye si wodzikuza chifukwa kudzikuza kumaipitsa munthu. (Maliko 7:20-22) Taonani zimene mneneri Yeremiya anauza Yehova. Iye anati: “Ndithu mudzandikumbukira ndi kundiweramira kuti mundithandize.”a (Maliro 3:20) Tangoganizani. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa anali wofunitsitsa ‘kuwerama,’ kapena kuti kugwada kuti afanane msinkhu ndi Yeremiya, n’cholinga choti athandize munthu yemwe sanali wangwiroyu. (Salimo 113:7) Kunena zoona, Yehova ndi wodzichepetsa. Koma kodi Mulungu amasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa? Kodi kudzichepetsa n’kogwirizana bwanji ndi kukhala wanzeru? Nanga kudzichepetsa kwa Yehova kumatithandiza bwanji?

      Kodi Yehova Amasonyeza Bwanji Kuti Ndi Wodzichepetsa?

      4, 5. (a) Kodi kudzichepetsa n’chiyani, nanga timadziwa bwanji kuti munthu ndi wodzichepetsa? N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti munthu wodzichepetsa ndi wofooka kapena wamantha? (b) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kudzichepetsa tikaganizira mmene anachitira zinthu ndi Davide, nanga kudzichepetsa kwa Yehova kumatithandiza bwanji?

      4 Kudzichepetsa kumatanthauza kusadzikuza, kusadzikweza ndiponso kusakhala wonyada. Kudzichepetsa kumachokera mumtima ndipo munthu amene ali ndi khalidweli amakhalanso wofatsa, woleza mtima komanso wololera. (Agalatiya 5:22, 23) Komabe, tisamaganize kuti popeza Yehova ndi wodzichepetsa, wofatsa ndiponso woleza mtima, ndiye kuti sangakwiye ndi zinthu zopanda chilungamo. Tisamaganizenso kuti ndi wofooka kapena wamantha ndipo sangagwiritse ntchito mphamvu zake zowononga. M’malomwake, pokhala wodzichepetsa komanso wofatsa, Yehova amasonyeza kuti ali ndi mphamvu zopanda malire moti amatha kudziletsa bwinobwino. (Yesaya 42:14) Ndiye kodi kudzichepetsa kumagwirizana bwanji ndi nzeru? Buku lina lofotokoza za m’Baibulo limati: “Mwachidule tinganene kuti munthu amadziwika kuti ndi wodzichepetsa . . . ngati ali wosadzikonda ndipo kudzichepetsa n’kofunika kwambiri kuti munthu athe kuchita zinthu mwanzeru pa chilichonse.” Choncho munthu sangakhale ndi nzeru zenizeni ngati si wodzichepetsa. Kodi kudzichepetsa kwa Yehova kumatithandiza bwanji?

      Bambo wanzeru amachita zinthu ndi ana ake modzichepetsa ndiponso mofatsa

      5 Mfumu Davide anaimbira Yehova kuti: “Inu mumandipatsa chishango chanu chachipulumutso, dzanja lanu lamanja limandithandiza, ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.” (Salimo 18:35) Tingati Yehova anadzitsitsa kuti afanane msinkhu ndi munthu yemwe sanali wangwiroyu n’cholinga choti azimuteteza komanso kumusamalira tsiku lililonse. Davide ankadziwa kuti akanapulumutsidwa ndiponso kukhala mfumu yaikulu pokhapokha ngati Yehova akanadzichepetsa mwanjira imeneyi n’kumuthandiza. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo. Ndi ndani akanakhala ndi chiyembekezo chodzapulumuka zikanakhala kuti Yehova sanadzichepetse kuti atithandize ngati Bambo wofatsa komanso wokoma mtima?

      6, 7. (a) N’chifukwa chiyani Baibulo silisonyeza kuti kudzichepetsa kwa Yehova n’kofanana ndi kwa anthu? (b) Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kufatsa ndi nzeru, nanga ndi ndani amene amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi?

      6 Kudzichepetsa ndi khalidwe labwino kwambiri limene anthu okhulupirika ayenera kukhala nalo. Khalidweli limayendera limodzi ndi kukhala wanzeru. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 11:2 limati: “Anthu odzichepetsa ndi amene ali ndi nzeru.” Komabe, Baibulo silinena kuti Yehova ndi wodzichepetsa m’njira yofanana ndi mmene anthu amayenera kukhalira odzichepetsa. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa m’Baibulo mawu akuti kudzichepetsa akamanena za anthu, amatanthauza kudziwa kuti pali zina zomwe sungathe kuchita kapena si udindo wako kuzichita. Koma Mulungu Wamphamvuyonse akhoza kuchita chilichonse kupatulapo zimene anachita kusankha kuti asamachite chifukwa chotsatira mfundo zake zolungama. (Maliko 10:27; Tito 1:2) Ndiponso popeza iye ndi Wam’mwambamwamba, palibe ali ndi ufulu womuuza zochita. Choncho kwa Yehova, kudzichepetsa sikutanthauza kudziwa kuti pali zina zomwe sangathe kuchita kapena si udindo wake kuzichita.

      7 Komabe, Yehova ndi wodzichepetsa ndiponso wofatsa. Amaphunzitsa atumiki ake kuti kukhala wofatsa n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi nzeru zenizeni. Mawu ake amanena kuti ‘kufatsa ndi khalidwe limene limabwera chifukwa cha nzeru.’ (Yakobo 3:13) Taganizirani chitsanzo cha Yehova pa nkhaniyi.

      Yehova Amapatsa Ena Zochita Komanso Amamvetsera

      8-10. (a) N’chifukwa chiyani n’zochititsa chidwi kuti Yehova amapatsa ena zochita komanso amamvetsera? (b) Kodi Wamphamvuyonse anasonyeza bwanji kudzichepetsa pochita zinthu ndi angelo ake?

      8 Yehova amasonyezanso kuti ndi wodzichepetsa m’njira ina yochititsa chidwi kwambiri. Mofunitsitsa, iye amapatsa ena zochita ndiponso amamvetsera. N’zodabwitsa kwambiri kuti iye amachita zimenezi, chifukwatu Yehova safunika thandizo kapena malangizo. (Yesaya 40:13, 14; Aroma 11:34, 35) Koma m’Baibulo muli zitsanzo zambiri zimene zimasonyeza kuti Yehova amadzichepetsa n’kumapatsa ena zochita komanso amamvetsera.

      9 Mwachitsanzo, taganizirani zinthu zosaiwalika zomwe zinachitikira Abulahamu. Abulahamu analandira alendo atatu ndipo mmodzi wa iwo ankamutchula kuti “Yehova.” Alendowo anali angelo, koma mmodzi anabwera m’dzina la Yehova ndipo ankachita zinthu m’dzina la Yehovayo. Mngelo ameneyo akamalankhula komanso kuchita zinthu, zinali ngati akuchita zimenezo ndi Yehova. Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, Yehova anauza Abulahamu kuti anamva ‘madandaulo ambiri okhudza machimo a anthu am’mizinda ya Sodomu ndi Gomora.’ Yehova anati: “Ndipitako kuti ndikaone ngati akuchitadi zimene ndamvazo. Ndikufuna ndidziwe ngati zochita zawo zilidi zoipa choncho.” (Genesis 18:3, 20, 21) Komabe mawu a Yehovawa sankatanthauza kuti Wamphamvuyonseyo ‘apitako’ yekha. Iye anatumanso angelo kuti akamuimire. (Genesis 19:1) Chifukwa chiyani? N’zodziwikiratu kuti Yehova, yemwe amaona zonse, akanatha ‘kudziwa’ zimene zinkachitika kuderalo. Koma modzichepetsa, anapatsa angelowo ntchito yoti akafufuze zimene zinkachitika ndiponso akaone Loti ndi banja lake ku Sodomu.

      10 Komanso, Yehova amamvetsera. Pa nthawi ina anafunsa angelo ake kuti apereke maganizo awo pa zimene angachite kuti alimbikitse Ahabu kupita kunkhondo n’kukafa. Sikuti Yehova ankafunika thandizo pa nkhaniyi. Komatu anagwirizana ndi maganizo a mngelo wina n’kumutuma kuti akachite zimene ananenazo. (1 Mafumu 22:19-22) Kodi kudzichepetsa kupose pamenepa?

      11, 12. Kodi Abulahamu anadziwa bwanji kuti Yehova ndi wodzichepetsa?

      11 Yehova amakhalanso wokonzeka kumvetsera anthu omwe si angwiro akamafotokoza maganizo awo komanso zinthu zomwe zikuwadetsa nkhawa. Mwachitsanzo, Yehova atauza Abulahamu kuti akufuna kuwononga Sodomu ndi Gomora, munthu wokhulupirikayo anadabwa kwambiri. Iye anati: “Simungachite zimenezo. Ndinu Woweruza wa dziko lonse lapansi. Ndiye kodi simuchita chilungamo?” Abulahamu anafunsa Yehova ngati sakanawononga mizindayo mukanapezeka anthu olungama 50. Yehova anamutsimikizira kuti sakanawononga. Koma Abulahamu anafunsanso. Anachepetsa nambala ya anthu olungamawo kufika pa 45, kenako pa 40 n’kumangoichepetsabe. Ngakhale kuti Yehova ankamutsimikizira kuti sakanawononga, Abulahamu anapitiriza kufunsa mpaka nambalayo inafika pa 10. Mwina pa nthawiyi Abulahamu anali asanamvetse kuti Yehova ndi wachifundo kwambiri. Koma Yehova moleza mtima ndiponso modzichepetsa, analola kuti Abulahamu, yemwe anali mnzake komanso mtumiki wake, afotokoze zimene zinkamudetsa nkhawa.​—Genesis 18:23-33.

      12 Kodi ndi anthu angati anzeru ndiponso ophunzira amene angamvetsere moleza mtima chonchi kwa munthu wosaphunzira?b Komatu Mulungu wathu anachita zimenezi chifukwa ndi wodzichepetsa. Pa nthawi imene ankakambiranayi, Abulahamu anaonanso kuti Yehova ndi “wosakwiya msanga.” (Ekisodo 34:6) Mwina chifukwa chodziwa kuti analibe ufulu wofunsa Wam’mwambamwamba chifukwa chake akuchita zinazake, Abulahamu anapempha kawiri konse kuti: “Yehova, musandipsere mtima.” (Genesis 18:30, 32) Yehova sanamupseredi mtima. Iye ndi wofatsa, “khalidwe limene limabwera chifukwa cha nzeru.”

      Yehova Ndi Wololera

      13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi wololera?

      13 Yehova ndi wololera ndipo khalidweli limasonyezanso kuti ndi wodzichepetsa. N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri anthu omwe si angwirofe timalephera kukhala ololera. Monga taona kale, Yehova amakhala wokonzeka kumvetsera angelo ake komanso anthu akamalankhula. Koma kuwonjezera pamenepa, amakhalanso wololera ngati mfundo zake sizikuphwanyidwa. Khalidwe limeneli ndi umboni winanso woti Yehova ndi wanzeru. Lemba la Yakobo 3:17 limati: ‘Nzeru yochokera kumwamba ndi yololera.’ Kodi Yehova, yemwe ndi wanzeru pa chilichonse, amasonyeza bwanji kuti ndi wololera? Njira imodzi ndi yakuti amatha kusintha n’kuchita zinthu mogwirizana ndi mmene zilili pa nthawiyo. Kumbukirani kuti dzina lake limatanthauza kuti amakhala chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse cholinga chake. (Ekisodo 3:14) Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Yehova ndi wololera ndipo amasintha pakafunika kutero?

      14, 15. Kodi masomphenya a Ezekieli a galeta lakumwamba la Yehova amatiphunzitsa chiyani zokhudza mbali yakumwamba ya gulu la Yehova, ndipo limasiyana bwanji ndi mabungwe a anthu?

      14 Chaputala china cha m’Baibulo chimatithandiza kumvetsa mfundo yoti Yehova amatha kusintha ngati pakufunika kutero. Mneneri Ezekieli anaona masomphenya a mbali yakumwamba ya gulu la Yehova, yomwe ndi angelo. Anaona galeta lalikulu ndiponso lochititsa mantha, lomwe lili ngati “galimoto” ya Yehova imene amaiwongolera. Galetali linkayenda mochititsa chidwi kwambiri. Linali ndi mawiro akuluakulu omwe anali ndi mbali 4 ndiponso maso paliponse moti ankatha kuona chilichonse. Galetali linkatha kusintha kopita mofulumira kwambiri popanda kuima kapena kukhota. Ngakhale kuti ndi lalikulu, silinkayenda pang’onopang’ono ngati mmene zimakhalira ndi chigalimoto chachikulu chopangidwa ndi anthu. Linkayenda pa liwiro lofanana ndi mphezi n’kumathanso kukhota likuthamanga choncho. (Ezekieli 1:1, 14-28) Choncho mofanana ndi Yehova, nalonso gulu lake limatha kusintha mofulumira mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa nthawiyo.

      15 Nawonso anthu angafune kuti azichita zimenezi. Komabe nthawi zambiri anthuwa komanso mabungwe amavutika kuti asinthe n’kumachita mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Mwachitsanzo, sitima yapamadzi yonyamula mafuta kapena yapamtunda yonyamula katundu imachititsa chidwi kwambiri chifukwa choti imakhala yaikulu komanso yamphamvu. Koma kodi sitima zimenezi zimatani pakachitika zinthu zadzidzidzi? Ngati kutsogolo kwa sitima yonyamula katundu kutagwera chinthu, sizingatheke kuti ikhotere kumbali. Imavutikanso kuti iime mwadzidzidzi. Ndipo ngati yanyamula katundu wambiri ingayendebe pafupifupi mtunda wa makilomita awiri pambuyo poti amanga mabuleki. Nayonso sitima yapamadzi yonyamula mafuta ikhoza kuyendabe mtunda wa makilomita 8, atazimitsa injini zake. Ngakhale injini zake ataziika mu giya yobwerera m’mbuyo, sitimayi ingapitebe kutsogolo makilomita atatu, isanayambe kubwerera m’mbuyo. Zimenezi n’zofanana ndi zimene mabungwe a anthu amachita. Nthawi zambiri zinthu zikasintha amavutika kusintha ndipo sakhala ololera. Iwo amachita zimenezi chifukwa cha kunyada. Zotsatira zake zimakhala zakuti makampani amakumana ndi mavuto azachuma komanso maboma amagwa. (Miyambo 16:18) Koma timasangalala kwambiri chifukwa Yehova ndiponso gulu lake ndi osiyana kwambiri ndi anthu.

      Kodi Yehova Amasonyeza Bwanji Kuti Ndi Wololera?

      16. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kulolera pa zomwe anachitira Loti asanawononge Sodomu ndi Gomora?

      16 Taganiziraninso nkhani yokhudza kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora. Mngelo wa Yehova anapatsa Loti ndi banja lake malangizo omveka bwino akuti: “Thawirani kudera lakumapiri.” Komabe zimenezi sizinamusangalatse Loti moti anapempha kuti: “Chonde Yehova, kumeneko ayi!” Loti ankaona kuti akathawira kumapiriko akafa, choncho anachonderera kuti iye ndi banja lake athawire kutauni ya Zowari, yomwe inali yapafupi. Koma Yehova ankafuna kuwononganso tauni imeneyi. Ndiponso panalibe zifukwa zomveka zoti Loti achitire mantha chifukwa Yehova akanatha kumuteteza kumapiriko. Komabe Yehova anavomera zimene Loti anapemphazi. Mngelo uja anauza Loti kuti: “Chabwino, ndavomera zimene wapempha. Sindiwononga tauni imene wanenayo.” (Genesis 19:17-22) Apatu Yehova anasonyeza kulolera.

      17, 18. Pa zimene anachitira anthu a ku Nineve, kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi wololera?

      17 Yehova amathanso kusintha munthu akalapa mochokera pansi pa mtima ndipo amamuchitira zinthu mwachifundo ndiponso mwachilungamo. Taganizirani zimene zinachitika mneneri Yona atatumidwa kumzinda wa Nineve womwe anthu ake ankachita zoipa komanso zachiwawa. Yona ankayenda m’misewu ya ku Nineve n’kumalengeza uthenga wosavuta kumva wochokera kwa Yehova wakuti mzinda wamphamvuwo uwonongedwa pakatha masiku 40. Komabe zinthu zinasintha kwambiri. Anthu a ku Nineve analapa.​—Yona, chaputala 3.

      18 Tingaphunzire zambiri tikayerekezera zimene Yehova anachita ndi zimene Yona anachita zinthu zitasintha chonchi. Yehova anasintha mogwirizana ndi mmene zinthu zinalili ndipo anakhala Wokhululukira machimo m’malo mokhala “msilikali wamphamvu.”c (Ekisodo 15:3) Koma Yona sanali wokonzeka kusintha ndipo sanasonyeze chifundo. M’malo mokhala wololera ngati Yehova, iye anachita zinthu ngati sitima yapamadzi yonyamula mafuta kapena yapamtunda yonyamula katundu ija. Popeza anali atalengeza kuti anthuwo awonongedwa, iye ankaona kuti akuyenera kuwonongedwa basi. Komabe, moleza mtima Yehova anaphunzitsa mneneri wake wosaleza mtimayu mfundo yofunika kwambiri pa nkhani ya kulolera ndiponso chifundo.​—Yona, chaputala 4.

      M’bale wachinyamata ali mu utumiki ndi m’bale wachikulire ndipo akumuthandiza mosangalala.

      Yehova ndi wololera ndipo amamvetsa zimene sitingathe kuchita

      19. (a) N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova ndi wololera pa zimene amayembekezera kuti tizichita? (b) Kodi lemba la Miyambo 19:17 likusonyeza bwanji kuti Yehova ndi Bwana wabwino, wololera komanso wodzichepetsa kwambiri?

      19 Chomaliza, Yehova amasonyezanso kuti ndi wololera pa zimene amayembekezera kuti anthufe tizichita. Mfumu Davide inati: “Iye akudziwa bwino mmene anatipangira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:14) Yehova amadziwa zimene sitingathe kuchita ndiponso chifukwa chake timalakwitsa zinthu zina kuposa mmene eni akefe timadziwira. Sayembekezera kuti tizichita zomwe sitingathe. Baibulo limanena kuti pali mabwana “abwino ndi ololera,” komanso pali “ovuta kuwakondweretsa.” (1 Petulo 2:18) Kodi tingati Yehova ndi Bwana wotani? Taonani zimene lemba la Miyambo 19:17 limanena: “Amene amakomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova.” Kunena zoona, mabwana abwino komanso ololera okha ndi amene angamadziwe chinthu chabwino chilichonse chimene ena achitira anthu ovutika. Kuwonjezera pamenepa, lembali likusonyeza kuti Mlengi wa chilengedwe chonse amaona kuti ali ndi ngongole kwa anthu amene amachitira ena zinthu zachifundo zimenezo. Pamenepatu amasonyeza kuti ndi wodzichepetsa kwambiri.

      20. Kodi n’chiyani chimatitsimikizira kuti Yehova amamva ndiponso kuyankha mapemphero athu?

      20 Masiku anonso Yehova amasonyeza kuti ndi wofatsa komanso wololera akamachita zinthu ndi atumiki ake. Tikamapemphera tili ndi chikhulupiriro, iye amamvetsera. Ndipo ngakhale kuti satumiza angelo kuti adzalankhule nafe, tisamaganize kuti sayankha mapemphero athu. Kumbukirani kuti pamene mtumwi Paulo anapempha Akhristu anzake kuti ‘azimupempherera’ kuti amasulidwe m’ndende, anatinso: “Kuti ndibwerere kumeneko mwamsanga.” (Aheberi 13:18, 19) Choncho mapemphero athu akhoza kuchititsa kuti Yehova achite zinthu zimene mwina sakanazichita.​—Yakobo 5:16.

      21. Kodi sitiyenera kuganiza chiyani zokhudza kudzichepetsa kwa Yehova, koma tiyenera kuzindikira mfundo iti yokhudza iyeyo?

      21 Komabe ngakhale kuti Yehova amasonyeza kuti ndi wodzichepetsa pokhala wofatsa, wokonzeka kumvetsera, woleza mtima ndiponso wololera, sanyalanyaza mfundo zake zolungama. Atsogoleri a matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu angaganize kuti ndi ololera akamauza anthu awo kuti sikulakwa kuchita zinthu zimene Yehova amadana nazo, chifukwa choti zimenezo ndi zimene anthuwo angafune kumva. (2 Timoteyo 4:3) Anthu ali ndi chizolowezi chololera kuchita zolakwika pongofuna kusangalatsa ena, koma kulolera kumeneku n’kosagwirizana ndi kulolera kwa Mulungu. Yehova ndi woyera ndipo saphwanya mfundo zake zolungama. (Levitiko 11:44) Choncho tiyenera kumvetsa mfundo yoti Yehova ndi wololera chifukwa choti ndi wodzichepetsa ndipo tiyenera kumukonda kwambiri chifukwa cha zimenezi. Kodi si zosangalatsa kudziwa kuti Yehova, yemwe ndi wanzeru kwambiri m’chilengedwe chonse, ndi wodzichepetsa kwambiri? Ndi mwayitu waukulu kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu wogometsa ameneyu, yemwenso ndi wofatsa, woleza mtima komanso wololera.

      a Anthu ena akale omwe ankakopera Baibulo otchedwa Asoferimu anasintha vesili kuti lizimveka ngati Yeremiya ndi amene akuwerama osati Yehova. Zikuoneka kuti iwo ankaganiza kuti n’zosayenera kunena kuti Mulungu angachite zinthu modzichepetsa chonchi kuti athandize munthu. Chifukwa cha zimenezi, Mabaibulo ambiri sanamasulire bwino mfundo yosangalatsa imene ili m’vesili. Komabe, Baibulo lina linamasulira molondola kuti Yeremiya anauza Mulungu kuti: “Kumbukirani, kumbukirani ndipo mundiweramire.”​—The New English Bible.

      b N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limanena kuti munthu wosaleza mtima amakhala wodzikuza. (Mlaliki 7:8) Choncho mfundo yoti Yehova ndi woleza mtima, ikusonyezanso kuti ndi wodzichepetsa.​—2 Petulo 3:9.

      c Pa Salimo 86:5, Baibulo limati Yehova ndi ‘wabwino ndiponso wokonzeka kukhululuka.’ Pamene Salimoli ankalimasulira m’Chigiriki, mawu akuti “wokonzeka kukhululuka” anawamasulira kuti e·pi·ei·kesʹ, kapena kuti “wololera.”

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Ekisodo 32:9-14 Kodi Yehova anasonyeza bwanji kudzichepetsa pamene anamvera zimene Mose anamuchonderera zokhudza Aisiraeli?

      • Oweruza 6:36-40 Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuleza mtima ndiponso kulolera pochita zimene Gidiyoni anapempha?

      • Salimo 113:1-9 Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa akamachita zinthu ndi anthu?

      • Luka 1:46-55 Kodi Mariya ankakhulupirira kuti Yehova amawaona bwanji anthu odzichepetsa ndi onyozeka? Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhaniyi?

  • Yesu Amatisonyeza “Nzeru za Mulungu”
    Yandikirani Yehova
    • Yesu akuphunzitsa gulu lalikulu la anthu.

      MUTU 21

      Yesu Amatisonyeza “Nzeru za Mulungu”

      1-3. Kodi anthu akwawo kwa Yesu anatani atamva zimene Yesuyo ankaphunzitsa, ndipo analephera kudziwa mfundo iti yokhudza iyeyo?

      ANTHU amene ankamumvetsera anadabwa kwambiri. Yesu, yemwe anali wachinyamata, anaimirira kutsogolo kwawo m’sunagoge n’kumaphunzitsa. Sanali mlendo kwa anthuwo, chifukwa anakulira m’tauni yawo yomweyo ndipo kwa zaka zambiri ankamuona akugwira ntchito ya ukalipentala. Mwina ena mwa anthuwa ankakhala m’nyumba zimene Yesu anamanga nawo, kapena polima minda yawo ankagwiritsa ntchito mapulawo ndi magoli amene iye anapanga.a Ndiye kodi iwo akanamvera zonena za munthu ameneyu yemwe poyamba anali kalipentala?

      2 Ambiri mwa anthu amene ankamumvetsera anadabwa ndipo ankafunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu, nzeru . . . zoterezi anazitenga kuti?” Anafunsanso kuti: “Kodi iyeyu si kalipentala, mwana wa Mariya?” (Mateyu 13:54-58; Maliko 6:1-3) N’zomvetsa chisoni kuti anthu akwawo kwa Yesuwa ankangoganiza kuti, ‘kalipentala uyu ndi munthu wa kwathu konkuno.’ Ngakhale kuti ankalankhula zanzeru, iwo anamukana. Koma sanadziwe kuti nzeruzo sizinali zake.

      3 Kodi Yesu anazitenga kuti nzeru zimenezi? Iye anati, “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga, koma ndi za amene anandituma.” (Yohane 7:16) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Yesu “amatisonyeza nzeru za Mulungu.” (1 Akorinto 1:30) Mwana wa Mulunguyu amatithandiza kudziwa nzeru za Yehova. Zimenezi n’zoonadi, moti mpaka Yesu anafika ponena kuti: “Ine ndi Atate ndife amodzi.” (Yohane 10:30) Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene Yesu anasonyezera “nzeru za Mulungu.”

      Zimene Ankaphunzitsa

      4. (a) Kodi mfundo yaikulu ya uthenga umene Yesu ankalalikira inali yotani, ndipo n’chifukwa chiyani uthengawo ndi wofunika kwambiri? (b) N’chifukwa chiyani nthawi zonse malangizo a Yesu anali othandiza kwa omvera ake?

      4 Choyamba, taganizirani zimene Yesu ankaphunzitsa. Mfundo yaikulu ya zimene ankalalikira inali “uthenga wabwino wa Ufumu.” (Luka 4:43) Umenewo unali uthenga wofunika kwambiri chifukwa Ufumuwo udzathandiza kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe, zomwe zikuphatikizapo kutsimikizira kuti iye ndi Wolamulira wachilungamo. Udzathandizanso kuti anthu apeze madalitso osatha. Akamaphunzitsa, Yesu ankaperekanso malangizo othandiza pa moyo wa tsiku ndi tsiku. Anasonyeza kuti analidi “Mlangizi Wodabwitsa” amene Malemba ananeneratu. (Yesaya 9:6) Koma kodi n’chifukwa chiyani Yesu anali “Mlangizi Wodabwitsa”? Ndi chifukwa choti ankadziwa bwino Mawu a Mulungu komanso chifuniro chake, ankamvetsa bwino mmene anthu alili komanso ankakonda kwambiri anthu. Choncho nthawi zonse malangizo ake anali othandiza kwambiri. Yesu ankalankhula “mawu othandiza munthu kuti adzapeze moyo wosatha.” Zoonadi, munthu akamatsatira malangizo a Yesu, adzapeza moyo wosatha.​—Yohane 6:68.

      5. Kodi ndi nkhani zina ziti zimene Yesu anatchula pa ulaliki wa paphiri?

      5 Ulaliki wa pa phiri ndi chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza kuti zimene Yesu ankaphunzitsa zinali zanzeru. Ulaliki umenewu umapezeka pa Mateyu 5:3 mpaka 7:27 ndipo mwina mfundo zake munthu angazifotokoze kwa 20 minitsi yokha. Komabe malangizo ake ndi othandiza komanso ofunika kwambiri masiku ano ngati mmene zinalili pa nthawiyo. Yesu anapereka malangizo pa nkhani zosiyanasiyana monga mmene munthu angakhalire bwino ndi anthu ena (5:23-26, 38-42; 7:1-5, 12), mmene angakhalire ndi khalidwe loyera (5:27-32) ndiponso zimene angachite kuti azisangalala (6:19-24; 7:24-27). Sikuti Yesu anangouza anthuwo malangizo anzeru, koma ankawafotokozera zifukwa zake komanso kuwapatsa zitsanzo. Zimenezi zinkawathandiza kudziwa kufunika kotsatira malangizowo.

      6-8. (a) Kodi Yesu anapereka zifukwa zomveka ziti zotichititsa kuti tisamade nkhawa? (b) N’chiyani chikuonetsa kuti malangizo a Yesu amasonyeza nzeru zochokera kumwamba?

      6 Mwachitsanzo, taonani malangizo anzeru a Yesu pa nkhani yokhudza kudera nkhawa zinthu zofunika pa moyo opezeka pa Mateyu chaputala 6. Iye anatilangiza kuti: “Siyani kudera nkhawa za moyo wanu, kuti mudzadya chiyani kapena kuti mudzamwa chiyani kapenanso kudera nkhawa za matupi anu kuti mudzavala chiyani.” (Vesi 25) Chakudya ndi zovala ndi zinthu zofunika kwambiri pa moyo, ndipo mwachibadwa timada nkhawa kuti tizipeza bwanji. Koma Yesu anatiuza kuti ‘tisiye kudera nkhawa’ zinthu zimenezi.b Chifukwa chiyani?

      7 Yesu anafotokoza zifukwa zomveka zotichititsa kuti tisamade nkhawa. Popeza Yehova anatipatsa moyo ndiponso thupi, kodi sangatipatsenso zovala komanso chakudya chothandiza kuti tikhale ndi moyo? (Vesi 25) Ngati Mulungu amapatsa mbalame chakudya ndiponso kuchititsa kuti maluwa azioneka okongola, ndiye kuli bwanji anthu amene amamulambira? (Vesi 26, 28-30) Kunena zoona, kuda nkhawa kwambiri kulibe phindu lililonse. Sikungatithandize kuti tiwonjezere masiku a moyo wathu.c (Vesi 27) Ndiye kodi tingatani kuti tisamade nkhawa? Yesu anatipatsa malangizo akuti: Pitirizani kuika zinthu zokhudza kulambira pa malo oyamba. Anthu amene amachita zimenezi ayenera kukhulupirira kuti Atate wawo wakumwamba ‘adzawapatsa’ zofunika za tsiku lililonse. (Vesi 33) Pomaliza, Yesu anapereka malangizo othandiza kwambiri akuti, tizithana kaye ndi mavuto a tsiku limodzi. Tisamawonjezere nkhawa za mawa pa mavuto a lero. (Vesi 34) Ndiponso palibe chifukwa choti tizidera nkhawa kwambiri za zinthu zimene mwina sizidzachitika n’komwe. Kutsatira malangizo anzeru amenewa kungatithandize kuti tipewe mavuto ambiri m’dziko loipali.

      8 N’zodziwikiratu kuti malangizo amene Yesu anaperekawa ndi othandiza masiku ano ngati mmenenso analili zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Kodi umenewu si umboni wa nzeru zochokera kumwamba? Malangizo ochokera kwa anthu, ngakhale atakhala anzeru, pakapita nthawi amakhala osathandiza ndipo amafunika kuwakonzanso kapena kuwasintha. Koma zimene Yesu anaphunzitsa zikugwirabe ntchito mpaka pano. Komatu zimenezi siziyenera kutidabwitsa, chifukwa Mlangizi Wodabwitsayu ankalankhula “mawu a Mulungu.”​—Yohane 3:34.

      Mmene Ankaphunzitsira

      9. Kodi alonda ena anati chiyani zokhudza mmene Yesu ankaphunzitsira, nanga n’chifukwa chiyani sikunali kukokomeza?

      9 Njira yachiwiri imene Yesu anasonyezera nzeru za Mulungu, inali mmene ankaphunzitsira. Pa nthawi ina, alonda omwe anatumidwa kuti akamugwire anabwerako chimanjamanja, n’kunena kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” (Yohane 7:45, 46) Sikuti anthuwa ankangokokomeza. Pa anthu onse amene anakhalako, Yesu, yemwe anali “wochokera kumwamba,” ndi amene ankadziwa zinthu zochuluka ndiponso ndi amene anaona zinthu zambiri kuposa wina aliyense moti ankalankhula kuchokera pa zimenezo. (Yohane 8:23) N’chifukwa chake ankaphunzitsa mosiyana ndi wina aliyense. Tiyeni tione njira ziwiri zokha zimene Mphunzitsi wanzeruyu ankagwiritsa ntchito pophunzitsa.

      “Anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake”

      10, 11. (a) N’chifukwa chiyani timagoma tikaganizira mmene Yesu ankagwiritsira ntchito mafanizo? (b) Perekani chitsanzo cha nkhani yongoyerekezera imene Yesu anafotokoza yomwe imatiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri.

      10 Ankagwiritsa ntchito mafanizo mogwira mtima. Baibulo limati Yesu ‘analankhula ndi gulu la anthulo pogwiritsa ntchito mafanizo. Ndithudi, nthawi zonse iye ankalankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo.’ (Mateyu 13:34) Timagoma tikaganizira luso lake lophunzitsa choonadi pogwiritsa ntchito zinthu zimene anthu ankazidziwa bwino. Anatchula za alimi akudzala mbewu, azimayi akukonzekera kupanga mkate, ana akusewera pamsika, asodzi akuponya makoka ndiponso abusa akufunafuna nkhosa zosochera. Zonsezi zinali zinthu zimene omvera ake ankaziona nthawi zambiri. Mfundo zofunika kwambiri za choonadi zikafotokozedwa pogwiritsa ntchito zinthu zodziwika bwino, anthu amazimva mosavuta ndipo zimakhazikika mumtima mwawo.​—Mateyu 11:16-19; 13:3-8, 33, 47-50; 18:12-14.

      11 Nthawi zambiri Yesu ankafotokozanso mafanizo a nkhani zongoyerekezera pofuna kuphunzitsa mfundo za makhalidwe abwino komanso za choonadi. Popeza nkhanizi sizivuta kuzimvetsa ndiponso kuzikumbukira, njira imeneyi inkathandiza anthu kuti azikumbukirabe mfundo zofunika zimene Yesu anawaphunzitsa. Munkhani zambiri zoterezi, Yesu ankapereka chithunzi chooneka bwino chokhudza mmene Atate ake alili ndipo zimenezi zinkathandiza anthu kumakumbukirabe mfundo zokhudza Yehova zomwe aphunzira. Mwachitsanzo, ndani sangamvetse mfundo ya m’fanizo la mwana wolowerera, yakuti munthu amene wasiya choonadi akalapa kuchokera pansi pa mtima, Yehova amamuchitira chifundo n’kumulandiranso mwachikondi?​—Luka 15:11-32.

      12. (a) Kodi Yesu ankagwiritsa ntchito bwanji mafunso pophunzitsa? (b) Kodi Yesu anafunsa funso liti lomwe linachititsa kuti anthu amene ankakayikira zoti iye ali ndi ulamuliro asowe chonena?

      12 Ankagwiritsa ntchito mafunso mwaluso. Yesu ankagwiritsa ntchito mafunso kuti omvera ake apeze okha yankho, adzifufuze komanso asankhe zochita. (Mateyu 12:24-30; 17:24-27; 22:41-46) Mwachitsanzo, atsogoleri achipembedzo atakayikira ngati Yesu anapatsidwadi ulamuliro ndi Mulungu, iye anayankha kuti: “Kodi ubatizo umene Yohane ankachita unali wochokera kumwamba kapena kwa anthu?” Iwo anadabwa kwambiri ndi funsoli moti anayamba kuuzana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ Koma tinganene kuti ‘Unachokera kwa anthu’ ngati? Iwo ankaopa gulu la anthu, chifukwa anthu onsewo ankakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri. Choncho iwo anayankha Yesu kuti: ‘Sitikudziwa.’” (Maliko 11:27-33; Mateyu 21:23-27) Pogwiritsa ntchito funso limodzi lokha losavuta, Yesu anawasowetsa chonena ndipo zinadziwika kuti anali anthu achinyengo.

      13-15. Kodi fanizo la Msamariya wachifundo limasonyeza bwanji kuti Yesu ndi wanzeru?

      13 Nthawi zina Yesu ankaphatikiza njira ziwiri pophunzitsa. Akafotokoza nkhani yongoyerekezera, kenako ankafunsa mafunso. Mwachitsanzo, Myuda wina wodziwa Chilamulo anafunsa Yesu chimene chimafunika kuti munthu adzapeze moyo wosatha. Yesu anamuuza za Chilamulo cha Mose chomwe chimanena za kukonda Mulungu komanso anthu anzathu. Pofuna kudzionetsa kuti ndi wolungama, munthuyo anafunsa kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndi ndani kwenikweni?” Poyankha, Yesu anafotokoza nkhani yongoyerekezera. Myuda wina ankayenda yekhayekha ndipo anakumana ndi achifwamba omwe anamuvulaza n’kumusiya atatsala pang’ono kufa. Panafika Ayuda awiri, poyamba wansembe kenako Mlevi. Koma onsewo sanamuthandize. Kenako panafika Msamariya. Chifukwa cha chifundo, iye anamanga mabala a wovulalayo ndipo anapita naye kunyumba ya alendo kumene akanatha kuchira. Pomaliza, Yesu anafunsa munthuyo kuti: “Ndi ndani pa anthu atatuwa amene iweyo ukuona kuti anakonda munthu amene anakumana ndi achifwambayu?” Munthuyo anakakamizika kuyankha kuti: “Ndi amene anamuchitira chifundoyo.”​—Luka 10:25-37.

      14 Kodi nkhaniyi ikusonyeza bwanji kuti Yesu ndi wanzeru? Munthawi ya Yesu, Ayuda ankanena kuti ‘mnzawo’ ndi munthu yekhayo amene ankasunga miyambo yawo ndipo n’zodziwikiratu kuti ankaona kuti Asamariya si anzawo. (Yohane 4:9) Ngati pofotokoza nkhaniyi Yesu akananena kuti Msamariya ndi amene anavulala ndipo Myuda ndi yemwe anamuthandiza, kodi akanathandiza munthuyo kuti achotse maganizo a tsankhowo? Mwanzeru, Yesu anafotokoza nkhaniyi m’njira yakuti Msamariya ndi yemwe anasamalira Myuda mwachikondi. Taonaninso funso limene Yesu anafunsa kumapeto kwa nkhaniyo pofuna kuthandiza munthu uja kumvetsa zimene kukonda mnzathu kumatanthauza. Tingati munthuyo anafunsa kuti: ‘Kodi ndi ndani amene ndiyenera kumusonyeza chikondi monga mnzanga?’ Koma Yesu anamufunsa kuti: ‘Ndi ndani pa anthu atatuwa amene iweyo ukuona kuti anakonda munthuyo?’ Mfundo ya Yesu sinali pa munthu amene anasonyezedwa chifundo, koma amene anasonyeza chifundo, yemwe ndi Msamariya uja. Mnzathu weniweni amayamba ndi iyeyo kusonyeza chikondi kwa ena mosatengera kuti ndi a mtundu uti. Apatu Yesu anaphunzitsa mwanzeru kwambiri.

      15 M’pake kuti anthu anadabwa ndi “kaphunzitsidwe” ka Yesu ndipo ankakopeka naye. (Mateyu 7:28, 29) Moti pa nthawi ina, “gulu la anthu” linakhala naye limodzi kwa masiku atatu ndipo mwina anthuwo sankachoka kuti akadye.​—Maliko 8:1, 2.

      Zimene Ankachita

      16. Kodi Yesu ‘anasonyeza’ bwanji kuti ankatsogoleredwa ndi nzeru za Mulungu?

      16 Njira yachitatu imene Yesu anasonyezera nzeru za Yehova ndi zimene ankachita pa moyo wake. Munthu akachita zinthu mwanzeru zotsatira zake zimakhala zabwino. Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anafunsa kuti: “Kodi pakati panu pali aliyense wanzeru ndi womvetsa zinthu?” Kenako anati: “Ngati alipo asonyeze zimenezi pochita zinthu zabwino pa moyo wake.” (Yakobo 3:13) Zimene Yesu ankachita ‘zinkasonyeza’ kuti ankatsogoleredwa ndi nzeru za Mulungu. Tiyeni tione mmene anasonyezera kuti anali munthu woganiza bwino pa zimene ankachita pa moyo wake komanso mmene ankachitira zinthu ndi ena.

      17. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yesu sankachita zinthu mopitirira malire?

      17 Kodi munaona kuti anthu osaganiza bwino nthawi zambiri amachita zinthu mopitirira malire? Pamafunika nzeru kuti munthu asamachite zimenezi. Popeza Yesu ankasonyeza nzeru za Mulungu, nthawi zonse ankachita zinthu moganiza bwino. Iye ankaika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba. Ankatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino. Iye anati: “Ndinabwera kudzachita zimenezi.” (Maliko 1:38) Sankaona kuti kukhala ndi katundu n’kofunika kwambiri ndipo zikuoneka kuti analibe zinthu zambiri. (Mateyu 8:20) Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti sankasangalala ndi zinthu zabwino. Mofanana ndi Atate ake, omwe ndi “Mulungu wachimwemwe,” Yesu ankasangalala ndipo ankathandizanso anthu ena kuti azisangalala. (1 Timoteyo 1:11; 6:15) Pamene anapezeka paphwando laukwati, pomwe nthawi zambiri pamakhala nyimbo, kuimba ndiponso kusangalala, sanapezekepo kuti asokoneze mwambowo. Vinyo atatha, iye anasandutsa madzi kukhala vinyo wokoma, chakumwa ‘chimene chimasangalatsa mtima wa munthu.’ (Salimo 104:15; Yohane 2:1-11) Komanso Yesu ankapita kunyumba za anthu ambiri akamuitanira chakudya ndipo nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito mpata umenewu pophunzitsa anthu.​—Luka 10:38-42; 14:1-6.

      18. Kodi Yesu anasonyeza bwanji nzeru pochita zinthu ndi ophunzira ake?

      18 Yesu anasonyezanso nzeru pochita zinthu ndi anthu. Popeza ankadziwa bwino anthu, ankatha kuwamvetsa ophunzira ake. Ankadziwa kuti ophunzira akewo sanali angwiro. Koma ankadziwanso makhalidwe awo abwino. Ankaona kuti anthu amenewa, omwe Yehova anali atawakoka, angathe kuchita zambiri. (Yohane 6:44) Ngakhale kuti iwo ankalakwitsa zinthu zina, Yesu ankawakhulupirira. Posonyeza kuti ankawakhulupirira, anawapatsa udindo waukulu kwambiri. Anawapatsa ntchito yolalikira uthenga wabwino ndipo ankakhulupirira kuti aikwanitsa. (Mateyu 28:19, 20) Buku la Machitidwe limasonyeza kuti ophunzirawo anagwira mokhulupirika ntchito yomwe anawapatsayo. (Machitidwe 2:41, 42; 4:33; 5:27-32) Choncho n’zodziwikiratu kuti Yesu anasonyeza nzeru powakhulupirira.

      19. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali “wofatsa ndi wodzichepetsa”?

      19 Monga taonera m’Mutu 20, Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa kudzichepetsa, kufatsa ndi nzeru. N’zoona kuti chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi ndi Yehova. Nanga bwanji Yesu? N’zosangalatsa kuona mmene Yesu ankachitira zinthu modzichepetsa ndi ophunzira ake. Popeza anali wangwiro, ankawaposa. Komabe sankadziona kuti ndi wapamwamba kuposa iwowo. Sanawachititsepo kudziona kuti ndi otsika kapena olephera. M’malomwake, ankadziwa kuti panali zinthu zina zomwe sakanakwanitsa kuchita ndipo ankawalezera mtima pa zimene ankalakwitsa. (Maliko 14:34-38; Yohane 16:12) Kodi si zochititsa chidwi kuti ngakhale ana ankamasuka ndi Yesu? Zoonadi, iwo ankasangalala kukhala naye pafupi chifukwa ankaona kuti anali “wofatsa ndi wodzichepetsa.”​—Mateyu 11:29; Maliko 10:13-16.

      20. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kulolera pamene ankachita zinthu ndi mayi yemwe sanali Myuda, amene mwana wake anagwidwa ndi chiwanda?

      20 Yesu anasonyeza kuti amatsanzira Yehova pa nkhani yodzichepetsa m’njira inanso yofunika kwambiri. Iye anali wololera ndipo ankasonyeza chifundo pakakhala zifukwa zabwino zochitira zimenezo. Mwachitsanzo, kumbukirani nthawi imene mayi wina yemwe sanali Myuda anamupempha kuti amuchiritsire mwana wake wamkazi yemwe anagwidwa ndi chiwanda. Katatu konse, Yesu anasonyeza kuti sankafuna kumuthandiza. Koyamba sanamuyankhe mayiyo, kachiwiri, anamuuza mwachindunji kuti sanatumidwe kwa anthu amene sanali Ayuda koma kwa Ayuda, ndipo kachitatu, anafotokoza fanizo limene mokoma mtima linafotokoza chifukwa chake sakanamuthandiza. Koma mayiyo anali ndi chikhulupiriro cholimba moti anapitiriza kupempha Yesu kuti amuthandize. Ndiye kodi Yesu anatani? Anachita zomwezo zimene anati sangachite. Anachiritsa mwana wa mayiyo. (Mateyu 15:21-28) Apatu Yesu anasonyeza kuti anali wodzichepetsa kwambiri. Ndipo kumbukirani kuti munthu wanzeru amakhalanso wodzichepetsa.

      21. N’chifukwa chiyani tiyenera kumayesetsa kuti tizitsanzira zimene Yesu ankachita komanso kulankhula?

      21 Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa mabuku a Uthenga Wabwino amatiuza zambiri zokhudza zimene Yesu, yemwe ndi munthu wanzeru kwambiri pa anthu onse amene anakhalako padzikoli, anachita ndiponso kulankhula. Tizikumbukira kuti Yesu ankasonyeza bwino mmene Atate ake alili. Tikamatsanzira zimene ankachita komanso kulankhula, tidzakhala tikusonyeza nzeru zochokera kumwamba. M’mutu wotsatira, tiona mmene tingagwiritsire ntchito nzeru za Mulungu pa moyo wathu.

      a Kale, makalipentala ankamanga nyumba, kupanga zinthu zamatabwa ndiponso kupanga zipangizo zaulimi. Justin Martyr, wa zaka za m’ma 100 C.E., analemba zokhudza Yesu kuti: “Ali padzikoli ankagwira ntchito ya ukalipentala ndipo ankapanga mapulawo ndi magoli.”

      b Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “kudera nkhawa,” amatanthauza “kusokonezedwa maganizo.” Mawu a pa Mateyu 6:25 amenewa, amanena za kuda nkhawa chifukwa choopa chinachake zomwe zimachititsa kuti munthu asokonezeke maganizo komanso asamasangalale.

      c Ndipotu, asayansi anapeza kuti kuda nkhawa kwambiri kungachititse kuti tikhale pa ngozi yodwala matenda a mtima ndi matenda enanso ambiri amene angachititse kuti tife msanga.

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Miyambo 8:22-31 Kodi zimene zikufotokozedwa pamavesiwa zokhudza nzeru zikugwirizana bwanji ndi zimene Baibulo limanena zokhudza Mwana woyamba kubadwa wa Yehova?

      • Mateyu 13:10-15 Kodi chimodzi mwa zifukwa zimene zinkachititsa Yesu kugwiritsa ntchito mafanizo chinali chiyani?

      • Yohane 1:9-18 N’chifukwa chiyani Yesu ankatha kuthandiza anthu kuti adziwe nzeru za Mulungu?

      • Yohane 13:2-5, 12-17 Kodi Yesu anachita chiyani kuti athandize atumwi kuona zimene ayenera kuchitirana?

  • Kodi Mumagwiritsa Ntchito “Nzeru Yochokera Kumwamba” pa Moyo Wanu?
    Yandikirani Yehova
    • Mlongo akuphunzira Baibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo.

      MUTU 22

      Kodi Mumagwiritsa Ntchito “Nzeru Yochokera Kumwamba”?

      1-3. (a) Kodi Solomo anasonyeza bwanji nzeru zapadera pamene anathetsa mkangano wolimbirana mwana? (b) Kodi Yehova amalonjeza kuti azitipatsa chiyani, nanga zimenezi zingachititse kuti pakhale mafunso ati?

      UNALI mlandu wovuta kwambiri, azimayi awiri ankalimbirana mwana. Azimayiwa ankakhala m’nyumba imodzi ndipo onse anabereka ana aamuna m’masiku oyandikana. Kenako mwana mmodzi anapezeka kuti wafa. Ndiyeno azimayiwo anayamba kulimbirana mwana wamoyoyo.a Panalibe aliyense woti aperekere umboni wa zimene zinachitikazi. N’kutheka kuti nkhaniyi inapita kukhoti laling’ono koma analephera kuithetsa. Pamapeto pake anapita nayo kwa Solomo, mfumu ya Isiraeli. Kodi iye akanakwanitsa kudziwa mayi wake weniweni wa mwanayo?

      2 Atamvetsera kwa kanthawi azimayiwo akukangana, Solomo anaitanitsa lupanga. Kenako analamula kuti mwanayo amudule pakati ndipo mayi aliyense amupatse mbali imodzi. Ndipo zinkaoneka ngati watsimikizadi kuti mwanayo adulidwe pakati. Nthawi yomweyo mayi wake weniweni anachonderera mfumuyo kuti mwana wake wokondedwayo aperekedwe kwa mnzakeyo. Koma mayi winayo ankaumirira kuti mwanayo amudule basi. Apa Solomo anadziwa zoona zake. Iye ankadziwa kuti mayi amakonda kwambiri mwana wobereka yekha ndipo anagwiritsa ntchito zimenezi pothetsa mkanganowo. Taganizirani mmene mayi wake wa mwanayu anasangalalira Solomo atamupatsa mwanayo n’kunena kuti: “Mayi ake ndi amenewa.”​—1 Mafumu 3:16-27.

      3 Zimenezitu zinali nzeru zapadera. Anthu atamva mmene Solomo anaweruzira mlanduwo, anagoma kwambiri “chifukwa anaona kuti Mulungu wamupatsa nzeru.” Zoonadi, nzeru za Solomo zinali zochokera kwa Mulungu. Yehova anamupatsa “mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu.” (1 Mafumu 3:12, 28) Koma bwanji ifeyo? Kodi ifenso Mulungu angatipatse nzeru? Inde, chifukwa mouziridwa ndi Mulungu, Solomo analemba kuti: “Yehova ndi amene amapereka nzeru.” (Miyambo 2:6) Yehova amalonjeza kuti azipereka nzeru, lomwe ndi luso lotha kugwiritsa ntchito zimene ukudziwa, kwa anthu onse omwe amafunitsitsa kukhala nazo. Ndiye kodi tingatani kuti tikhale ndi nzeru zochokera kumwamba? Ndipo kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito nzeru zimenezi pa moyo wathu?

      Kodi Tingatani Kuti ‘Tipeze Nzeru’?

      4-7. Tchulani zinthu 4 zofunika kuti munthu akhale wanzeru.

      4 Kodi tiyenera kukhala anzeru mwachibadwa kapena ophunzira kwambiri kuti tipeze nzeru za Mulungu? Ayi. Yehova ndi wokonzeka kutipatsa nzeru zake posatengera maphunziro athu kapenanso kuti ndife ndani. (1 Akorinto 1:26-29) Koma timafunika kuchita mbali yathu, chifukwa Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tipeze nzeru.’ (Miyambo 4:7) Kodi tingachite bwanji zimenezi?

      5 Choyamba, tiyenera kumaopa Mulungu. Lemba la Miyambo 9:10 limati: “Kuopa Yehova ndi chiyambi cha nzeru.” Choncho kuti tikhale ndi nzeru zenizeni tiyenera kumaopa Mulungu. N’chifukwa chiyani zili choncho? Kumbukirani kuti nzeru zimatanthauza kudziwa mfundo zokhudza nkhani inayake, kuonetsetsa kuti tazimvetsa kenako n’kuzigwiritsa ntchito moyenera. Kuopa Mulungu sikutanthauza kunjenjemera chifukwa chochita naye mantha, koma kumatanthauza kumumvera chifukwa chomulemekeza kwambiri. Kuchita zimenezi n’kwabwino ndipo kumatithandiza kuti tizichita zoyenera komanso zogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna kuti tizichita. Palibe chinthu chanzeru kwambiri chimene tingachite kuposa zimenezi chifukwa anthu amene amatsatira mfundo za Yehova zinthu zimawayendera bwino kwambiri nthawi zonse.

      6 Chachiwiri, tiyenera kukhala odzichepetsa. Munthu sangakhale ndi nzeru za Mulungu ngati si wodzichepetsa. (Miyambo 11:2) N’chifukwa chiyani zili choncho? Tikakhala odzichepetsa, timavomereza kuti sitidziwa zonse, si nthawi zonse pamene maganizo athu amakhala olondola ndiponso kuti timafunika kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana. Yehova “amatsutsa odzikuza” koma amasangalala kupereka nzeru kwa anthu odzichepetsa.​—Yakobo 4:6.

      7 Chachitatu, tiyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu. Timadziwa nzeru za Yehova tikamawerenga Mawu ake. Kuti tipeze nzeruzi, tiyenera kumazifunafuna mwakhama. (Miyambo 2:1-5) Chinthu cha 4 ndi pemphero. Tikamapempha nzeru za Mulungu mochokera pansi pa mtima, iye adzatipatsa mosaumira. (Yakobo 1:5) Adzatithandizanso pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera ngati titamupempha. Ndipo mzimu wake ungatithandize kupeza malangizo anzeru m’Mawu ake. Malangizowa angatithandize kulimbana ndi mavuto, kupewa zinthu zoopsa ndiponso kusankha zochita mwanzeru.​—Luka 11:13.

      Kuti tipeze nzeru za Mulungu, tiyenera kuzifufuza mwakhama

      8. Ngati tilidi ndi nzeru zochokera kwa Mulungu, kodi zotsatira zake zingakhale zotani?

      8 Monga tinaonera m’Mutu 17, nzeru za Yehova n’zothandiza. Choncho ngati tilidi ndi nzeru zochokera kwa Mulungu, zimene timachita zimasonyeza zimenezi. Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anafotokoza zimene zimachitika munthu akakhala ndi nzeru za Mulungu. Anati: “Nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, ndiponso yopanda chinyengo.” (Yakobo 3:17) Tikamakambirana mbali iliyonse yokhudza nzeru za Mulunguzi, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndimagwiritsa ntchito nzeru yochokera kumwamba pa moyo wanga?’

      “Yoyera, Kenako Yamtendere”

      9. Kodi kukhala woyera kumatanthauza chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani n’zomveka kuti choyamba tiyenera kukhala oyera kuti tithe kusonyeza nzeru ya Mulungu?

      9 “Choyamba, ndi yoyera.” Kukhala woyera kumatanthauza kukhala wosadetsedwa, kunja ndi mkati momwe. Baibulo limati nzeru zimalowa mumtima. Komatu nzeru yochokera kumwamba singalowe mumtima umene wadetsedwa ndi maganizo olakwika, zilakolako zoipa komanso zolinga zosayenera. (Miyambo 2:10; Mateyu 15:19, 20) Koma tikamayesetsa kuti mtima wathu ukhale woyera, ‘timapewa kuchita zoipa ndipo timachita zabwino.’ (Salimo 37:27; Miyambo 3:7) M’pake kuti Baibulo limati choyamba tiyenera kukhala oyera kuti tikwanitse kusonyeza makhalidwe ena amene munthu amakhala nawo ngati ali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu.

      10, 11. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kumakhala mwamtendere ndi ena? (b) Ngati mwazindikira kuti mwakhumudwitsa Mkhristu mnzanu, kodi mungatani kuti mukhazikitse mtendere? (Onaninso mawu a m’munsi.)

      10 “Kenako yamtendere.” Nzeru yochokera kumwamba imatithandiza kuti tiziyesetsa kukhala mwamtendere. Khalidweli timakhala nalo mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22) Timayesetsa kuti tisasokoneze ‘mtendere umene uli ngati chomangira chimene chimagwirizanitsa’ anthu a Yehova. (Aefeso 4:3) Timayesetsanso kubwezeretsa mtendere ukasokonekera. N’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika? Baibulo limati: “Pitirizani . . . kukhala mwamtendere. Mukatero, Mulungu amene ndi wachikondi komanso wamtendere adzakhala nanu.” (2 Akorinto 13:11) Choncho tikamapitiriza kukhala mwamtendere, Mulungu wamtendere adzakhala nafe. Mmene timachitira zinthu ndi Akhristu anzathu zimakhudza ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndiye kodi tingakhazikitse bwanji mtendere? Taganizirani chitsanzo ichi.

      11 Kodi mungatani ngati mwazindikira kuti mwakhumudwitsa Mkhristu mnzanu? Yesu anati: “Ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo n’kuchokapo. Choyamba pita ukakhazikitse mtendere ndi m’bale wakoyo. Kenako ukabwerenso n’kudzapereka mphatso yakoyo.” (Mateyu 5:23, 24) Muziyamba ndi inuyo kupita kukakambirana ndi m’bale wanuyo ndipo mukamatero mumasonyeza kuti mukutsatira malangizo amenewa. Kodi cholinga chanu chiyenera kukhala chiyani? ‘Kukakhazikitsa mtendere.’b Kuti zimenezi zitheke mungafunike kuvomereza, osati kukana, kuti nkhaniyo yamukhumudwitsa mnzanuyo. Ngati pa nthawi yonse imene mukulankhulana mutakhala ndi cholinga choti mubwezeretse mtendere, mukhoza kuthetsa kusamvana, kupepesana ndiponso kukhululukirana. Mukayesetsa kuti mukhazikitse mtendere, mumasonyeza kuti mukutsogoleredwa ndi nzeru za Mulungu.

      “Yololera, Yokonzeka Kumvera”

      12, 13. (a) Kodi mawu amene anawamasulira kuti “kulolera” pa Yakobo 3:17, amatanthauza chiyani? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ololera?

      12 “Yololera.” Kodi kulolera kumatanthauza chiyani? Akatswiri ena a Baibulo amati mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “yololera” pa Yakobo 3:17 ndi ovuta kuwamasulira. Omasulira ena anamasulira mawuwa kuti “yodekha,” “yoleza mtima” ndi “yokoma mtima.” Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ololera?

      13 Lemba la Afilipi 4:5 limati: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” Baibulo lina limati: “Mukhale ndi mbiri yoti ndinu wololera.” (The New Testament in Modern English, lomasuliridwa ndi J. B. Phillips) Onani kuti nkhani si mmene timadzionera koma mmene ena amationera, kuti timadziwika ndi mbiri yotani. Munthu wololera saumirira malamulo kapenanso kufuna kuti nthawi zonse zinthu zichitike mmene iye akufunira. Koma amakhala wokonzeka kumva maganizo a ena ndipo amachita zimene anthuwo akufuna ngati kuchita zimenezo kuli koyenera. Amakhala wodekha, osati waukali kapena wankhanza. Ngakhale kuti zimenezi n’zofunika kwa Akhristu onse, n’zofunika kwambiri makamaka kwa akulu. Anthu amakopeka ndi munthu wodekha, ndipo mkulu wodekha savuta kulankhula naye. (1 Atesalonika 2:7, 8) Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi anthu amandiona kuti ndine wokoma mtima, wololera komanso wodekha?’

      14. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ‘okonzeka kumvera’?

      14 “Yokonzeka kumvera.” Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “yokonzeka kumvera” amapezeka pamalo okhawa m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu. Katswiri wina ananena kuti mawu amenewa “nthawi zambiri amagwiritsidwa ntchito ponena za asilikali amene ndi ofunitsitsa kumvera malamulo ankhondo.” Amanena za “kukopeka mosavuta” ndiponso “kugonjera.” Munthu amene akutsogoleredwa ndi nzeru yochokera kumwamba amagonjera mosavuta zimene Malemba amanena. Sadziwika kuti ndi munthu womva zake zokha yemwe safuna kumva mfundo zotsutsana ndi zake. Koma amasintha mofulumira akapatsidwa umboni womveka bwino wochokera m’Malemba woti akuchita zolakwika kapena sanasankhe bwino. Kodi inuyo mumadziwika kuti ndinu munthu wotero?

      “Yodzaza ndi Chifundo ndi Zipatso Zabwino”

      15. Kodi chifundo n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani chatchulidwa limodzi ndi “zipatso zabwino” pa Yakobo 3:17?

      15 “Yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino.”c Chifundo ndi mbali yofunika kwambiri ya nzeru yochokera kumwamba, chifukwa nzeruyi imatchulidwa kuti ndi “yodzaza ndi chifundo.” Onani kuti “chifundo” chatchulidwa limodzi ndi “zipatso zabwino.” Zimenezi n’zoyenera, chifukwa m’Baibulo mawu akuti chifundo nthawi zambiri amanena za kudera nkhawa munthu kapena kumumvera chisoni n’kumuchitira zinthu zabwino. Buku lina linanena kuti chifundo ndi “kumvera chisoni munthu amene zoipa zamuchitikira kenako n’kuyesetsa kumuthandiza.” Choncho munthu amene ali ndi nzeru yochokera kumwamba sikuti amangodziwa zimene anthu ena akumana nazo, koma amakhala wokoma mtima komanso woganizira ena. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odzaza ndi chifundo?

      16, 17. (a) Kuwonjezera pa kukonda Mulungu, n’chiyaninso chimatichititsa kuti tizigwira nawo ntchito yolalikira? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odzadza ndi chifundo?

      16 Njira yofunika kwambiri ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. N’chifukwa chiyani timagwira ntchitoyi? Chifukwa chachikulu n’chakuti timakonda Mulungu. Koma timagwiranso ntchitoyi chifukwa choti timachitira ena chifundo. (Mateyu 22:37-39) Masiku ano anthu ambiri ndi “onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” (Mateyu 9:36) Atsogoleri awo achipembedzo samawasamalira komanso amawasocheretsa. Zotsatira zake n’zakuti anthuwa sadziwa malangizo anzeru omwe amapezeka m’Mawu a Mulungu ndiponso madalitso amene Ufumu wa Mulungu ubweretse padzikoli posachedwa. Choncho tikamaganizira kuti anthu akufunika kumva uthenga wabwino, timawamvera chisoni ndipo timafuna kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tiwauze uthengawu.

      Mwamuna ndi mkazi wake komanso ana awo awiri abweretsa zakudya ndi zipangizo kuti athandize mlongo wachikulire.

      Tikamachitira ena chifundo, timasonyeza kuti tili ndi “nzeru yochokera kumwamba”

      17 Kodi tingasonyeze kuti ndife odzadza ndi chifundo m’njira zinanso ziti? Kumbukirani fanizo la Yesu la Msamariya amene anapeza munthu atagona m’mbali mwa msewu, atamubera ndiponso kumumenya. Msamariyayo anamva chisoni ndipo ‘anamuchitira chifundo’ n’kumumanga mabala ake ndiponso kumusamalira. (Luka 10:29-37) Zimenezitu zikusonyeza kuti munthu wachifundo amathandiza anthu amene akuvutika. Baibulo limatiuza kuti ‘tizichitira onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10) Taonani zina zimene tingachite pa nkhaniyi. Mkhristu wachikulire angafunike kumuthandiza kuti apite kumisonkhano yampingo. Mlongo wamasiye mumpingo angafunike kumuthandiza kukonza nyumba yake. (Yakobo 1:27) Munthu amene ali ndi nkhawa angafunike kumuuza “mawu abwino” omwe angamulimbikitse. (Miyambo 12:25) Tikamasonyeza chifundo m’njira ngati zimenezi, ndi umboni wakuti nzeru yochokera kumwamba ikutitsogolera.

      “Yopanda Tsankho, Ndiponso Yopanda Chinyengo”

      18. Ngati tikutsogoleredwa ndi nzeru yochokera kumwamba, kodi tiyenera kuyesetsa kuchotsa chiyani mumtima mwathu ndipo n’chifukwa chiyani?

      18 “Yopanda tsankho.” Nzeru yochokera kumwamba imatithandiza kuti tisamaganize kuti ndife apamwamba kusiyana ndi anthu amitundu ina kapena a m’mayiko ena. Tikamatsogoleredwa ndi nzeru imeneyi, timayesetsa kuchotsa tsankho mumtima mwathu. (Yakobo 2:9) Tikamachitira ena zabwino, sititengera kuti ndi ophunzira, opeza bwino kapena ali ndi udindo mumpingo. Ndiponso timaona kuti Mkhristu aliyense ndi wofunika ngakhale amene amaoneka ngati wonyozeka. Ngati Yehova amakonda anthu amenewa, ndiye kuti nafenso tiyenera kuwakonda.

      19, 20. (a) Kodi mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “wachinyengo,” anayambira pati? (b) Kodi timasonyeza bwanji kuti ‘timakonda abale mopanda chinyengo,’ ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

      19 “Yopanda Chinyengo.” Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “wachinyengo,” anganene za “munthu amene wachita nawo sewero pabwalo la masewera.” Kale, Agiriki ndi Aroma akamachita masewero ankavala zinthu zobisa nkhope. Choncho mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “wachinyengo,” anayamba kuwagwiritsa ntchito ponena za munthu amene ankachita zinthu mwachinyengo kapena amene ankapusitsa anthu. Mbali imeneyi ya nzeru yochokera kumwamba, imakhudza mmene timachitira zinthu ndi Akhristu anzathu komanso mmene timawaonera mumtima mwathu.

      20 Mtumwi Petulo ananena kuti popeza ‘timamvera choonadi,’ tiyenera ‘kumakonda abale mopanda chinyengo.’ (1 Petulo 1:22) Zoonadi, sitiyenera kukonda abale ndi alongo athu n’cholinga chongofuna kudzionetsera kapena kuoneka ngati abwino. Chikondi chathu chiyenera kukhala chenicheni komanso chochokera pansi pa mtima. Tikamachita zimenezi, abale ndi alongo athu azitikhulupirira chifukwa adzadziwa kuti si ife achinyengo. Zimenezi zingathandize kuti tizigwirizana kwambiri ndiponso kuti anthu mumpingo azidalirana.

      “Uteteze Nzeru Zopindulitsa”

      21, 22. (a) Kodi Solomo analephera bwanji kuteteza nzeru? (b) Kodi tingateteze bwanji nzeru, nanga kuchita zimenezi kungatithandize bwanji?

      21 Nzeru yochokera kumwamba ndi mphatso imene Yehova amatipatsa, choncho tiyenera kuiteteza. Solomo anati: “Mwana wanga, . . . uteteze nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.” (Miyambo 3:21) Koma n’zomvetsa chisoni kuti Solomoyo analephera kuchita zimenezi. Anali wanzeru pa nthawi yonse imene ankamvera Mulungu. Koma patapita nthawi, akazi ake ambirimbiri achilendo anamuchititsa kuti asamalambire Yehova movomerezeka. (1 Mafumu 11:1-8) Zimene zinachitikira Solomo zimatiphunzitsa kuti zinthu zimene timadziwa sizingatithandize ngati sitingazigwiritse ntchito bwino.

      22 Kodi tingateteze bwanji nzeru zopindulitsa? Kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo nthawi zonse ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo omwe “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” amapereka, tiyenera kuyesetsa kumagwiritsa ntchito zimene timaphunzira. (Mateyu 24:45). Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kugwiritsira ntchito nzeru za Mulungu pa moyo wathu. Nzeruzi zimatithandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino panopa. Zimatithandizanso kuti ‘tigwire mwamphamvu moyo weniweniwo’ womwe tidzakhale nawo m’dziko latsopano. (1 Timoteyo 6:19) Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti kukhala ndi nzeru yochokera kumwamba kumatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu, yemwe ndi Mwiniwake wa nzeru zonse.

      a Mogwirizana ndi 1 Mafumu 3:16, azimayi awiriwo anali mahule. Buku la Insight on the Scriptures limati: “N’kutheka kuti azimayiwa sanali oyendayenda, koma anali mahule m’njira yakuti ankachita zachiwerewere. Mwina anali Ayuda kapenanso sanali Ayuda.”​—Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

      b Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “ukakhazikitse mtendere,” amatanthauza “kusiya kukhala adani n’kukhala mabwenzi, kugwirizananso ndiponso kuyambiranso kuchitira zinthu limodzi.” Choncho cholinga chanu n’kuthandiza m’bale wanu amene wakhumudwayo kuti ngati zingatheke asiye kukhumudwa nanu.​—Aroma 12:18.

      c Baibulo lina linamasulira mawu amenewa kuti “yodzaza ndi chifundo ndi ntchito zabwino.”​—A Translation in the Language of the People, lomasuliridwa ndi Charles B. Williams.

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Deuteronomo 4:4-6 Kodi timasonyeza bwanji kuti ndife anzeru?

      • Salimo 119:97-105 Kodi kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu ndiponso kugwiritsa ntchito zomwe tikuphunzirazo kungatithandize bwanji?

      • Miyambo 4:10-13, 20-27 N’chifukwa chiyani timafunikira nzeru za Yehova?

      • Yakobo 3:1-16 Kodi anthu amene ali udindo woyang’anira mumpingo angasonyeze bwanji kuti ndi anzeru ndiponso omvetsa zinthu?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena